Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyenda pa Boti ku Kerala

Kuyenda pa Boti ku Kerala

Kuyenda pa Boti ku Kerala

YOLEMBEDWA KU INDIA

TAGANIZIRANI kuti mwakwera boti lokongola lokhala ndi zonse m’kati ndipo likakufikitsani m’malo 44 amene mitsinje yosiyanasiyana imakumanirana ndi nyanja. Mungathe kukwera boti lotereli paulendo wa makilomita 900 m’madera akumidzi a boma la Kerala, kum’mwera cha kumadzulo kwa dziko la India. Kukwera maboti amenewa n’kosangalatsa kwambiri. Botilo likamayenda pang’onopang’ono mumatha kuona gombe lokongola. M’mphepete monse mwa gombeli mumaona mitengo ya mgwalangwa, mbewu zampunga zobiriwira, nyanja zosiyanasiyana zachilengedwe, ndiponso ngalande. N’kutheka kuti chifukwa cha madera akumidziwa, magazini ina inati Kerala “ndi dera limodzi mwa madera 50 ‘amene munthu aliyense ayenera kuyesetsa kukafikako pamoyo wake.’”National Geographic Traveler.

Komanso anthu amene amakhala kumeneku ndi ochititsa chidwi kwambiri. Iwowa amakumbukira kuti kale kuderali kunalibe alendo alionse odzaona malo ndipo kunalibe mahotela alionse apamwamba. Komabe, moyo wawo sikuti unasintha kwenikweni ayi. Ngakhale kuti tsopano ena mwa anthuwa analembedwa ntchito m’mahotela kapena m’ntchito zina zokopa alendo, zinthu zambiri pa chikhalidwe chawo sizinasinthe ayi. Amasamalira mpunga umene amalima ndiponso mitengo yawo ya mgwalangwa. Amawedzanso nsomba kuti apeze chakudya ndi ndalama.

Kuwedza Nsomba M’maderawa

Anthu ambiri a kuno ndi asodzi. Ndi kuno kokha kumene mungaone azimayi akugwira nsomba (zotchedwa karimeen) ndi manja. Nsomba zimenezi zimapezeka m’madera akumidzi a ku Kerala ndipo amwenye komanso alendo obwera kuno amazikonda kwambiri. Pofunafuna nsombazi, azimayiwo amayenda mumtsinje mapoto awo akuyandama m’mbuyo mwawo. Nsombazo zimabisala m’matope zikangoona azimayiwo. Komabe azimayiwo anazidziwirira nsombazi moti amapapasira ndi mapazi awo kuti adziwe pamene zabisala. Akazipeza amazimbwandira msangamsanga n’kuziika m’mapoto aja. Akagwira nsomba zambiri ndithu amapita kumtunda kumene anthu amawayembekezera kuti agule. Nsomba zikuluzikulu ndiponso zodula amazigulitsa m’mahotela akuluakulu, ndipo anthu olemera ndi amene amadya. Nsomba zing’onozing’ono zimagulidwa ndi anthu osauka ndipo zimakoma kwambiri.

Maukonde a ku China

M’madera amenewa mumaona maukonde ambirimbiri a ku China. Anthu ambiri amabwera kudzaona maukondewa.

Zikuoneka kuti anthu amalonda ochokera ku Kublai Khan m’dziko la China, ndi amene anabweretsa maukondewa ku Cochin (kumene tsopano kumatchedwa Kochi) chisanafike chaka cha 1400. Anthu oyambirira kugwiritsa ntchito maukonde amenewa anali Matchaina ndipo kenako Apwitikizi. Masiku ano, asodzi ambiri a ku India amadalira maukondewa, omwenso amathandiza kuti anthu ambirimbiri azipeza chakudya ngati mmene zinkachitikira zaka 600 zapitazo. Chochititsa chidwi n’chakuti nsomba za muukonde umodzi wokha zingakwanire anthu a m’mudzi wonse. Anthu ambiri odzaona malo amakonda kujambula zinthunzi zokopa za maukondewa atayanikidwa padzuwa.

Sizithunzi za maukonde a ku China zokha zimene zimakopa alendo m’derali. Chaka chilichonse anthu ambirimbiri amabweranso kuno kudzachita zinthu zina, monga mpikisano wa maboti.

