Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Miyambo Yakale Ilipobe ku Mexico

Miyambo Yakale Ilipobe ku Mexico

Miyambo Yakale Ilipobe ku Mexico

YOLEMBEDWA KU MEXICO

MIYAMBO yakale yachipembedzo ku Mexico ndi yofala kwambiri ngati mmene alili mafoni a m’manja ndi Intaneti. Kwa zaka zambiri, miyambo ina ya amwenye inasakanikirana ndi miyambo ya tchalitchi cha Roma Katolika. Ndipotu, Akatolika ambiri ku Mexico amatsatira miyamboyi polambira.

Mwachitsanzo, chaka ndi chaka pa November 2, anthu ambiri ku Mexico amapita ku manda kukachita mwambo wa Tsiku la Anthu Akufa. Iwo amaika maluwa, chakudya ndiponso mowa pamandapo poganiza kuti akufawo amwa. Enanso amaitana magulu a zoimbaimba kuti aimbe nyimbo zimene anthu akufawo ankakonda. Akatolika ambiri amamanga maguwa m’nyumba zawo ndipo m’maguwamo amaikamo zithunzi za abale awo amene anamwalira.

Buku lina (Enciclopedia de México) limafotokoza kuti miyambo ina yokhudza anthu akufa imatsatiridwa mwina ndi cholinga choti “miyambo ina ya amwenye isaiwalike. Miyamboyi inkachitika m’miyezi inayake ndipo pa miyambo yotereyi anthu ankapereka nsembe za maluwa ndi chimanga, ndipo zimenezi zinkachitika atangomaliza kukolola, cha kumapeto kwa October ndiponso cha kumayambiriro kwa November.” Monga mmene bukuli limanenera, ina mwa miyambo imeneyi imafanana ndi miyambo ina yakalekale ya anthu ochokera ku Latin America. Pa miyambo imeneyi anthuwo ankayenda m’misewu akuimba.

Kulambira Kwawo

Chaka chilichonse pa December 12, Akatolika a ku Mexico amakhala patchuthi. Patsikuli, anthu ambirimbiri ochokera m’madera osiyanasiyana m’dzikolo amakasonkhana ku tchalitchi cha Virigo wa ku Guadalupe, chomwe chili m’mphepete mwa phiri lotchedwa Tepeyac ku Mexico City. Anthu ambiri amayenda ulendo wa masiku angapo kwinaku akupemphera kwa Virigoyo. Anthuwa akafika kumeneko amalowa m’tchalitchi akuyenda ndi mawondo (pamwambapa), n’kukapereka nsembe za maluwa okongola.

Masiku ano, zithunzi za Virigo wa ku Guadalupe zimapezekanso m’nyumba za anthu, m’malo okwerera basi ndiponso m’malo ena. Virigoyu amadziwikanso ndi dzina lakuti “Amayi a Mulungu” ndiponso “Virigo Woderako wa ku Tepeyac.” Kungoyambira cha m’ma 1500 C.E., anthu ambiri akhala akukhulupirira kuti Virigoyu amachiritsa ndiponso amachita zinthu zina zodabwitsa.

Zinayamba Bwanji?

Kalekale, anthu otchedwa Aaziteki ndiwo anayambitsa mwambo wolemekeza milungu yaikazi ndi zinthu zina zomwe zimachitika pamwambowu. Iwowa ankalambira mulungu wamkazi wotchedwa Cihuacóatl kapena kuti Tonantzin, kutanthauza kuti “Mayi Wathu Wamng’ono.” Buku lina lonena za mbiri ya ku Mexico (México a través de los siglos) limafotokoza kuti Aaziteki ndiwo anabwera ndi mulunguyu komanso mwana wake Huitzilopochtli ku likulu la ufumu wawo lotchedwa Tenochtitlán, lomwe panopa ndi mzinda wa Mexico City.

Kachisi wa mulunguyu anamangidwa m’mphepete mwa phiri la Tepeyac ndipo anawonongedwa ndi asilikali a ku Spain. Malingana ndi zimene anthu ambiri kumeneku amakhulupirira, akuti Virigo wa ku Guadalupe anaonekera kwa mmwenye wina wakumeneko, dzina lake Juan Diego, pasanathe zaka 40 Columbus atafika m’dzikolo. Akuti Virigoyu anapempha kuti pamalowo amangepo kachisi.

Virigoyu ankalemekezedwa kwambiri ndi Aaziteki. Akuti iye anali ndi tsitsi lalitali, losapotana ndipo ankavala mkanjo woyera. Khomo lolowera ku kachisi wake linali laling’ono kwambiri moti anthu ankalowa chogwada. Akalowa m’kati mwa kachisiyo, anthu odzapembedzawo ankatha kuona chithunzi cha mulunguyu chitazunguliridwa ndi mafano ndipo zimenezi zinali kumuchititsa kuoneka ngati “mayi . . . wa milungu yonse.”

Popembedza mulungu wamkaziyu, ankapereka anthu nsembe, ankavina ndipo gulu la asilikali “linkanyamula maluwa m’manja. Maluwa ena ankawakoloweka m’khosi ndipo ena ankawaika pa mutu.” Mphatso zimenezi ankaziika padenga la kachisi kuti mwana wa Virigo uja azilandire. Amwenye ena, kuphatikizapo a ku Guatemala, ankayenda ulendo wa makilomita ambirimbiri kuti akapezeke ku mwambowu.

Kudziwa Chiyambi Chake N’kofunika

N’zoonekeratu kuti kulambira fano la Akatolika la Virigo wa ku Guadalupe, kunayamba ndi anthu amene sankalambira Mulungu woona wotchulidwa m’Baibulo. (Salmo 83:18) Ndiyeno kodi ifeyo tiyenera kuona motani kulambira kumeneku? Kodi kudziwa mmene kalambiridwe kenakake kanayambira n’kofunikadi?

Mtumwi Paulo anapereka malangizo anzeru pankhaniyi. Iye anati: “Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira. . . . Pali m’gwirizano wanji pakati pa Khristu ndi Beliyali? Kapena munthu wokhulupirira agawana chiyani ndi wosakhulupirira?” Paulo ananenanso kuti: “Tsimikizirani zinthu zonse. Gwirani zolimba chimene chili chabwino.”—2 Akorinto 6:14, 15; 1 Atesalonika 5:21.

Mfundo imeneyi ndi yofunikanso masiku ano. Tikamalambira Mulungu, tiyenera kumadzifunsa kuti: ‘Kodi kulambira kwanga n’kogwirizana ndi zimene Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, limaphunzitsa? Kapena kodi n’kosakanikirana ndi ziphunzitso za anthu amene amalambira milungu yonyenga?’ Munthu aliyense amene akufuna kusangalatsa Mulungu woona Yehova, ayenera kufufuza mayankho a mafunso ngati amenewa.

[Chithunzi patsamba 23]

Oyimba ali kumanda, pa November 2

[Chithunzi patsamba 23]

Alendo odzapembedza akufika pa tchalitchi cha Virigo wa ku Guadalupe