Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MBIRI YA MOYO WANGA

Yehova Wakhala ‘Akuwongola Njira Zanga’

Yehova Wakhala ‘Akuwongola Njira Zanga’

NTHAWI ina, m’bale wina wachinyamata anandifunsa kuti, “Kodi ndi lemba liti limene limakusangalatsani kwambiri?” Nthawi yomweyo ndinamuyankha kuti: “Miyambo 3 vesi 5 ndi 6, lomwe limati: ‘Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.’” Kunena zoona, Yehova wawongoladi njira zanga. Kodi iye wachita bwanji zimenezi?

MAKOLO ANGA ANANDITHANDIZA KUTI NDIZIYENDA PANJIRA YOYENERA

Makolo anga anaphunzira choonadi cha m’ma 1920 ndipo pa nthawiyi anali asanakwatirane. Ineyo ndinabadwa chakumayambiriro kwa chaka cha 1939. Ndili wamng’ono tinkakhala ku England ndipo ndinkapita ndi makolo anga kumisonkhano. Kenako ndinalowa mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Mpaka pano, ndimakumbukirabe nthawi imene ndinakamba nkhani yanga yoyamba. Pa nthawiyo ndinali ndi zaka 6 ndipo ndinaima pabokosi kuti nditalikeko pang’ono n’cholinga choti ndiziona bwinobwino anthu. Ndinkachita mantha kwambiri ndikayang’ana gulu la anthu akuluakulu omwe ankamvetsera.

Ndikulalikira mumsewu limodzi ndi makolo anga

Bambo anga anandilembera pakhadi ulaliki wachidule umene ndinkagwiritsa ntchito mu utumiki. Ndili ndi zaka 8 ndi pamene ndinapita ndekha koyamba kukalalikira pakhomo la munthu. Ndinasangalala kwambiri mwininyumba atawerenga ulaliki womwe unali pakhadi langalo n’kulandira buku limene ndinamupatsa lakuti “Mulungu akhale woona.” Nthawi yomweyo ndinathamanga kukauza bambo anga. Ndinkasangalala kwambiri kupezeka pamisonkhano komanso kugwira nawo ntchito yolalikira. Zimenezi zinandithandiza kuti ndiyambe kulakalaka nditadzachita utumiki wa nthawi zonse.

Ndinayamba kukonda kwambiri mfundo za m’Baibulo bambo anga atandilembetsera kuti ndizilandira Nsanja ya Olonda. Magazini iliyonse ikangofika ndinkayamba kuiwerenga nthawi yomweyo mpaka kuimaliza. Zimenezi zinandithandiza kuti ndizikhulupirira kwambiri Yehova ndipo ndinadzipereka kwa iye.

Mu 1950, banja lathu linakapezeka pamsonkhano wakuti “Kuwonjezeka kwa Teokrase,” womwe unachitikira ku New York. Mutu wa Lachinayi pa 3 August unali wakuti: “Tsiku la Amishonale.” Patsikuli, M’bale Carey Barber yemwe anadzatumikira m’Bungwe Lolamulira ndi amene anakamba nkhani ya ubatizo. Kumapeto kwa nkhani yake, atafunsa mafunso awiri oti anthu amene amafuna kubatizidwa ayankhe, ndinaimirira nawo n’kuyankha kuti, “Inde.” Ndinali ndi zaka 11 koma ndinazindikira kuti ndachita chinthu chofunika kwambiri. Komabe ndinkaopa kulowa m’madzi chifukwa pa nthawiyo sindinkadziwa kusambira. Bambo anga aang’ono anandiperekeza kupita pamalo obatizirawo ndipo ananditsimikizira kuti zonse zikhala bwino. Ndipo sizinatengedi nthawi, moti mapazi anga sanagunde ngakhale pansi padamulo. Abale anangondilandizana, wina kundibatiza wina n’kunditulutsa m’madzimo. Kungochokera tsiku lofunika limeneli, Yehova wakhala akuwongola njira zanga.