Mpikisano wa Maboti

Maboti amene amachitira mpikisano amakhala aatali. Kutsogolo kwake kumaoneka ngati mutu wa mamba, moti anthu amangowatchula kuti boti la njoka. Kalekale, mafumu a m’madera amenewa ankagwiritsira ntchito mabotiwa pa nkhondo zomwe ankachita akatha kukolola. Nkhondozo zitatha, mabotiwo sankafunikiranso kwenikweni. Motero ankangowagwiritsira ntchito pa zikondwerero za kukachisi. Pazikondwererozi mabotiwa ankawakongoletsa kwambiri kuti azisonyeza chikhalidwe chawo. Panthawi yachikondwereroyo, ankachita mpikisano wa maboti pofuna kuti akuluakulu azionerera. Mwambo umenewu unayamba pafupifupi zaka 1000 zapitazo ndipo udakalipobe.

Nthawi zambiri maboti 20 oterewa amakhala nawo pa mipikisano yotereyi ndipo m’boti lililonse mumatha kukhala amuna 100 kapena 150. Anthu oposa 100 amakhala moyang’anizana m’botilo atatenga zopalasira zifupizifupi. Kumbuyo kwa mabotiwa kumakhala amuna anayi omwenso amapalasa botilo ndi zopalasira zikuluzikulu. Anthu ena awiri amakhala pakatikati pa botilo ndipo amaomba ching’oma china ndi mitengo kuti opalasa ayambe ntchito yawo. Opalasawo amalimbikitsidwanso ndi anthu ena pafupifupi 6 amene amakwera nawo botilo. Anthu amenewa amaimba m’manja, malikhweru, kuchemerera ndi kuimba nyimbo kuti opalasawo apitirize kupalasa paliwiro lomwelo. Ndiyeno opalasa botilo amalimbikira kupalasako motsatira nyimbozo mpaka kukafika kumapeto kwa mpikisanowo.

M’chaka cha 1952 mtsogoleri woyamba wa ku India Jawaharlal Nehru, anapita m’tauni yodziwika kwambiri m’derali yotchedwa Alleppey. Iye anasangalala kwambiri kuonera mpikisano umenewu. Iye anatengeka mtima kwambiri moti anachoka pamalo otetezeka amene anam’konzera n’kudumphira m’boti lomwe linapambana kenaka n’kuyamba kuwomba m’manja ndi kuimba nyimbo pamodzi ndi anthu opalasawo. Atabwerera ku Delhi, mtsogoleriyu anatumiza mphatso ya chidole chasiliva cha botilo chokhala ndi siginecha yake ndipo analembapo kuti: “Mphatso ya opambana mpikisano wa maboti umene umasonyeza chikhalidwe chenicheni cha anthu a kuno.” Chidole chimenechi amachigwiritsa ntchito ngati chikho chimene anthu opambana mpikisanowo amapatsidwa. Chaka chilichonse anthu ambirimbiri amapita kukaonerera mpikisanowu. Panthawiyi m’dera lakumidzi limeneli mumachitika zinthu zambiri.

Mahotela Okongola Oyenda Panyanja

Sikuti anthu amangopita kuderali kukaona maboti amtundu wokhawu. Palinso mtundu wina wa maboti amene anthu amawakonda. Mabotiwa ndi achikalekale kwambiri koma anawakonza kuti akhale ngati nyumba zabwino kwambiri.

Ngakhale kuti maboti amene amatenga anthu okaona malo ndi okonzedwa posachedwapa, maboti ambiri akhala zaka zoposa 100. Kalelo ankatchedwa kettuvallam kutanthauza kuti “maboti a mfundo.” Boti lonselo linkapangidwa ndi matabwa olumikizidwa ndi zingwe zomangidwa mfundo popanda kukhoma misomali. Maboti amenewa ankagwiritsidwa ntchito ponyamula mpunga ndi zinthu zina kuchokera ku mudzi wina kupita kumudzi wina kapena kutenga zinthu zokometsera zakudya kupita nazo madera akutali. Chifukwa cha njira zatsopano za kayendedwe, mabotiwa anasiya kugwira ntchito. Ndiyeno munthu wina wodziwa bizinesi anaganiza zokonzanso maboti amenewa kuti akhale ngati nyumba zoti anthu odzaona malo azigwiritsa ntchito. Mabotiwa amakhala ndi zipinda zochezera komanso zogona zokhala ndi mabafa. Izi n’zimene zimachititsa kuti mabotiwa azikhala ngati mahotela ndithu. Pamakhala anthu okuperekezani pabotilo n’kumayenda nanu kulikonse kumene mukufuna komanso kukuphikirani chakudya chilichonse cha ku mtima wanu.

