Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumene Ndinamvera Dzina Loti Yehova

Kumene Ndinamvera Dzina Loti Yehova

Kumene Ndinamvera Dzina Loti Yehova

Yosimbidwa ndi Pavol Kovár

Tinayenda movutikira kukabisala pamalo enaake chifukwa cha mabomba amene anali kuphulitsidwa. Mabombawo anafika poipa kwambiri moti anagwedeza kwambiri ndende yathu. Zitatero mkaidi mnzathu wina anapemphera mokweza kuti: “Yehova, chonde tipulumutseni! Chonde tipulumutseni kuti dzina lanu likwezeke!”

ZIMENEZI zinachitika pa January 8, 1945, pamene ndinagwidwa ukaidi ndili msilikali mumzinda wa Linz, ku Austria. M’ndendeyo tinalimo anthu 250 ndipo tonse tinapulumuka pamene mabombawa ankaphulika. Titatuluka m’ndendemo, tinaona kuti zinthu zambiri zinali zitawonongeka. Pemphero lija linandikhudza mtima kwambiri, ngakhale kuti sindinadziwe kuti ndani ankapemphera chonchoyo. Ndisanafotokoze mmene ndinadziwira kuti Yehova ndi ndani, ndiyamba ndafotokoza pang’ono za moyo wanga.

Ndinabadwira kunyumba, pa September 28, 1921, pafupi ndi tauni ya Krajné, kumadzulo kwa Slovakia, kumene panthawiyo kunali mbali ya dziko la Czechoslovakia. Makolo anga anali Apulotesitanti okonda kupemphera. Bambo ankakonda kuwerenga Baibulo Lamlungu m’mawa, ndipo mayi ndi ana anayife tinkangokhala phee n’kumamvetsera. Koma sindinamvepo bambo akutchula dzina lakuti Yehova. M’dera limene tinkakhala, anthu ambiri ankakhala moyo wosalira zambiri, koma tonse tinkakhutira ndi zinthu zochepa zomwe tinali nazo.

Mu 1939, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itayamba, anthu ambiri anachita mantha. Anthu ambiri ankakumbukira mmene anavutikira pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, zaka 20 za m’mbuyomo. Mu 1942, anandiitana kuti ndikalembetse usilikali m’gulu la nkhondo la dziko la Slovakia. Ngakhale kuti dziko la Slovakia linanena kuti pankhondoyo lili ku mbali ya dziko la Germany, mu August 1944 dzikoli linkafuna kukhazikitsa ulamuliro wa demokalase. Zimenezi zitalephereka, ine ndinali m’gulu la asilikali ambirimbiri a ku Slovakia amene anagwidwa n’kukaikidwa m’madera olamulidwa ndi Ajeremani. Ineyo anakandisiya m’ndende ya Gusen, yoyandikana ndi ndende yotchuka yozunzirako anthu yotchedwa Mauthausen, kufupi ndi ku Linz.

Ndili Mkaidi

Tinapatsidwa ntchito pa malo okonzera ndege kufupi ndi tawuni yotchedwa Sankt Georgen an der Gusen. Ndipo ine ndimagwira ntchito yocheka matabwa. Ankatipatsa chakudya chochepa ndipo mu January 1945 anachepetsanso chakudyacho chifukwa chakuti asilikali a Nazi anayamba kugonja m’madera onse momwe m’mamenyedwa nkhondoyo. Chakudya chophika chimene tinkalandira chinali supu basi. M’mawa uliwonse kunkabwera anthu amene ankagwira ntchito kundende ya Mauthausen. Asilikali ankamenya munthu aliyense amene anali wofooka mpaka kumupha. Zikatero akaidi ankanyamula mitemboyo pangolo n’kupita nayo kumalo owotchera mitembo.

Ngakhale kuti panali mavuto ambiri, tinali ndi chiyembekezo choti nkhondoyo itha. Pa May 5, 1945, patangodutsa miyezi inayi kuchokera pamene tinapulumuka mabomba aja, panachitika chipwirikiti chomwe chinandidzidzimutsa. Nditadzuka ndinathamangira kunja n’kupeza kuti asilikali onse anathawa ndipo mfuti zawo zaunjikidwa malo amodzi. Mageti anali otsegula. Kenako tinaona kuti ku ndende ina akaidi anamasulidwa ndipo anangoti nyomi ngati njuchi zothawa moto. Akaidiwo atangomasulidwa anayamba kubwezera zoipa zimene ankachitiridwa. Ndimakumbukirabe nkhanza zina zimene zinachitika.