NDINASANKHA KUKHULUPIRIRA YEHOVA

Nditamaliza sukulu ndinkafuna kuchita upainiya, koma aphunzitsi anga anandilimbikitsa kuti ndipite kuyunivesite kuti ndikachite maphunziro apamwamba. Ndinatsatira maganizo awo moti ndinapitadi kuyunivesite, koma mwamsanga ndinazindikira kuti ngati ndipitiriza maphunzirowo sindingakhale wolimba m’choonadi, choncho ndinaganiza zosiya sukuluyo. Ndinapemphera kwa Yehova za nkhaniyi ndipo ndinalembera aphunzitsi angawo kalata n’kuwafotokozera mwaulemu kuti ndisiya sukuluyo kumapeto kwa chaka choyambacho. Nthawi yomweyo ndinayamba upainiya ndipo ndinkakhulupirira kwambiri kuti Yehova andithandiza.

Ndinayamba utumiki wanthawi zonse mu July 1957 m’tawuni ya Wellingborough. Ndinapempha abale ku Beteli ya ku London kuti andipezere m’bale amene anali atachita upainiya kwa nthawi yaitali kuti ndizikatumikira naye limodzi. M’bale Bert Vaisey anandiphunzitsa zinthu zambiri, iye anali wakhama pa ntchito yolalikira ndipo anandithandiza kuti ndikhale ndi ndandanda yabwino yolowera mu utumiki. Mumpingo umene tinali munali ineyo, alongo achikulire 6 ndi M’bale Vaisey. Zimene zinandithandiza kuti ndizikhulupirira kwambiri Yehova komanso ndiziuza ena zimene ndimakhulupirira ndi kukonzekera, kuyankha komanso kukamba nkhani pamisonkhano.

Ndinamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali, ndipo nditakhala m’ndende kwa nthawi yochepa ndinatulutsidwa. Kenako ndinakumana ndi mlongo wina dzina lake Barbara, yemwe anali mpainiya wapadera. Tinakwatirana mu 1959, ndipo tinali ofunitsitsa kukatumikira kulikonse kumene angatitumize. Poyamba anatitumiza ku Lancashire, komwe ndi kumpoto chakumadzulo kwa dziko la England. Kenako mu January 1961, ndinaitanidwa kukachita nawo maphunziro a mwezi umodzi a Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku Beteli ya ku London. Pamapeto pa maphunzirowo ndinadabwa kuti anandipatsa utumiki woti ndikakhale woyang’anira dera. Kwa milungu iwiri, ine ndi Barbara tinaphunzitsidwa ndi woyang’anira dera wina waluso yemwe ankatumikira mumzinda wa Birmingham. Kenako tinapita ku utumiki wathu ndipo tinkayendera dera la Lancashire ndi Cheshire.

KUKHULUPIRIRA YEHOVA SIKUNATIGWIRITSE MWALA

Mu August 1962, tili ku tchuthi, tinalandira kalata yochokera ku ofesi ya nthambi. Mu envelopuyo munalinso mafomu a Sukulu ya Giliyadi. Titapemphera kwa Yehova, ine ndi Barbara tinalemba mafomuwa n’kuwatumiza mwamsanga ku ofesi ya nthambi. Patapita miyezi 5 tinauyamba ulendo wa ku Brooklyn ku New York, kukachita nawo maphunziro a Baibulo kwa miyezi 10, m’kalasi nambala 38 ya Sukulu ya Giliyadi.

