Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhala Bwinobwino M’chipale Chofewa

Kukhala Bwinobwino M’chipale Chofewa

Kukhala Bwinobwino M’chipale Chofewa

YOLEMBEDWA KU FINLAND

M’MADERA ozizira kwambiri padziko pano, munthu akhoza kudwala kapenanso kufa ngati atapanda kuvala zovala zotentha. Komabe, nyama zambirimbiri zimakhala mosangalala m’nyengo yotentha ndi yozizira yomwe. M’nyengo yachisanu, nyamazi zimamera nthenga ndi ubweya wotenthera bwino komanso zimatetezeka chifukwa cha chipale chofewa.

Kwenikweni, chipale chofewa ndi timibulu tomwe timapangidwa nthunzi ya madzi ikazizira kwambiri n’kuundana. Chipale chakuya masentimita okwana 25 chimakhala ndi madzi akuya masentimita awiri ndi theka. Choncho m’chipale chofewa mumakhala mpweya wambiri chifukwa timibuluti timakhala ndi mipatamipata. Chifukwa cha zimenezi, chipale chofewa chimathandiza kwambiri kuteteza njere za zomera ndiponso mbewu zosiyanasiyana kuti zisaume ndi chisanu mpaka nyengo yozizira itadutsa. Kenaka, chipale chofewachi chimasungunuka ndipo madzi ake amayenderera m’nthaka yonseyo mpaka kufika m’timakwawa tam’deralo.

Pansi pa Chipale Chofewa Pamakhala Zamoyo

Pansi pa chipale chofewa pamakhala tinyama tosiyanasiyana taubweya tomwe timayendayenda m’mayenje, pochita zinthu zosiyanasiyana, makamaka posaka chakudya. Tina mwa tinyamati ndi mbira, anamfuko, asakhwi kapena kuti zolo, ndi tinyama tina tomwe timadya tizilombo ting’onoting’ono. Pamwamba pa chipale chofewa pamakhalanso mbewa zomwe zimakhala yakaliyakali kufunafuna zakudya zosiyanasiyana zokhala ngati malubeni, mtedza, njere za mbewu zosiyanasiyana, ndiponso makungwa ofewa a mbewu zing’onozing’ono.

Kodi tinyama timeneti timatani kuti tisamazizidwe kwambiri? Tinyama tambiri tili ndi ubweya wotenthera bwino komanso thupi lawo limagaya chakudya mwamsanga, zomwe zimathandiza kuti lizitentha. Kuti zimenezi zitheke, tinyama timeneti timadya mwadzaoneni. Mwachitsanzo mbira imodzi imadya chakudya cholemera kuposa mbirayo. Imadya tizilombo monga ziyabwe ndiponso mbozi. Koma pali mtundu wina wa asakhwi umene umadya kuposa pamenepa. Motero kukangocha tinyama timeneti timangokhalira kufunafuna chakudya basi.

Tinyama tambiriti timadyedwanso kwambiri ndi nyama zina, monga akadzidzi komanso mitundu yosiyanasiyana ya amwiri. Amwiri amakhala ochenjera moti savutika kuthamangitsa tinyamati n’kutigwira. Mwiri amathanso kugwira mbira yaikulu kuposa msinkhu wake.

Nawonso akadzidzi amasaka tinyama tosiyanasiyana. Pali akadzidzi enaake amene ali ndi makutu otha kumva patali kwambiri moti amatha kumva namfuko akuyenda mu una wake pansi pa chipale chofewa, makamaka ngati chipalecho n’chosaya kwambiri. Kadzidziyo akadziwa pamene pali nyamayo, amalowa m’chipale chofewacho mwamphamvu n’kuimbwandira kenaka n’kuuluka nayo. Komabe, chipale chofewa chikazama kwambiri, nyama zochuluka zimakhala ndi njala, moti zina zimafa kumene. Zimenezi zimachititsanso kuti tinyama tina tichuluke mosowetsa mtendere.

Tinyama tina timanenepa kwambiri panyengo yotentha ndipo zimenezi zimathandiza kuti tisafe ndi njala chifukwa chosowa chakudya panyengo yozizirayi. Komabe, nthawi zambiri chakudya sichisoweratu. Mwachitsanzo, mphalapala zinazake za kumeneku zimadya tinsonga tamitengo, makamaka ya mkungudza. Agologolo amadya tinjere tinatake topatsa thanzi tomwe amatisunga m’malo osiyanasiyana, ndipo akalulu amachecheta makungwa ndiponso mphukira za mitengo. Palinso mbalame zinazake zimene zimadya mitundu yosiyanasiyana ya malubeni ndi zibalobalo za mkungudza.