Akaidi ankamenya mpaka kupha anyapala amene ankachitira nkhanza anzawo pofuna kusangalatsa asilikali oyang’anira ndende. Anyapala amenewa anali ankhanza mwinanso kuposa asilikali a Nazi. Ndinaona mkaidi wina akumenya nyapala wina mpaka kumupha uku akufuula kuti: “Ameneyu anapha bambo anga dzana lomweli. Lero ndikanapulumuka nawo limodzi.” Pofika madzulo mitembo ya anyapala ndi akaidi ena inali ngundangunda muudzu. Tisananyamuke tinazungulirazungulira pa ndendeyo n’kumaona malo ndi zipangizo zimene ankaphera anthu.

Ndinaphunzira za Mulungu Woona

Ndinafika kwathu cha ku mapeto kwa May, mu 1945. Panthawiyi n’kuti makolo anga ataphunzira kale za Yehova, mpaka kukhala Mboni za Yehova. Nditangofika, sipanatenge nthawi ndipo ndinadziwana ndi Ol’ga. Iye anali mtsikana wokonda Mulungu, ndipo tinakwatirana patatha chaka chimodzi. Chifukwa cha khama lake lofuna kudziwa choonadi cha m’Baibulo iye anandilimbikitsa kupitiriza kuphunzira za Yehova. Ineyo ndi Ol’ga pamodzi ndi anthu enanso 50 tinabatizidwa mu mtsinje wa Váh ku Piešťany, pa msonkhano wina. Izi zinachitika ntchito yolalikira isanaletsedwe ndi boma la chikomyunizimu mu 1949. Kenako tinali ndi ana awiri aakazi ndipo mayina awo anali Oľga ndi Vlasta.

M’bale wina dzina lake Ján Sebín ndi amene anathandiza kwambiri kuti ntchito yolalikira iyambenso pambuyo pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Iye ankabwera kawirikawiri kunyumba kwathu ndipo tinkayendera limodzi muutumiki. Ngakhale kuti boma la chikomyunizimu linkatizunza, tinapitirizabe kulalikira. Tinkalalikira choonadi cha Baibulo mosamala ndipo tinali ndi maphunziro a Baibulo ambiri. Ján atachoka, ine ndi mkazi wanga tinapitiriza kuchititsa maphunziro amenewa. Pamisonkhano ikuluikulu tinkakumana ndi abale athu okondedwawa, limodzi ndi ana awo komanso zidzukulu zawo. Tinkasangalala kwambiri panthawi imeneyi.

Utumiki Wapadera

Pofika mu 1953, Mboni zambiri zimene zinkatsogolera ntchito yolalikira zinamangidwa. Choncho ndinapemphedwa kuti ndizikatumikira kudera lina lomwe linali pa mtunda wa makilomita 150 kuchokera kumene tinkakhala. Ndinkapitako pa milungu iwiri iliyonse ndipo ndinkanyamuka Loweruka madzulo. Ndinkakwera sitima m’tauni ya Nové Mesto nad Váhom kupita ku Martin kumpoto chapakati m’dziko la Slovakia. Lamlungu, ndinkaphunzitsa anthu Baibulo tsiku lonse. Madzulo ndinkakwera sitima kubwerera ku Nové Mesto. Ndinkafika kumudzi pakati pa usiku ndipo ndinkafikira kubanja lina la anthu okalamba omwe anali kundisamalira bwino. Kukacha, ndinkangolawirira ku ntchito ndipo ndinkafika kwathu ku Krajné Lolemba madzulo. Oľga ndi amene ankasamalira ana athu Loweruka ndi Lamlungu ine ndikachokapo.

