Genesis 31:1-55
31 Patapita nthawi, Yakobo anamva zimene ana aamuna a Labani anali kunena, kuti: “Yakobo watenga chilichonse cha bambo athu, ndipo chuma chonse chimene wasonkhanitsachi chachokera kwa bambo athu.”+
2 Tsopano Yakobo anaona kuti Labani sanali kumuyang’ana ndi diso labwino ngati poyamba.+
3 Potsirizira pake Yehova anauza Yakobo kuti: “Tsopano bwerera kudziko la makolo ako ndi kwa abale ako,+ ndipo ine ndidzakhalabe nawe.”+
4 Ndiyeno Yakobo anaitanitsa Rakele ndi Leya, kuti abwere kubusa kumene iye anali ndi nkhosa zake.
5 Iye anawauza kuti:
“Ndikuona kuti bambo anu sakundiyang’ana ndi diso labwino ngati poyamba,+ koma Mulungu wa bambo anga sanandisiye.+
6 Inunso mukudziwa ndithu, kuti ndagwirira ntchito bambo anu ndi mphamvu zanga zonse.+
7 Koma bambo anu akhala akundipusitsa, ndipo asintha malipiro anga maulendo 10. Ngakhale ndi choncho, Mulungu sanawalole kuti andichite choipa.+
8 Nthawi zonse Labani akanena kuti, ‘Zamawangamawanga ndizo zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinali kubereka zamawangamawanga. Akanena kuti, ‘Zamizeremizere ndizo zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinali kubereka zamizeremizere.+
9 Mulungu anali kuchotsa ziweto kwa bambo anu n’kuzipereka kwa ine.+
10 Pamene ziweto zinali m’nthawi yotentha thupi kukonzekera kutenga bere, ndinakweza maso anga n’kuona m’maloto+ mbuzi zamphongo zikukwera zazikazi. Mbuzi zamphongozo zinali zamizeremizere, zamawangamawanga ndi zamathothomathotho.+
11 Kenako, mngelo wa Mulungu woona anandiitana m’malotowo kuti, ‘Yakobo!’ Ine ndinayankha kuti, ‘Ine pano.’+
12 Iye anapitiriza kuti, ‘Kweza maso ako ndipo ona kuti mbuzi zonse zamphongo zimene zikukwerazi ndi zamizeremizere, zamawangamawanga ndiponso zamathothomathotho. Ndachita zimenezi chifukwa ndaona zonse zimene Labani akuchita kwa iwe.+
13 Ndine Mulungu woona wa ku Beteli+ uja, kumene unadzoza mwala+ kuja, kumenenso unachita lonjezo kwa ine.+ Tsopano nyamuka, uchoke kudziko lino, ubwerere kudziko limene unabadwira.’”+
14 Pamenepo Rakele ndi Leya anamuyankha kuti: “Kodi ifeyo tatsala ndi cholowa chilichonse m’nyumba ya bambo athu ngati?+
15 Kodi iwowa sakutiona ife ngati alendo? Bambowa anatigulitsa ndipo akupitiriza kudya ndalama zimene inu munatiperekera.+
16 Pakuti chuma chonse chimene Mulungu watenga kwa bambo athuwa, ndi chathu ndi cha ana athu.+ Ndiye chilichonse chimene Mulungu wakuuzani, chitani.”+
17 Ndiyeno Yakobo ananyamuka n’kukweza ana ake ndi akazi ake pangamila.+
18 Kenako, anayamba kukusa ziweto zake zonse, ndi kutenganso katundu wake yense amene anapeza+ ku Padana-ramu, n’kunyamuka ulendo wopita kudziko la Kanani kwa bambo ake Isaki.+
19 Pa nthawiyi n’kuti Labani atapita kukameta ubweya wa nkhosa zake. Akali kumeneko, Rakele anaba aterafi*+ a bambo ake.
20 Chotero Yakobo anachoka mozembera Labani Msiriya uja, chifukwa sanamuuze kuti akuchoka.
21 Yakobo anathawa n’kuwoloka Mtsinje*+ limodzi ndi zonse zimene anali nazo. Atatero, anayenda molunjika dera la kumapiri la Giliyadi.+
22 Pa tsiku lachitatu, Labani anamva kuti Yakobo wathawa.
23 Atamva zimenezo, iye anatenga abale ake n’kuyamba kuthamangira+ Yakobo. Iwo anayenda ulendo wa masiku 7, ndipo anamupeza m’dera la kumapiri la Giliyadi.
