Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchitira Nkhanza Akazi Ndi Vuto la Padziko Lonse

Kuchitira Nkhanza Akazi Ndi Vuto la Padziko Lonse

Kuchitira Nkhanza Akazi Ndi Vuto la Padziko Lonse

NOVEMBER 25 ndi tsiku limene anthu padziko lonse amaganizira za vuto lochitira nkhanza akazi. Tsiku limeneli linakhazikitsidwa pa msonkhano waukulu wa bungwe la United Nations mu 1999 pofuna kudziwitsa anthu za mmene ena akuphwanyira ufulu wa akazi. N’chifukwa chiyani anaona kuti m’pofunika kuchita zimenezi?

M’madera ambiri, anthu amaona akazi ngati apansi kuyerekezera ndi amuna. Motero akazi sayesedwa kanthu. Akazi ambiri amazunzidwa m’njira zosiyanasiyana, ngakhale m’mayiko otukuka. A Kofi Annan, omwe kale anali mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations, ananena kuti “mchitidwe wochitira nkhanza akazi wafala padziko lonse, sunasiye malo kwina kulikonse ayi. Nkhanzazi zimachitika kwa akazi otchuka, osatchuka, a m’mafuko onse, m’madera onse ndiponso m’mabanja osiyanasiyana.”

Radhika Coomaraswamy, yemwe kale anali nthumwi yapadera ya nthambi yoona za ufulu wachibadwidwe ya bungwe la United Nations, anati akazi ambiri amaona kuti kuchitira nkhanza akazi “ndi nkhani yosayenera kukambirana, imene amangoibisa chifukwa ndi yochititsa manyazi kwambiri.” Bungwe lina loona za anthu ochitiridwa nkhanza la ku Holland linafotokoza kuti akazi 23 pa akazi 100 aliwonse m’dziko lina la ku South America, kapena kuti mkazi mmodzi pa akazi anayi aliwonse, akuchitiridwa nkhanza zinazake panyumba pake. Komanso bungwe lina la mayiko a ku Ulaya (Council of Europe) linati pafupifupi mkazi mmodzi pa akazi anayi aliwonse a ku Ulaya amachitiridwa nkhanza kunyumba pamoyo wake. Unduna wa za m’dziko ku Britain unati, m’chaka china chaposachedwapa, ku England ndi ku Wales, pafupifupi mlungu uliwonse akazi awiri ankaphedwa ndi anthu amene anali kukhala nawo monga amuna awo panthawiyo kapena kale. Magazini ina inafotokoza kuti “akazi ambiri ku India amakhala mwamantha kwambiri chifukwa nthawi iliyonse angathe kugwiriridwa kulikonse, kaya ndi mumsewu, kapena malo alionse omwe kumakhala anthu.” (India Today International) Bungwe lina loona za ufulu wachibadwidwe padziko lonse (Amnesty International) linafotokoza kuti kuchitira nkhanza akazi ndiwo “mchitidwe umene ukuphwanya kwambiri ufulu wachibadwidwe” masiku ano.

Pamenepa taona mmene anthu ambiri amaonera akazi. Kodi umu ndi mmenenso Mulungu amaonera akazi? Funso limeneli liyankhidwa m’nkhani yotsatira.