Kenako mu 1956, ndinaikidwa kukhala woyang’anira woyendayenda ndipo ndinkachezera ndi kulimbikitsa mipingo ya m’dera lathu. Ndinavomera utumiki umenewu chifukwa oyang’anira oyendayenda ambiri anali atamangidwa. Ine ndi mkazi wanga tinali ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzasamalira banja lathu.

Malinga ndi lamulo la chikomyunizimu, munthu aliyense anafunika kukhala pantchito. Boma linkaona kuti munthu amene sali pa ntchito ndi wosokoneza ndipo ankamutsekera ku ndende. Motero sindinasiye ntchito yanga. Pamwezi, masiku a Loweruka ndi Lamlungu awiri ndinkakhala panyumba ndi banja langa kuti ndililimbikitse mwauzimu koma awiri enawo ndinkayendera mpingo umodzi m’dera langa. M’derali munali mipingo 6.

Kufalitsa Mabuku Ataletsa Ntchito Yathu

Woyang’anira woyendayenda ndi amene anali ndi udindo woonetsetsa kuti mpingo uliwonse ukulandira mabuku ofotokoza Baibulo. Poyamba, magazini tinkawalemba pamanja kapena pataipi. Kenako tinayamba kulandira zithunzi zosatsuka za masamba a magazini ya Nsanja ya Olonda n’kuzitumiza ku mipingo yosiyanasiyana. Kumeneko ankatsukitsa zithunzizo. Popeza anthu akanatha kudabwa ngati munthu atagula mapepala otsukitsira ambirimbiri, aliyense wokagula zimenezi ankachita zinthu molimba mtima komanso mosamala kwambiri.

Štefan Hučko ankaidziwa bwino ntchito imeneyi ndipo anali wakhama. Mwachitsanzo, tsiku lina Štefan anapita ku sitolo ina kumene ankagula mapepala otsukitsira zithunzi koma sanawapeze. Kenako, akuti azibwerera, anaona munthu wina wogulitsa m’sitolo amene anamulonjeza mapepala amenewa. Ndiyeno akuti azilankhula naye, Štefan anaona wapolisi akulowa m’sitoloyo. Koma wogulitsayo atangomuona Štefan anayamba kulankhula mwansangala kuti: “Bwana mwachita mwayi kwabasi. Mapepala mumawafuna kwambiri aja abwera.”

Štefan anaganiza mwamsanga n’kuyankha kuti: “Pepani mayi. Si ine ayi, mwina ndangofanana ndi munthuyo. Ine ndikungofuna pepala limodzi basi.”

Atatuluka, Štefan anangopita kukadikira pa galimoto yake ija chifukwa sanafune kubwerera opanda mapepalawo. Kenako anavula chijasi chimene anavala n’kuvulanso chipewa chake. Anachita izi kuti asamuzindikire ndipo analowanso m’sitolo ija kukakumana ndi wogulitsa uja. Atafika anati: “Ndinabwera mlungu watha ndipo munandiuza kuti mundiitanitsira mapepala. Kodi alipo?”

Wogulitsayo anayankha kuti: “Ee, alipo. Posachedwapa kunabweratu munthu wina. Koma ndiye mukufanana naye bwanji! Mungokhala ngati munabadwa mapasa.” Štefan anagula mapepalawo msangamsanga n’kunyamuka uku akuthokoza Yehova chifukwa chomuthandiza kuti apeze mapepalawo.

Cha m’ma 1980, tinayamba kugwiritsa ntchito makina apanthawiyo ochitira fotokope mapepala ndiponso posindikizira mabuku ofotokoza Baibulo m’zipinda za pansi ndiponso m’malo ena obisika. Kenako, tinayamba kupanga magazini komanso mabuku ambiri moti amakwanira Mboni zonse, penanso ena ankatsala.

Alendo Ovutitsa

Tsiku lina, mu 1960 ndinauzidwa kuti ndikaonekere kwa asilikali a m’kampani imene ndinkagwirako ntchito. Anthu atatu, ovala zovala wamba anandifunsa kuti: “Kodi unayamba liti kusonkhana ndi a Mboni za Yehova? Komanso tikufuna utiuze anzako amene umasonkhana nawo.” Mafunsowa ndinawayankha mozungulira motero anandiuza kuti andiitananso nthawi ina. Iyi inali nthawi yanga yoyamba kufunsidwa mafunso ndi apolisi ofufuza zinthu mwachinsinsi.

