Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akambuku Akuluakulu a ku Siberia Satheratu?

Kodi Akambuku Akuluakulu a ku Siberia Satheratu?

Kodi Akambuku Akuluakulu a ku Siberia Satheratu?

YOLEMBEDWA KU RUSSIA

Tsiku lina m’nyengo yozizira ku Russia, kambuku wamkulu anathamanga kwambiri m’chipale chofewa uku ndege ikubwera. Ndiyeno munthu wina m’ndegemo anatulutsa mutu wake mfuti ili m’manja, ndipo kambukuyo anakwera mumtengo uku akubangula. Kenako, munthu uja anawombera kambukuyo. Zitatero, ndege ija inatera ndipo anthu anatsika mochenjera n’kupita pamene panagwera kambukuyo.

KODI amenewa ndi opha nyama moswa lamulo? Ayi. Iwo ndi anthu oona zachilengedwe ndipo kambukuyo anamuwombera ndi zipolopolo zongofooketsa. Anabwera kuno kudzaphunzira za akambuku akuluakulu a ku Siberia * amene atsala pang’ono kutheratu.

Akambukuwa ndi Okongola Kwambiri

Akambuku amtundu umenewu ankapezeka ku Korea, Northern China, Mongolia, ndiponso kum’mwera cha kunyanja ya Baikal, ku Russia. Koma akambukuwa akucheperachepera. Panopo kumene amakhala motetezeka ndi kumapiri akutali, chakumpoto kwa Vladivostok, m’dziko la Russia, m’mphepete mwa nyanja ya Japan.

Akambukuwa amadziwana chifukwa cha fungo moti akambuku aamuna savutika kupeza akambuku aakazi. Amabereka ana awiri kapena atatu ndipo anawo akangobadwa kumene saona. Anawo amasimbwa ngati ana a mphaka, kungoti iwowa salira ngati amphaka ayi. Amangolira chapansipansi kwinaku akuyamwa. Amayamwa kwa miyezi isanu kapena isanu ndi umodzi. Kenako amayamba kudya nyama. Poyamba amasakira limodzi ndi mayi wawo ndipo amakhala chaka chimodzi ndi theka asanayambe kusaka paokha. Akambuku aang’ono amakhala ndi amayi awo, mwina kwa zaka ziwiri, kenako amakakhala paokha.

Akakhala kutchire, ena mwa akambuku amenewa amakula kwambiri. Aamuna amalemera mwina makilogalamu 270 ndipo kuchokera kumutu mpaka kufika kumchira amatalika mamita atatu. Akambuku amenewa savutika m’nyengo yozizira kwambiri. Amakhala ndi ubweya wambiri ndipo mapazi awo amakhalanso ndi ubweya wambiri moti amangokhala ngati avala nsapato.

Thupi la akambuku amenewa limakhala lonkera kuchikasu ndipo limakhala ndi mawanga akuda. Mawanga a kambuku aliyense wa mtunduwu amakhala osiyana ndi wina. Kusiyana kwake n’kofanana ndi mmene zimasiyanirana zidindo za zala za anthu. Chifukwa cha mawanga ake, kambuku ameneyu akangokhala phee m’tchire saoneka. Koma m’nyengo yozizira amaonekera kwambiri akamayenda m’chipale chofewa m’malo opanda mitengo. Izi zimachititsa kuti anthu ofuna kugwira nyamazi asamavutike kuziona ndipo ndi anthu okha amene amapha nyamazi.

Akhoza Kutha Onse

Akambukuwa amadya nyama zikuluzikulu monga mitundu yosiyanasiyana ya mphalapala za kumeneku. Koma nyama zimenezi zikusowa kwambiri m’derali. M’nkhalango yaikulu makilomita 1,000 mukhoza kupezeka nyama zongokwanira akambuku anayi kapena asanu okha. Motero kuti akambuku amenewa apeze chakudya chokwanira pamafunika nkhalango zazikulu kwambiri.

Kwa zaka zambiri, ku Siberia kunali nkhalango zambiri mmene akambukuwa ankakhala bwinobwino. Ndi anthu ochepa kwambiri amene ankafika ku nkhalango zimenezi kuti akagwire nyamazi. Koma masiku ano, makampani ambiri akudula mitengo yambiri pofuna matabwa.

Kutha kwa mitengoyi kukuchititsa kuti mphalapala zamitundumitundu komanso akambuku amenewa asowe. Pofuna kuti akambuku amenewa asatheretu, boma la Russia lateteza nkhalango zingapo kuti nyamazi zizikhalamo. Mwachitsanzo kuli nkhalango yotchedwa Sikhote Alin Nature Reserve. Koma akambukuwa akatuluka m’nkhalangoyi amatha kugwidwa ndi anthu osaka. Mano, zikhadabo, mafupa komanso zikopa za akambuku amenewa ndi zamtengo wapatali.

Kuteteza Akambukuwa

Anthu ambiri akuyesetsa kuteteza Akambuku amenewa. Chifukwa cha zimenezi chiwerengero cha akambukuwa chawonjezeka pang’ono. Mu 2005, kafukufuku anasonyeza kuti ku Siberia kuli akambuku pafupifupi 430 kapena 540 a mtundu umenewu.

Komabe akambuku oweta amaberekana kwambiri ndipo amakula bwino ndithu. Padziko lonse pali akambuku oterewa pafupifupi 500 amene akusungidwa m’malo osungira nyama. Koma n’chifukwa chiyani akambukuwa sawapititsanso kutchire kuti akapitirize kuswana? Asayansi safuna kuchita zimenezi. Ndipo wina anati: “Sibwino kukaika dala nyama m’tchire mukudziwa kale kuti akaipha.”

Zamoyo zonse kuphatikizapo akambuku akuluakuluwa zimasonyeza kuti Mulungu ndi wanzeru komanso ndi wamphamvu. Mulunguyo amaona kuti n’zofunika ndipo amazisamalira. (Salmo 104:10, 11, 21, 22) Anthu ambiri amene amayamikira zimene Mlengi anachita sakayikira kuti ikudza nthawi imene moyo wa akambukuwa sudzakhalanso pangozi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Nyama zimenezi zimatchedwanso tiger, kapena kuti akambuku a ku Amur chifukwa chakuti zimapezeka pafupi ndi mtsinje wa Amur ku Russia.

[Bokosi/Chithunzi pamasamba 16, 17]

KAMBUKU WAMKULU KWAMBIRI

Kambuku amene bambo ake ndi mkango ndipo mayi ake ndi kambuku wa ku Siberia, amakhala wamkulu kwambiri. Akakula amakhala wamtali kuposa mamita atatu ndipo amalemera makilogalamu oposa 500. Ana oterewa amabadwira m’malo osungira nyama ndipo m’povuta kuti apezeke m’nkhalango.

[Mawu a Chithunzi patsamba 16]

Top: © photodisc/age fotostock; bottom: Hobbs, courtesy Sierra Safari Zoo, Reno, NV