Maphunziro a Giliyadi anatithandiza kudziwa zambiri zokhudza Mawu a Mulungu, gulu lake komanso abale ndi alongo padziko lonse. Tinali ndi zaka za m’ma 20 ndipo tinaphunzira zambiri kwa ophunzira ena omwe tinalowa nawo kalasiyo. Tsiku lililonse ndinali ndi mwayi wogwira ntchito ndi M’bale Fred Rusk, yemwe anali mmodzi wa alangizi athu. Chinthu chimodzi chimene ndinaphunzira kwa m’baleyu ndi kufunika kopereka malangizo mwachilungamo. Mobwerezabwereza iye ankanena kuti nthawi zonse malangizo ayenera kukhala ochokera m’Malemba. Ena mwa abale amene ankabwera kudzatikambira nkhani pa nthawi ya maphunziro athu anali abale a luso monga M’bale Nathan Knorr, Frederick Franz komanso Karl Klein. Ndinaphunziranso zambiri kuchokera kwa M’bale A. H. Macmillan, yemwe anali wodzichepetsa. M’baleyu anakamba nkhani imene inatithandiza kudziwa mmene Yehova anathandizira anthu ake pa nthawi yovuta kuyambira mu 1914 mpaka kumayambiriro kwa 1919.

KUSINTHA KWA UTUMIKI

Chakumapeto kwa maphunziro athu, M’bale Knorr anandiuza ine ndi Barbara kuti atitumiza ku Burundi ku Africa. Nthawi yomweyo tinathamanga kupita ku laibulale ku Beteliko kukayang’ana m’buku la pachaka kuti tione kuti ku Burundi kunali ofalitsa angati pa nthawiyo. Tinadabwa kuti sitinapeze paliponse pomwe analemba kuti m’dzikolo munali ofalitsa angati. Zinali choncho chifukwa ku Burundi kunalibe wa Mboni aliyense. Tinkachita mantha chifukwa sitinkadziwa zambiri zokhudza ku Africa. Koma titapemphera mochokera pansi pamtima, mitima yathu inakhala m’malo.

Ku utumiki wathu watsopanowu chilichonse chinali chosiyana kwambiri ndi zimene tinazolowera, kungoyambira nyengo, chikhalidwe komanso chinenero. Tsopano tinafunika kuphunzira Chifulenchi. Tinafunikanso kupeza malo okhala. Patangotha masiku awiri titafika, m’bale wina yemwe tinalowa naye kalasi imodzi dzina lake Harry Arnott, anabwera kudzationa. Iye anali akubwerera ku utumiki wake ku Zambia. M’baleyu anatithandiza kupeza nyumba, yomwe inadzakhala nyumba yoyamba ya amishonale. Koma pasanapite nthawi akuluakulu a boma omwe sankadziwa chilichonse chokhudza a Mboni za Yehova anayamba kutitsutsa kwambiri. Titangoyamba kusangalala ndi utumiki wathu akuluakulu a bomawo anabwera kudzatiuza kuti sitingapitirize kukhala m’dzikolo chifukwa tinalibe zikalata zotiloleza kugwira ntchito kumeneko. N’zomvetsa chisoni kuti tinafunika kuchoka m’dzikolo ndipo pa nthawiyi tinapita ku Uganda.

Tinkaopa kupita ku Uganda tilibe visa koma tinakhulupirira kuti Yehova atithandiza. M’bale wina wa ku Canada yemwe ankatumikira kugawo losowa ku Uganda anatithandiza ndipo analankhula ndi mmodzi wa akuluakulu a m’dipatimenti yoona za anthu olowa ndi otuluka m’dzikolo. Ndiye akuluakulu a ku maofesiwo anatilola kukhala m’dzikolo kwa miyezi ingapo pamene tinkadikirira mapepala otilola kukhala m’dzikolo. Zimene zinachitikazi zinatitsimikizira kuti Yehova ankatithandiza.

Zinthu zinali zosiyana kwambiri pa utumiki wathu ku Uganda poyerekezera ndi ku Burundi. Ntchito yolalikira inali itayamba kale ku Uganda ngakhale kuti kunali ofalitsa 28 okha. Tikamalalikira tinkapeza anthu ambiri oyankhula Chingelezi. Komabe pasanapite nthawi tinazindikira kuti, kuti tikwanitse kuthandiza anthu ambiri achidwi tinafunika kuphunzira chimodzi mwa zinenero za kumeneko. Tinayamba kulalikira ku Kampala kumene anthu ambiri ankalankhula Chiluganda, choncho tinaganiza zophunzira chinenerochi. Zinatitengera zaka zingapo kuti tichidziwe bwinobwino chinenerochi koma kuchidziwa kunatithandiza kuti tiziwafika anthu pamtima tikamalalikira. Apa tsopano tinayamba kudziwa bwino mmene tingathandizire anthu amene tinkaphunzira nawo Baibulo. Nawonso anayamba kumasuka nafe n’kumatifotokozera mmene ankamvera chifukwa cha zimene ankaphunzira.

