Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Adzachita Chiyani?

Kodi Mulungu Adzachita Chiyani?

Nthawi zambiri tikakhala ndi vuto, timayembekezera kuti mnzathu achita kenakake kuti atithandize. Ambiri akaganizira mfundo imeneyi, amaona kuti Mulungu si mnzawo chifukwa palibe chimene akuchita kuti awathandize pa mavuto awo. Komatu zoona ndi zoti Mulungu watichitira zambiri ndipo m’tsogolomu pali zimene achite kuti athetse mavuto onse. Kodi Mulungu adzachita chiyani?

ADZATHETSA ZOIPA ZONSE

Mulungu adzathetsa zoipa zonse pochotsa amene amayambitsa zoipazo. Baibulo limatiuza amene anayambitsa zoipa. Limati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) ‘Woipa’ amene akutchulidwa apa si winanso ayi, koma Satana Mdyerekezi, ndipo Yesu anamutchula kuti ndi “wolamulira wa dzikoli.” (Yohane 12:31) Satana ndi amene amachititsa kuti anthu azichita zinthu zoipa zomwe zachititsa kuti padzikoli pakhale mavuto ambiri. Kodi Mulungu adzachita chiyani?

Posachedwapa Yehova Mulungu adzagwiritsa ntchito Mwana wake Yesu Khristu kuti “awononge Mdyerekezi, amene ali ndi njira yobweretsera imfa.” (Aheberi 2:14; 1 Yohane 3:8) Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti ngakhale Mdyerekezi mwiniwakeyo amadziwa kuti “wangotsala ndi kanthawi kochepa” kuti awonongedwe. (Chivumbulutso 12:12) Mulungu adzathetsanso zoipa zonse komanso kuwononga anthu onse amene amachita zoipa.​—Salimo 37:9; Miyambo 2:22.

ADZAPANGITSA KUTI DZIKOLI LIKHALE PARADAISO

Mulungu akadzamaliza kuchotsa zoipa zonse padzikoli, adzachita zinthu zomwe zidzathandize kuti cholinga chake chokhudza anthu ndi dziko lapansi chikwaniritsidwe. Kodi tiyembekezere zotani?

Mtendere wosatha ndi chitetezo. “Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”​—Salimo 37:11.

Chakudya chamwanaalirenji komanso chopatsa thanzi. “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”​—Salimo 72:16.

Nyumba zabwino komanso ntchito yosangalatsa. “Adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. . . . Anthu anga osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo.”​—Yesaya 65:21, 22.

Kodi inuyo mukufunitsitsa kudzakhalapo pa nthawi imeneyi? Posachedwapa anthu onse adzasangalala ndi madalitso amene tatchulawa.

ADZACHOTSA MATENDA NDI IMFA

Panopa anthu onse amadwala komanso kufa. Koma zimenezi zitha posachedwapa. Mulungu adzagwiritsa ntchito dipo la Yesu “kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Kodi zotsatira zake zidzakhala zotani?

Sikudzakhala matenda. “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’ Anthu okhala mmenemo adzakhala amene machimo awo anakhululukidwa.”​—Yesaya 33:24.

Sikudzakhala imfa. “Iye adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.”​—Yesaya 25:8.

Anthu adzakhala ndi moyo kwamuyaya. “Mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”​—Aroma 6:23.

Anthu amene anamwalira adzaukitsidwa. “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15) Choncho dipo lidzathandizanso kuti anthu amene anamwalira aukitsidwe.

Kodi Mulungu adzachita bwanji zinthu zonsezi?

ADZAKHAZIKITSA BOMA LABWINO KWAMBIRI

Kuti akwaniritse cholinga chake chokhudza anthu ndi dziko lapansi, Mulungu adzagwiritsa ntchito boma lakumwamba lomwe wolamulira wake ndi Yesu Khristu. (Salimo 110:1, 2) Limeneli ndi boma kapena kuti Ufumu umene Yesu anauza otsatira ake kuti aziupempherera kuti: “Atate wathu wakumwamba, . . . Ufumu wanu ubwere.”​—Mateyu 6:9, 10.

Ufumu wa Mulungu udzalamulira padzikoli ndipo udzathetsa mavuto onse. Limeneli ndi boma labwino kwambiri ndipo anthu sangakhale ndi boma labwino kuposa limeneli. N’chifukwa chake pamene Yesu anali padzikoli, anadzipereka kwambiri kulalikira “uthenga wabwino wa ufumu” umenewu, ndipo anauza ophunzira ake kuti nawonso azichita chimodzimodzi.​—Mateyu 4:23; 24:14.

Chifukwa choti amakonda kwambiri anthu, Yehova Mulungu walonjeza kuti adzatichitira zinthu zonsezi. Kodi zimenezi sizikukuchititsani kufuna kuti mumudziwe bwino komanso mukhale naye pa ubwenzi? Nkhani yotsatira ifotokoza madalitso amene mungapeze ngati mutasankha kuchita zimenezi.

KODI MULUNGU ADZACHITA CHIYANI? Mulungu adzachotsa matenda ndi imfa, adzagwirizanitsa anthu kudzera mu Ufumu wake komanso adzakonza dzikoli kuti likhale lokongola kwambiri