Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi?
Kodi mungayankhe kuti . . .
-
inde?
-
ayi?
-
kapena mwina adzatha?
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
“Mulungu . . . adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4, Baibulo la Dziko Latsopano.
KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?
Zikutipatsa umboni wakuti si Mulungu amene amachititsa mavuto amene tikukumana nawo.—Yakobo 1:13.
Zikutithandiza kudziwa kuti Mulungu amamvetsa mmene tikumvera tikamavutika.—Zekariya 2:8.
Komanso zikutitsimikizira kuti mavuto onse adzatha.—Salimo 37:9-11.
KODI ZIMENE BAIBULO LIKUNENAZI TINGAZIKHULUPIRIREDI?
Inde, tingazikhulupirire pa zifukwa zitatu izi:
-
Mulungu amadana n’zoti anthu azivutika komanso amadana ndi kupanda chilungamo. Ganizirani mmene Yehova Mulungu anamvera pa nthawi imene atumiki ake ankazunzidwa. Baibulo limanena kuti Mulungu ankamva chisoni chifukwa anthu ‘ankakankhakankha’ atumiki akewo.—Oweruza 2:18, Baibulo la Dziko Latsopano.
Mulungu amadana kwambiri ndi anthu amene amazunza anzawo. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti Mulungu amadana ndi “manja okhetsa magazi a anthu osalakwa.”—Miyambo 6:16, 17.
-
Mulungu amatiganizira aliyense payekha. N’zoona kuti munthu aliyense payekha “akudziwa mliri wake ndi ululu wake.” Koma Yehova nayenso akudziwa zimene zikuchitikira munthu aliyense.—2 Mbiri 6:29, 30.
Posachedwapa Yehova athetsa mavuto amene munthu aliyense payekha akukumana nawo, ndipo achita zimenezi pogwiritsa ntchito Ufumu wake. (Mateyu 6:9, 10) Koma padakali pano, iye amatonthoza mwachifundo anthu amene akumufunafuna ndi mtima wonse.—Machitidwe 17:27; 2 Akorinto 1:3, 4.
GANIZIRANI MFUNDO IYI
N’chifukwa chiyani Mulungu akulola kuti tizivutika?
Baibulo limayankha funso limeneli pa AROMA 5:12 ndi pa 2 PETULO 3:9.