Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 7

Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo

Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo

1-3. Kodi tonsefe ndi akapolo a chiyani, nanga Yehova adzatimasula bwanji?

TAYEREKEZANI kuti akhoti agamula kuti mukakhale m’ndende kwa moyo wanu wonse pa mlandu womwe simunapalamule. Zimene agamulazo zikusonyeza kuti simudzatuluka mpaka kalekale. Apa mungaone kuti tsogolo lanu lawonongekeratu ndipo palibe chimene mungachite kuti mudzipulumutse. Ndiye tiyerekeze kuti mwadziwa zoti pali munthu wina amene ali ndi mphamvu zoti angakumasuleni ndipo walonjeza kuti akuthandizani. Kodi mungamve bwanji?

2 Tonsefe ndi akapolo a imfa. Ngakhale titachita zotani, sitingathe kuithawa. Koma Yehova ali ndi mphamvu yoti angatimasule ku ukapolo umenewu. Iye analonjeza kuti “imfa . . . monga mdani womalizira, idzawonongedwa.”—1 Akorinto 15:26.

3 Taganizirani mmene tidzasangalalire pa nthawi imene sitidzakhalanso ndi nkhawa yoti tikhoza kumwalira. Ndipotu Yehova sikuti adzangothetsa imfa, koma adzaukitsanso anthu amene anamwalira kale. Kodi nkhani imeneyi si yosangalatsa? Yehova analonjeza kuti “anthu amene anafa” adzakhalanso ndi moyo. (Yesaya 26:19) Zimenezi ndi zomwe Baibulo limatanthauza likamanena kuti akufa adzauka.

MMENE TIMAMVERA WACHIBALE KAPENA MNZATHU AKAMWALIRA

4. (a) Kodi n’chiyani chingatilimbikitse pamene wachibale kapena mnzathu wamwalira? (b) Kodi ena mwa anzake apamtima a Yesu anali ndani?

4 Wachibale wathu kapena mnzathu akamwalira, timakhala ndi chisoni chachikulu. Timathedwa nzeru chifukwa palibe chimene tingachite kuti munthuyo akhalenso ndi moyo. Koma zimene Baibulo limanena zimatitonthoza. (Werengani 2 Akorinto 1:3, 4.) Tiyeni tikambirane chitsanzo chimodzi chimene chikusonyeza kuti Yehova ndi Yesu akufunitsitsa kuukitsa achibale athu komanso anzathu amene anamwalira. Yesu ali padziko lapansi pano ankakonda kucheza ndi Lazaro komanso azichemwali ake, Marita ndi Mariya. Anthu amenewa ankagwirizana kwambiri ndi Yesu, moti Baibulo limati: “Yesu anali kukonda onsewa, Marita ndi m’bale wake, ndiponso Lazaro.” Koma patapita nthawi Lazaro anamwalira.—Yohane 11:3-5.

5, 6. (a) Kodi Yesu anachita chiyani ataona achibale komanso anzake a Lazaro akulira? (b) N’chifukwa chiyani n’zolimbikitsa kudziwa mmene Yesu anamvera pa nkhani ya imfa?

5 Yesu anapita kuti akalimbikitse Marita ndi Mariya. Marita atamva zoti Yesu akubwera, anapita kukamuchingamira. Iye anasangalala kuti Yesu wabwera, komabe ananena kuti: “Mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalira.” Marita ankaona kuti Yesu wabwera mochedwa moti palibe chimene angachite. Kenako, Yesu ataona Mariya akulira, zinamukhudza kwambiri poona chisoni chimene anali nacho ndipo nayenso analira. (Yohane 11:21, 33, 35) Iye anali ndi chisoni chimene timakhala nacho wachibale kapena mnzathu akamwalira.

6 N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yesu amamva ngati mmene ifeyo timamvera mnzathu kapena m’bale wathu akamwalira. Ndipotu Yesu anatengera khalidwe limeneli kwa Atate ake. (Yohane 14:9) Yehova ali ndi mphamvu zothetsa imfa, ndipo aithetsa posachedwapa.

“LAZARO, TULUKA!”

7, 8. N’chifukwa chiyani Marita analetsa anthu kuti asachotse mwala umene anatsekera pamanda a Lazaro, koma kodi Yesu anachita chiyani?

7 Yesu atafika pamanda amene Lazaro anaikidwa anapeza kuti khomo lake linali litatsekedwa ndi chimwala chachikulu. Yesu anauza anthu kuti: “Chotsani chimwalachi.” Koma Marita sankafuna kuti anthu achotse mwalawo chifukwa Lazaro anali atakhala m’mandamo masiku 4. (Yohane 11:39) Iye sankadziwa zimene Yesu ankafuna kuchita.

