Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulankhulana kuli ngati mlatho wokuthandizani kudziwa maganizo a mwana wanu

MAKOLO

5: Kulankhulana

5: Kulankhulana

ZIMENE ZIMACHITIKA

Zinthu zimayenda bwino makolo akamauza ana awo zimene akufuna komanso ngati anawo amamasuka kuuza makolo awo za mumtima mwawo.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUGANIZIRA NKHANIYI N’KOFUNIKA?

Nthawi zina makolo amavutika kulankhulana momasuka ndi ana awo achinyamata. Buku lina linanena kuti: “Ana akakhala aang’ono amauza makolo awo chilichonse. Koma akamakula samasuka kunena zimene akufuna. Choncho zimakhala zovuta kuti makolo adziwe maganizo awo.” Ngakhale zitaoneka kuti anawo sakumasuka, dziwani kuti akamakula m’pamene mumafunika kuyesetsa kwambiri kuti muzilankhula nawo.​—Breaking the Code.

ZIMENE MUNGACHITE

Muzikhala okonzeka kulankhula nawo nthawi iliyonse. Muzikhala okonzeka kukambirana ndi ana anu ngakhale utakhala usiku kwambiri.

A Lisa ananena kuti: “Nthawi zina munganene kuti, ‘Akufuna tizilankhulana nthawi ino, anali kuti tsiku lonseli?’ Palibe chifukwa chodandaulira ngati mwanayo akufuna kutilankhula. Ndipo kodi si zimene makolofe timafuna nanga?”

A Herbert ananena kuti: “Ndimagona mwamsanga. Koma nthawi zina ndimacheza ndi ana anga achinyamata mpaka pakati pa usiku. Ndimaona kuti ndi zothandiza.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.”​—1 Akorinto 10:24.

Musamalole kuti chilichonse chikusokonezeni. Bambo wina ananena kuti: “Nthawi zina ana anga akamandilankhula maganizo anga amakhala ali kwina. Amatha kuona kuti sindikuikirapo mtima.”

Ngati mumasokonezeka ndi TV kapena foni pamene mwana wanu akukulankhulani, ndi bwino kuithimitsa. Muziyesetsa kumvetsera zomwe mwana wanu akunena ndipo muzisonyeza kuti mukuchita nazo chidwi ngakhale mutaona kuti ndi zachibwanabwana.

A Maranda ananena kuti: “Tizisonyeza ana athu kuti timaona maganizo awo kukhala ofunika. Akaona kuti tilibe nazo chidwi angasiye kutiuza maganizo awo ndipo akhoza kupita kwa munthu wina kuti akawathandize.”

Anthony ananena kuti: “Musamathamangire kukalipira mwana wanu ngakhale mutaona kuti akuganiza molakwika.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Muzimvetsera mwatcheru kwambiri.”​—Luka 8:18.

Muzipeza mipata yosiyanasiyana yolankhulirana. Nthawi zina ana amamasuka kunena za mumtima mwawo mukamakambirana nawo ngati mukungocheza.

A Nicole ananena kuti: “Nthawi zina timakonza timaulendo. Ndipo zimayenda bwino tikamalankhulana kwinaku tikuyenda.”

Nthawi ya chakudya imakhalanso yabwino kwambiri kulankhulana.

A Robin ananena kuti: “Tikamadya chakudya chamadzulo, aliyense amafotokoza zomwe wakumana nazo tsiku limenelo. Zimenezi zimatithandiza kukhala ogwirizana. Ndipo aliyense akakumana ndi vuto linalake amadziwa kuti ndikafika kunyumba, anzanga akandithandiza.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, [koma] wodekha polankhula.”—Yakobo 1:19.