Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tikukuthokozani Chifukwa Chokonda Kwambiri Anthu”

“Tikukuthokozani Chifukwa Chokonda Kwambiri Anthu”

“Tikukuthokozani Chifukwa Chokonda Kwambiri Anthu”

YOLEMBEDWA KU RUSSIA

▪ Mumzinda wa Chita kummawa kwa Siberia, mpingo wina wa Mboni za Yehova usanasamukire m’Nyumba ya Ufumu yatsopano, unkachitira misonkhano yachikhristu m’kalasi pasukulu inayake. Mbonizo zinkayesetsa kwambiri kuyeretsa kalasiyo, kukonza zowonongeka ndiponso zinali zokoma mtima ndi zaulemu. Poona zimenezi, akuluakulu apasukuluyi analemba kalata yoyamikira mpingowo.

M’kalatayo, iwo anati: “Tikukuthokozani chifukwa chokonda kwambiri anthu, ndipo zimenezi zimaonekera kwa munthu aliyense amene mwakumana naye. Tikuthokozanso chifukwa cha ntchito yanu yolalikira ndi yothandiza anthu m’dera lathu. Sitidzaiwala zinthu zabwino zimene taphunzira kwa inu pa zaka zonse zomwe takhalira limodzi. Zatisonyeza kuti anthu amene amakhulupirira Mulungu ndi abwino, akhama ndi okoma mtima, komanso ndi anthu ofunitsitsa kukwaniritsa zolinga zawo, achikhulupiriro ndiponso moyo wawo umakhala ndi cholinga.” Mboni za Yehova zikusangalala kumva mawu amenewa.

▪ Kumadzulo kwa mzinda wa Chita, pamtunda wa makilomita pafupifupi 5,500, woimira nthambi ya Mboni za Yehova ku Russia anaitanidwa ku mwambo wapadera umene akuluakulu a boma la St. Petersburg anakonza. Kodi anaitanidwa chifukwa chiyani? Chaka chilichonse chipale chofewa chikasungunuka, Mboni zakumeneko zimathandiza kuchotsa zinyalala zomwe zimaunjikana mu msewu wa pafupi ndi nthambi, wamakilomita 60. Posonyeza kuyamikira mtima wofuna kuthandiza anthu umenewu, mkulu wa boma anapereka satifiketi kwa woimira nthambiyo. Anthu amene anali pa mwambowu anawombera m’manja mosangalala. Chochititsa chidwi ndi chakuti mmodzi wa akuluakulu amene analankhula pa mwambowu atalephera kutchula bwino dzina la Mulungu lakuti Yehova, mwamsanga anthu ambiri pamwambowu amene si Mboni anamuwongolera, kusonyeza kuti anthuwo amadziwa bwino dzina la Mulungu ndiponso anthu amene amadziwika ndi dzinalo.

Ku Russia, Mboni za Yehova zilipo pafupifupi 150,000, ndipo n’zodziwika bwino chonchi chifukwa cha ntchito yawo yolalikira kwa anthu onse. Cholinga chawo ndi chakuti apitirize ‘kukonda kwambiri anthu,’ mwa kulalikira uthenga wolimbikitsa wa m’Baibulo kwa anthu ofuna kumva.—Mateyo 22:39.

[Chithunzi patsamba 29]

Nthambi ya ku Russia inalandira satifiketi yoyamikira