TINAYENDA MAULENDO OSIYANASIYANA

Pamene tinkayendera madera osiyanasiyana ku Uganda

Tinkasangalala kuphunzitsa anthu choonadi ndipo chimwemwe chathu chinawonjezeka pamene tinalandira mwayi wa utumiki umene sitinkauyembekezera. Tinapemphedwa kuti tiziyendera mipingo yonse m’dzikolo. Ntchito yolalikira ku Uganda inkayang’aniridwa ndi ofesi ya nthambi ya ku Kenya. Ndiye abale ku ofesiko anatipempha kuti tifufuze madera amene kungatumizidwe apainiya apadera. Nthawi zambiri tinkakumana ndi anthu amene sanakumanepo ndi a Mboni koma ankachita nafe zinthu mokoma mtima. Ankatilandira bwino kwambiri moti nthawi zina ankatiphikira chakudya.

Kenako panapezeka ulendo winanso. Kuchokera ku Kampala ndinayenda masiku awiri pasitima ya pamtunda kukafika ku doko la Mombasa ku Kenya. Kuchoka pamenepo ndinayenda pasitima ya pamadzi kupita ku Seychelles, tizilumba timene tili pa nyanja ya Indian Ocean. Kenako kuyambira mu 1965 mpaka 1972, nthawi zambiri Barbara ankakhala nane limodzi ndikamapita ku Seychelles. Pa nthawi imeneyo kunali ofalitsa awiri okha koma kenako kunakhala kagulu ndipo n’kupita kwa nthawi kunadzakhala mpingo. Maulendo enanso omwe ndinayenda anali kupita kukaona abale ku mayiko ngati Eritrea, Ethiopia ndi Sudan.

Zinthu ku Uganda zinasintha pa nkhani za ndale asilikali atayamba kulamulira dzikolo. Kuchokera pamenepo zaka zotsatirazo zinali zovuta kwambiri koma ndinaphunzira kuti ndi bwino kutsatira malangizo akuti “perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara.” (Maliko 12:17) Pa nthawi ina anthu onse ochokera m’mayiko ena omwe ankakhala m’dzikolo anauzidwa kuti akalembetse mayina awo ku polisi yomwe anali nayo pafupi. Nthawi yomweyo tinamvera, ndiyeno patangopita masiku ochepa ine ndi mmishonale wina tikuyendetsa galimoto mumsewu wina ku Kampala, apolisi anatiimitsa. Tinachita mantha kwambiri. Iwo ankanena kuti ndife akazitape ndipo anatitengera kulikulu lawo la polisi kumene tinakafotokoza kuti ndife amishonale. Tinayesetsa kuwauza kuti tinalembetsa kale mayina athu ku polisi koma iwo sanafune kumva zimenezi. Kenako apolisiwo pamodzi ndi wapolisi wina wa mfuti anatitenga kupita nafe ku polisi yomwe inali pafupi ndi nyumba ya amishonale. Mitima yathu inakhala m’malo wapolisi wa kumeneko amene ankadziwa kuti tinalembetsa kale atatizindikira n’kuwauza anzakewo kuti atimasule.

M’masiku amenewo tinkavutika tikamadutsa m’malodiboloko, makamaka tikaimitsidwa ndi asilikali omwe aledzera. Nthawi zambiri tinkapemphera ndipo mitima yathu inkakhala m’malo akatilola kudutsa popanda kutivutitsa. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti mu 1973, amishonale onse analamulidwa kuti achoke ku Uganda.

