Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mukhoza Kupeza Nzeru

Mukhoza Kupeza Nzeru

“Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Palembali, mawu akuti “anauziridwa” akutanthauza kuti Mulungu wamphamvuyonse anaika maganizo ake m’mitima ya anthu amene ankalemba Baibulo.

Mulungu Akukupemphani Kuti Muzigwiritsa Ntchito Nzeru Zimene Amapereka

“Ine Yehova, ndine . . . amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo. Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga! Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje, ndipo chilungamo chanu chidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.”​—YESAYA 48:17, 18.

Muziona mawu a palembali kuti ndi zimene Mulungu akukupemphani kuchita. Iye amafuna kuti mukhale ndi mtendere wamumtima komanso muzisangalala mpaka kalekale, ndipo angakuthandizeni kupeza zinthu zimenezi.

Mukhoza Kupeza Nzeru za Mulungu

“M’mitundu yonse uthenga wabwino uyenera ulalikidwe.”​—MALIKO 13:10.

“Uthenga wabwino” ukuphatikizapo malonjezo a Yehova oti adzathetsa mavuto, adzakonza dzikoli kuti likhale labwino komanso adzaukitsa okondedwa athu amene anamwalira. A Mboni za Yehova amalalikira uthenga wa m’Baibulo umenewu padziko lonse.