24 Koma usiku m’maloto,+ Mulungu anafikira Labani Msiriyayo+ n’kumuuza kuti: “Samala kuti usanene chilichonse chosokoneza zochita za Yakobo.”+
25 Kenako Labani anapita kwa Yakobo. Pa nthawiyi n’kuti Yakobo atamanga hema wake m’dera la kumapiri la Giliyadi, ndipo Labani ndi abale ake anamanganso hema wawo m’dera lomwelo.
26 Ndiyeno Labani anafunsa Yakobo kuti: “Ndiye chiyani wachitachi, kuchoka mondizembera, n’kutenga ana anga aakazi ngati akapolo ogwidwa kunkhondo?+
27 N’chifukwa chiyani wathawa mwamseri, kundizembera osandiuza? Bwenzi nditatsanzikana nawe mosangalala, nyimbo zikuimbidwa,+ ndiponso maseche ndi azeze akulira.+
28 Sunandipatse mpata woti ndipsompsone adzukulu anga ndi ana anga.+ Zimene wachitazi n’zopusa.
29 Ndikanatha kukuchitani choipa anthu inu,+ koma Mulungu wa bambo anu analankhula nane usiku wapitawu kuti, ‘Samala kuti usanene chilichonse chosokoneza zochita za Yakobo.’+
30 Ngati wachoka chifukwa cholakalaka kwambiri kunyumba kwa bambo ako, nanga n’chifukwa chiyani waba milungu yanga?”+
31 Poyankha, Yakobo anauza Labani kuti: “Ndinachoka chozemba chifukwa ndinachita mantha.+ Ndinaganiza kuti mungandilande ana anu.
32 Aliyense amene mum’peze ndi milungu yanu aphedwe.+ Pamaso pa abale athuwa, fufuzani milungu yanuyo pa katundu wathu. Mukaipeza muitenge.”+ Koma Yakobo sanadziwe kuti Rakele anali ataba milunguyo.+
33 Pamenepo Labani anakalowa muhema wa Yakobo, ndi muhema wa Leya, ndiponso muhema wa akapolo aakazi awiri aja,+ koma sanaipeze. Potsirizira pake, anatuluka muhema wa Leya n’kukalowa muhema wa Rakele.
34 Rakele anali atatenga aterafi aja n’kuwabisa m’chishalo choika pangamila, n’kuchikhalira. Labani anafunafuna muhema monsemo, koma sanawapeze aterafiwo.
35 Kenako Rakele anauza bambo ake kuti: “Musakwiye nane mbuyanga+ poti sindikutha kunyamuka pano. Kungoti sindili bwino malinga ndi chikhalidwe chathu akazife.”+ Labani anapitiriza kufunafuna mosamala, koma sanawapeze aterafiwo.+
36 Ndiyeno Yakobo anapsa mtima+ n’kuyamba kukangana ndi Labani n’kumufunsa kuti: “Kodi ndakupandukirani motani,+ ndakuchimwirani chiyani kuti muchite kundilondola mwaukali chonchi?+
37 Popeza tsopano mwafunafuna m’katundu wanga yense, kodi n’chiyani chimene mwapezapo pa katundu yense wa m’nyumba mwanu?+ Chiikeni apa pamaso pa abale anga ndi abale anu,+ kuti iwo atiweruze.+
38 Pa zaka 20 zonsezi zimene ndakhala nanu, nkhosa zanu zazikazi ndi mbuzi zanu zazikazi sizinaberekepo mwana wakufa.+ Ndiponso, chikhalire sindinadyeko ndi imodzi yomwe ya nkhosa zanu zamphongo.