Ndikupanga fotokope Utumiki Wathu wa Ufumu ku nthambi ya ku Côte d’Ivoire mumzinda wa Abidjan

Apanso utumiki wathu unasintha ndipo tinapita ku Côte d’Ivoire, ku West Africa. Kumenekutu kunali kusintha kwakukulu kwambiri kwa ife, tinafunika kuphunzira chikhalidwe chatsopano, kuyambiranso kulankhula Chifulenchi nthawi zonse komanso kuyamba kuzolowerana ndi amishonale ena ochokera kumayiko ena. Koma tinaonanso Yehova akutitsogolera chifukwa tikalowa mu utumiki, anthu odzichepetsa ndi a mitima yabwino sankachedwa kumvetsera uthenga wabwino. Tinaona mmene kukhulupirira Yehova kunathandizira kuti aziwongola njira zathu.

Kenako mwadzidzidzi Barbara anapezeka ndi khansa. Ngakhale kuti nthawi zambiri tinkapita kwathu n’cholinga choti akalandire thandizo, pofika mu 1983 zinali zodziwikiratu kuti sitingapitirizenso kutumikira ku Africa. Zimenezitu zinatikhumudwitsa kwambiri.

KUSINTHA KWA ZINTHU

Matenda a Barbara anakula kwambiri tikutumikira ku Beteli ya ku London ndipo patapita nthawi anamwalira. Abale ndi alongo a pa Beteli anandithandiza kwambiri. Banja lina linandithandiza kwambiri kuti ndiyambirenso kuchita bwinobwino zinthu komanso kuti ndipitirize kukhulupirira Yehova. Patapita nthawi ndinakumana ndi mlongo wina dzina lake Ann, yemwe ankachita utumiki woyendera pa Beteli. Iye anali atachitaponso upainiya wapadera ndipo ankakonda kwambiri Yehova. Mu 1989 tinakwatirana ndipo kuchokera nthawi imeneyo, takhala tikutumikira limodzi pa Beteli ya ku London.

Ndili ndi Ann ku Beteli yatsopano ku Britain

Kuchokera mu 1995 mpaka mu 2018, ndinali ndi mwayi wotumikira monga woimira likulu (yemwe poyamba ankadziwika kuti woyendera nthambi), ndipo tinayenda m’mayiko pafupifupi 60. Pa ulendo uliwonse tinkaona umboni woti Yehova amasamalira anthu ake ngakhale akumane ndi mavuto otani.

Mu 2017 tinali ndi mwayi wopitanso ku Africa. Ndinasangalala kwambiri kupita ndi Ann ku Burundi, ndipo tonse tinadabwa kuona kuchuluka kwa anthu amene anali ataphunzira choonadi pa nthawiyi. Msewu umene ndinkalalikiramo nyumba ndi nyumba nthawi imeneyo mu 1964, panopa kuli Beteli yokongola yomwe ikuthandiza ofalitsa oposa 15,500.

Ndinasangalala kwambiri nditalandira ndandanda yosonyeza mayiko amene ndinkafunika kuyendera mu 2018. Limodzi mwa mayikowo linali la Côte d’Ivoire. Nditafika ku Abidjan, womwe ndi mzinda wina waukulu m’dzikolo, ndinkangokhala ngati ndafika kwathu. Nditayang’ana kabuku ka mayina ndi manambala a foni a abale ndi alongo a pa Beteli ndinazindikira dzina la m’bale wina yemwe amakhala chipinda choyandikana ndi chathu. Dzina lake anali Sossou. Ndinakumbukira kuti m’baleyu ankatumikira monga woyendera mzinda pa nthawi imene tinali ku Abidjan. Koma ndinalakwitsa chifukwa uyu anali mwana wake, osati Iyeyo.

Yehova wakhala akukwaniritsa malonjezo ake. Pa mavuto osiyanasiyana amene ndakhala ndikukumana nawo ndaphunzirapo kuti tikamakhulupirira Yehova, iye amawongoladi njira zathu. Panopa ndife ofunitsitsa kupitirizabe kuyenda panjira yopita kumoyo wosatha m’dziko latsopano.​—Miy. 4:18.