Genesis 8:1-22

8  Pambuyo pake, Mulungu anakumbukira+ Nowa ndi nyama zonse zakutchire, ndiponso nyama zonse zoweta zimene anali nazo m’chingalawa.+ Ndiyeno Mulungu anachititsa chimphepo kuwomba padziko lapansi, ndipo madzi anayamba kuchepa.+  Pamenepo, akasupe a madzi akuya+ ndi zotsekera madzi+ akumwamba zinatsekeka, choncho madzi omwe anali kukhuthuka kuchokera kumwamba anasiya.  Komanso madzi anali kuchepa pang’onopang’ono padziko lapansi. Pakutha pa masiku 150, madziwo anali atachepa ndithu.+  M’mwezi wa 7,* pa tsiku la 17 la mweziwo, chingalawacho+ chinaima pamapiri a Ararati.+  Madzi anapitirizabe kuchepa mpaka mwezi wa 10. M’mwezi wa 10 umenewo, pa tsiku loyamba la mweziwo, nsonga za mapiri zinaonekera.+  Ndiyeno patatha masiku 40, Nowa anatsegula windo+ la chingalawa limene anaika.  Atatero, anatumiza khwangwala,+ koma iye anali kumangouluka kunjako, kupita ndi kubwera kufikira pamene madzi anaphwa padziko lapansi.  Kenako, Nowa anatumiza njiwa+ kuti aone ngati madzi anaphwa padziko lapansi.  Koma njiwayo sinapeze malo alionse oti n’kuterapo. Chotero, inabwerera kwa iye m’chingalawamo chifukwa madzi anali asanaphwe padziko lonse lapansi.+ Itabwerera, iye anatulutsa dzanja lake, n’kuitenga kuilowetsa m’chingalawamo. 10  Anapitirizabe kudikira masiku ena 7. Kenako, anatumizanso njiwa ija kuchokera m’chingalawamo. 11  Njiwayo inabwerera kwa iye nthawi yamadzulo. Inabwerako ndi tsamba laliwisi kukamwa kwake, longothyoledwa kumene pamtengo wa maolivi.+ Nowa ataona, anadziwa kuti madzi anali ataphwa padziko lapansi.+ 12  Anadikirabe masiku enanso 7. Kenako anaitumizanso njiwa ija, koma sinabwererenso kwa iye.+ 13  Tsopano m’chaka+ cha 601 cha Nowa, mwezi woyamba, pa tsiku loyamba la mweziwo, madzi anali ataphwa padziko lapansi. Ndipo Nowa anayang’ana kunja kudzera pachibowo chimene chinali padenga la chingalawacho. Atatero, anaona kuti madzi aphwa panthaka.+ 14  M’mwezi wachiwiri, pa tsiku la 27 la mweziwo, madzi anaphweratu padziko lapansi.+ 15  Ndiyeno Mulungu analankhula ndi Nowa, kuti: 16  “Tsopano tulukani m’chingalawamo, iweyo, mkazi wako, ana ako, ndi akazi a ana ako.+ 17  Utuluke limodzi ndi zamoyo zamtundu uliwonse+ zimene uli nazo: Zolengedwa zouluka,+ zinyama+ ndi zonse zokwawa padziko lapansi,+ kuti zibalalike padziko lapansi, ziswane ndi kuchulukana.”+ 18  Pamenepo, Nowa anatuluka limodzi ndi ana ake,+ mkazi wake, ndi akazi a ana ake. 19  Komanso, zamoyo zilizonse, nyama zilizonse, zolengedwa zouluka zilizonse, zokwawa zilizonse za padziko lapansi, monga mwa magulu awo, zinatuluka m’chingalawamo.+ 20  Tsopano Nowa anamangira Yehova guwa lansembe.+ Atatero, anatenga zina mwa nyama zonse zoyera,+ ndi zina mwa zouluka zonse zoyera,+ n’kuzipereka nsembe yopsereza paguwapo.+ 21  Ndiyeno Yehova anamva fungo lokhazika mtima pansi,+ moti ananena mumtima+ mwake kuti: “Sindidzatembereranso nthaka+ chifukwa cha zochita za anthu, popeza maganizo+ a anthu amakhala oipa kuyambira pa ubwana wawo.+ Ndipo sindidzawononganso chilichonse monga ndachitiramu.+ 22  Masiku onse amene dziko lapansi lidzakhalapo, kubzala mbewu ndi kukolola sikudzatha. Ndiponso, nyengo yozizira ndi yotentha, chilimwe ndi chisanu, usana ndi usiku, zidzakhalapobe.”+

Mawu a M'munsi

“Mwezi wa 7” umene ukutchulidwa m’vesili unali kuyenderana ndi mwezi wa Abibu pakalendala yopatulika ya Ayuda. Pakalendala ya Ayuda imeneyi, mwezi wa Abibu kapena kuti Nisani, unali mwezi woyamba.