Kukada, mabotiwa amawakocheza mphepete mwa nyanja koma anthu amene akufuna kuti asamaonedwe ndi anthu ena amakocheza m’kati mwa nyanjayo. Munthu ukakhala kumeneku umasangalala chifukwa ndi kwa phee ngakhale kuti nthawi zina nsomba zimachita phokoso posewera.

Komabe sikuti anthu onse m’derali amangochita zinthu mwa phee. Kuli “asodzi a anthu” omwe achangu kwambiri.

‘Kusodza Anthu’ Kuderali

Mawu akuti “asodzi a anthu” ndi amene Yesu anauza asodzi amene anakhala ophunzira ake. Iye anati: “Nditsatireni ine, ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.” Yesu ankanena ntchito yothandiza anthu kukhala ophunzira ake. (Mateyo 4:18, 19; 28:19, 20) Mboni za Yehova zikugwira ntchito imeneyi padziko lonse kuphatikizapo malo ozungulira derali.

M’boma lonse la Kerala muli mipingo ya Mboni za Yehova 132 ndipo 13 mwa mipingo imeneyi ili kuderali. Anthu ambiri a m’mipingo imeneyi ntchito yawo ndi yopha nsomba. Tsiku lina msodzi wina anauza mnzake amene amasodza naye za Ufumu wa Mulungu. Sipanatenge nthawi yaitali kuti mnzakeyo aone kuti zimene ankaphunzira kutchalitchi chake ndi zosiyana ndi za m’Baibulo. Mkazi wake ndi ana ake anayi anayambanso kuphunzira Baibulo. Iwo anapita patsogolo mwamsanga ndipo panopo anthu anayi m’banjamo anabatizidwa. Ana ena awiriwo atsalanso pang’ono kubatizidwa.

Anthu ena a m’mpingo wina anayenda paboti kupita kukachilumba kena kuti akalalikire. Chifukwa chakuti maboti akuderali ndi osadalirika, chilumbachi anachipatsa dzina lakuti kadamakudi kutanthauza kuti “kosachokeka.” Ku chilumbachi, Mboni za Yehova zinakumana ndi Johny pamodzi ndi mkazi wake Rani. Iwowa anali Akatolika ndipo analinso m’gulu lina lachipembedzo kumene anapereka ndalama zawo zambiri. Komabe Johny anachita chidwi ndi uthenga wa choonadi cha m’Baibulo ndipo anayamba kuphunzira Baibulo. Iye anayamba kuuzanso anzake za chikhulupiriro chake chatsopanocho. Choonadi cha m’Baibulo chinamuthandizanso kusiya kusuta ndi kuledzera.

Ntchito imene Johny ankagwira inali yosagwirizana ndi Malemba choncho anasiya. Izi zinachititsa kuti banja lawo lisauke kwanthawi ndithu. Kenako Johny anayamba kugwira nkhanu n’kumagulitsa ndipo izi zinam’thandiza kusamalira banja lake. Iye anabatizidwa mu September 2006 ndipo mkazi wake ndi ana ake awiri anabatizidwa chaka chotsatira. Chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso chinasinthiratu maganizo awo.—Salmo 97:1; 1 Yohane 2:17.

N’zosangalatsa kwambiri kupita ku Kerala n’kukafika m’dera limeneli. Sikuti kumangosangalatsa chifukwa cha zinthu monga maukonde, maboti a mpikisano ndi maboti okhala ngati nyumba. Kumasangalatsanso chifukwa cha “asodzi a anthu,” omwe ndi Mboni za Yehova zokhulupirika za kumeneko.

[Mapu pamasamba 22, 23]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

INDIA

KERALA

[Chithunzi patsamba 23]

Ku Kerala anthu ambiri ndi asodzi

[Mawu a Chithunzi]

Top photo: Salim Pushpanath

[Chithunzi patsamba 23]

Azimayi akugwira nsomba ndi manja

[Chithunzi patsamba 24]

Mpikisano wa maboti

[Chithunzi patsamba 24]

“Kettuvallam”

[Chithunzi pamasamba 24, 25]

Boti langati nyumba

[Chithunzi pamasamba 24, 25]

Johny ndi mkazi wake Rani

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

Salim Pushpanath