39 Nyama yanu iliyonse imene inakhadzulidwa ndi chilombo sindinaibweretse kwa inu.+ Ndinali kuitenga kukhala yanga. Kaya ina ibedwe usana kapena usiku, munali kundiuza kuti ndikulipireni.+
40 Ndinkangokhalira kutenthedwa ndi dzuwa usana ndi kuzizidwa ndi mphepo usiku, ndipo tulo sindinkationa.+
41 Zonse pamodzi ndakhala zaka 20 m’nyumba mwanu. Ndakugwirirani ntchito zaka 14, kugwirira ana anu aakazi awiriwa. Zaka zinanso 6, ndagwirira ntchito ziweto. Koma inu munapitiriza kusinthasintha malipiro anga mpaka maulendo 10.+
42 Mulungu wa bambo anga,+ Mulungu wa Abulahamu, Mulungu amene Isaki anali kumuopa,+ akanapanda kukhala kumbali yanga, bwenzi mutandibweza kwathu chimanjamanja. Koma Mulungu waona kusautsika kwanga ndi ntchito zimene ndagwira molimbika, n’chifukwa chake anakudzudzulani usiku wapitawu.”+
43 Ndiyeno Labani anamuyankha Yakobo kuti: “Ana aakaziwa ndi ana anga, ana awo ndi ana anga, ziwetozi ndi ziweto zanga, ndipo chilichonse chimene ukuchiona ndi cha ine ndi ana anga aakaziwa. Kodi iwowa, kapena ana awo amene anabereka, ndingawachitire choipa lero chifukwa chiyani?
44 Tiye tichite pangano+ ine ndi iwe, kuti likhale mboni pakati pa ine ndi iwe.”+
45 Pamenepo Yakobo anatenga mwala n’kuuimika ngati mwala wachikumbutso.+
46 Kenako Yakobo anauza abale ake kuti: “Tengani miyala!” Iwo anatenga miyala n’kuiunjika mulu.+ Atatero, anadyera chakudya pamulu wa miyalapo.
47 Labani anatcha mulu wa miyalawo Yegara-sahaduta,* koma Yakobo anautcha Galeeda.*
48 Labani anapitiriza kulankhula kuti: “Mulu wa miyalawu ndi mboni yathu lero pakati pa ine ndi iwe.” N’chifukwa chake unatchedwa Galeeda,+
49 ndiponso kuti Nsanja ya Mlonda, chifukwa Labani anati: “Yehova aziyang’anira iwe ndi ine tikasiyana pano.+
50 Ukamakazunza ana angawa,+ ndipo ukakatenga akazi ena kuwonjezera pa ana anga, ngakhale palibe munthu pano, dziwa kuti Mulungu ndiye mboni pakati pa ine ndi iwe.”+
51 Labani anauzanso Yakobo kuti: “Ona mulu wa miyala ndiponso mwala wachikumbutso umene ndaimika monga chizindikiro cha pangano la pakati pa ine ndi iwe.
52 Muluwu ndiponso mwala wachikumbutsowu ndi mboni.+ Zikuchitira umboni kuti, pakati pa ine ndi iwe, wina sadzadutsa muluwu ndi mwala wachikumbutsowu kukachitira mnzake choipa.+
53 Atiweruze mulungu wa Abulahamu,+ mulungu wa Nahori,+ yemwe ali mulungu wa bambo awo.” Koma Yakobo analumbira pa Mulungu amene bambo ake Isaki anali kumuopa.+
54 Pambuyo pake, Yakobo anapereka nsembe m’phirimo n’kuitana abale ake kuti adye chakudya.+ Motero iwo anadya chakudya n’kugona m’phirimo usiku umenewo.
55 Ndiyeno Labani anadzuka m’mamawa n’kupsompsona+ adzukulu ake ndi ana ake aakazi ndipo anawadalitsa.+ Atatero, ananyamuka kubwerera kwawo.+
Mawu a M'munsi
^ “Aterafi” ndi milungu kapena mafano a banja.
^ Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
^ “Yegara-sahaduta” ndi dzina lachiaramu lotanthauza kuti “Mulu wa Umboni.”
^ “Galeeda” ndi dzina lachiheberi lotanthauza kuti “Mulu wa Umboni.”