Posakhalitsa, anandigwira ku ntchito kuja n’kundipititsa ku siteshoni ya polisi. Kumeneko munthu wina anandipatsa pepala n’kundiuza kuti ndilembepo mayina a anzanga ena a Mboni. Munthuyo anabweranso patatha ola limodzi koma anapeza kuti sindinalembe chilichonse papepalalo ndipo ndinam’fotokozera kuti sindilembapo dzina lililonse. Zimenezi zinachitikanso patatha mlungu umodzi. Koma panthawiyi anandimenya, ndipo atandilola kuti ndizibwerera kwathu, ankangondimenya mateche mpaka kufika panja.

Izi zitachitika, anandisiya kwa chaka chathunthu. Kenaka apolisi anatumiza munthu wina kuti adzandilankhule. Kale munthuyu anali mkaidi mnzanga m’ndende zozunzirako anthu za chipani cha Nazi. Munthuyu anandiuza kuti: “Anthu inu ndinu okanika kwabasi. Timati tikatsekera m’ndende wa Mboni mmodzi, amakatuluka ali a Mboni asanu.” Boma linkafuna kuti lipeze njira inayake yosokonezera ntchito yathu. Komabe ineyo ndinatsimikiza mtima kuti zivute zitani sindingawauze chilichonse choti chiwathandize kusokoneza ntchito yathu.

Kwa zaka zambiri, ineyo ndinali mmodzi wa anthu amene apolisiwa ankawavutitsa kwambiri. Nthawi zina ankanamizira kuti ndi anzathu koma nthawi zina ankamanga winawake pa gulu lathu. Ineyo ndinachita mwayi, chifukwa sanandimangepo koma alendo apolisi aja anapitirizabe kundiyendera mpaka mu 1989, pamene boma la chikomyunizimu linatha ku Czechoslovakia.

Patatha milungu ingapo bomali lisanathe, bwana wina wamkulu wa apolisi anandipeza kuchokera ku Bratislava. Mopepesa, iye anati: “Chipanda ineyo sibwenzi apolisi atakuvutitsani choncho.” Kenaka anatulutsa mapaketi awiri a zipatso, n’kundipatsa monga mphatso.

Yehova ndi Linga Lolimba

Ngakhale kuti nditangokhala wa Mboni za Yehova, ndinatumikira kwa zaka 40 ntchito yathu ili yoletsedwa, moyo wanga wakhala wosangalatsa kwambiri. Zinthu zimene tinakumana nazo pa zaka zimenezi zinathandiza kuti tigwirizane kwambiri ndi anzathu olambira Yehova. Tinkakondana ndi kukhulupirirana kwambiri.

Mu March 2003, mkazi wanga Oľga anamwalira ndipo izi zinandikhudza kwambiri. Mkazi wangayu anali mnzanga wapamtima pa zaka zonse zimene tinakhala limodzi. Tinkachitira limodzi utumiki zaka zonsezo. Panopo ndikupitirizabe kutumikira monga mkulu mumpingo ndipo ndimayesetsabe kufunafuna anthu ofuna kumva choonadi cha m’Baibulo. Ndinamva dzina la Yehova pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, koma mpaka pano dzinali lili ngati linga lolimba kwa ineyo. *Miyambo 18:10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 33 M’bale Pavol Kovár anamwalira pa July 14, 2007, nkhaniyi ikukonzedwa. Iye anali ndi zaka 85.

[Chithunzi patsamba 12]

Mu 1942, ndili m’gulu la nkhondo la Slovak

[Chithunzi patsamba 12]

Kenako, anandiika m’ndende ya Gusen (yomwe ikuoneka kumbuyoku)

[Mawu a Chithunzi]

© ČTK

[Chithunzi patsamba 12]

Bambo anga ankatiwerengera Baibulo Lamlungu m’mawa

[Chithunzi patsamba 13]

Pa ukwati wathu mu 1946

[Chithunzi patsamba 15]

Ndili ndi Ol’ga atangotsala pang’ono kumwalira