Liwiro Lokalowa M’chipale Chofewa

Potsata kutentha kwa m’chipale chofewa, mbalame zambiri zimalowa m’chipalechi zikamapuma masana komanso zikamagona usiku. Pa mbalame zoterezi pali mitundu yosiyanasiyana ya nkhwali ndi mpheta. Chipale chofewacho chikakhala chakuya komanso chosalimba kwambiri, mbalame zina zimayatsa liwiro lokalowa m’chipalecho, ngati mmene mbalame zakunyanja zimalowera m’madzi. Nzeru imeneyi imathandiza kuti nyama zolusa zisaone mapazi a mbalamezi kapena kununkhiza njira imene zadutsa.

Mbalamezi zikafika m’kati mwachipalechi zimakumba dzenje lalitali mita imodzi ndi theka. M’Chifinishi dzenjeli lili ndi dzina (kieppi). Mphepo imene imawomba usiku imafufuta chizindikiro chilichonse chosonyeza kuti pansipo palowa mbalame. Anthu akamadutsa pafupi, mbalamezi zimadzidzimuka chifukwa cha mdidi wawo. Kubulika kwa mbalamezo zikamauluka kungathe kudzidzimutsa kwambiri anthuwo.

Kuvala Zotentha

Nyengo ya chisanu ikayamba kutha, nyama zina zimasintha mtundu pomerera ubweya kapena nthenga zamaonekedwe ofanana ndi chipale chofewa. Ku Finland kuli mitundu ina ya ankhandwe, akalulu ndiponso amwiri osiyanasiyana imene imamerera ubweya wambiri woyera kapena wambuu.

Komanso pali mtundu wina wa nkhwali umene umakhala ndi nthenga zamawangamawanga. Nthenga za nkhwali zimenezi zimasintha n’kumaoneka zoyera monyezimira. Zipalapaso zawo, zomwe m’nthawi yotentha zimakhala zaubweya wa apo ndi apo, zimamerera ubweya wambiri m’nyengo yozizira, womwe umaziteteza ngati nsapato. Posintha maonekedwewa, nyama zambiri zimatetezedwa ku zinyama zoopsa chifukwa choti zimaoneka mofanana kwambiri ndi malowo, omwe amakhala ndi chipale chofewa mwina ndi mwina.

Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti n’chifukwa chiyani mbalame zambiri zimayenda bwinobwino pa chipale chofewa popanda chilichonse choteteza zipalapaso zawo? N’chifukwa choti zipalapaso zawo zinapangidwa m’njira yodabwitsa kwambiri kuti zisamamve kuzizira. Zimenezi zimathandiza kuti magazi otentha ochokera kumtima azikatenthetsa mapazi komanso kuti magazi ochokera ku mapaziko, omwe amakhala ozizira, azitenthetsedwa.

Inde, zamoyo zosiyanasiyana sizivutika padziko pano ngakhale m’madera ozizira kapena otentha kwambiri. Izo zimakhala bwinobwino m’madera onsewa. Anthu amene amajambula zithunzi zosonyeza mmene nyama zimenezi zimakhalira amapatsidwa ulemu kwabasi, ndipotu m’pomveka. Komatu amene ayenera kulandira ulemu waukulu kwambiri ndi Mlengi wa zinthu zodabwitsa kwambiri zimenezi. Lemba la Chivumbulutso 4:11 limati: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu, kulandira ulemerero, ndi ulemu, ndi mphamvu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo chifukwa cha chifuniro chanu, zinakhalapo, inde zinalengedwa.”

[Bokosi/Chithunzi patsamba 18]

Akhristu Osaopa Kuzizira

M’nyengo yozizira, Mboni za Yehova ku Finland zimavala zovala zotentha n’kumapitiriza kuchita ntchito zawo zosiyanasiyana zauzimu. Amboni ena amayenda maulendo aatali kupita kumisonkhano ya mpingo. Ndipotu ngakhale m’madera akumidzi, Amboni sajomba kumisonkhano m’miyezi yambirimbiri imene kunja kumakhala kukuzizira. Amboni za Yehova amakhalanso kalikiliki kugwira ntchito yawo yolalikira. Ndithu, iwo amaona kuti ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala Mboni za Mlengi, Yehova Mulungu, moti amalolera kutuluka panja pozizira kuti akauze ena za Ufumu wake.—Mateyo 24:14.

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Mbalame zitabisala pansi pa chipale chofewa

[Mawu a Chithunzi]

By courtesy of John R. Peiniger

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Mtundu wina wa amwiri

[Mawu a Chithunzi]

Mikko Pöllänen/​Kuvaliiteri

[Chithunzi patsamba 17]

Abakha am’madzi

[Zithunzi patsamba 17]

Kalulu

[Chithunzi patsamba 17]

Nkhandwe