Taganizirani mmene achibale komanso anzake a Lazaro anasangalalira ataona kuti waukitsidwa.—Yohane 11:38-44

8 Yesu anauza Lazaro kuti: “Tuluka!” Zimene Marita ndi Mariya anaona zinali zodabwitsa kwambiri chifukwa “amene anali wakufa uja anatuluka. Mapazi ndi manja ake anali okulungidwa ndi nsalu zamaliro.” (Yohane 11:43, 44) Lazaro anakhalanso ndi moyo ndipo anapitiriza kukhala ndi achibale ake komanso anzake. Iwo ankatha kumugwira komanso kulankhula naye. Zinalitu zodabwitsa kwambiri kuona Yesu ataukitsa Lazaro.

“KAMTSIKANA IWE, NDIKUNENA NDI IWE, ‘DZUKA!’”

9, 10. (a) Kodi ndi ndani anam’patsa Yesu mphamvu zoukitsira akufa? (b) Kodi nkhani za m’Baibulo za anthu amene anaukitsidwa n’zofunika bwanji?

9 Kodi Yesu ankaukitsa anthu ndi mphamvu zake? Ayi. Tikutero chifukwa asanaukitse Lazaro, iye anapemphera kwa Yehova ndipo ndi amene anam’patsa mphamvu zoukitsira Lazaro. (Werengani Yohane 11:41, 42.) Koma pali anthu enanso amene anaukitsidwa. Baibulo limanena za mtsikana wina wazaka 12 amene anadwala kwambiri. Bambo ake, a Yairo, anathedwa nzeru chifukwa mwana wawo anali yekhayu ndipo anapempha Yesu kuti amuchiritse. Yairo akulankhula ndi Yesu, anthu ena anabwera n’kumuuza kuti: “Mwana wanu uja wamwalira! Musiyeni mphunzitsiyu musamuvutitse.” Koma Yesu anauza Yairo kuti: “Usaope, ingokhala ndi chikhulupiriro basi, ndipo mwana wako apulumuka.” Kenako anapita limodzi ndi Yairo kunyumba kwake. Pamene ankayandikira kunyumbako, Yesu ayenera kuti ankamva komanso kuona anthu akulira. Iye anawauza kuti: “Tontholani, pakuti mwanayu sanamwalire ayi, koma akugona.” Makolo ake a mwanayu ayenera kuti anadabwa ndi zimene Yesu ananenazi. Yesu anauza aliyense kuti atuluke ndipo anatengana ndi makolo a mwanayo n’kupita kuchipinda kumene mwanayo anam’goneka. Iye anagwira dzanja la mwanayo n’kunena kuti: “Kamtsikana iwe, ndikunena ndi iwe, Dzuka!” Taganizirani mmene makolo ake anasangalalira ataona mwana wawoyo atadzuka n’kuyamba kuyenda. Apa Yesu anali ataukitsa mwanayo. (Maliko 5:22-24, 35-42; Luka 8:49-56) Kuchokera nthawi imeneyi, makolowo ayenera kuti ankati akaona mwana wawoyo ankakumbukira zimene Yehova anawachitira pogwiritsa ntchito Yesu. *

10 Anthu amene anaukitsidwa ndi Yesu anamwaliranso patapita nthawi. Komabe nkhani za anthu amenewa ndi zofunika kwambiri chifukwa zimatithandiza kukhulupirira kuti Yehova akufunitsitsa kuukitsa anthu ndipo palibe chimene chingamulepheretse.

ZIMENE TINGAPHUNZIRE PA NKHANI ZA ANTHU AMENE ANAUKITSIDWA

Mtumwi Petulo anaukitsa Dorika.—Machitidwe 9:36-42

Eliya anaukitsa mwana wa mzimayi wina wamasiye.—1 Mafumu 17:17-24

11. Malinga ndi zimene lemba la Mlaliki 9:5 limanena, kodi Lazaro atamwalira ankadziwa zimene zinkachitika?

11 Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti “akufa sadziwa chilichonse.” Ndi mmenenso zinalili ndi Lazaro. (Mlaliki 9:5) Monga mmene Yesu ananenera, zinali ngati ali m’tulo. (Yohane 11:11) Pa nthawi imene anali m’manda, Lazaro ‘sankadziwa chilichonse.’

12. Kodi tikudziwa bwanji kuti Lazaro anaukitsidwadi?

12 Anthu ambiri analipo pamene Yesu ankaukitsa Lazaro. Ngakhale anthu amene ankadana ndi Yesu anadziwa kuti Yesu waukitsa Lazaro. Zinthu zimenezi zimasonyeza kuti nkhani imeneyi si yongopeka. (Yohane 11:47) Komanso anthu ambiri anapita kukaona Lazaro, zomwe zinachititsa kuti ayambe kukhulupirira zoti Yesu anatumizidwa ndi Mulungu. Anthu amene ankadana ndi Yesu sanasangalale ndi zimenezi choncho anakonza zoti aphe Yesu ndi Lazaro yemwe.—Yohane 11:53; 12:9-11.

13. N’chifukwa chiyani sitikayikira zoti Yehova adzaukitsa anthu amene anamwalira?

13 Yesu ananena kuti “onse ali m’manda achikumbutso” adzaukitsidwa. (Yohane 5:28) Zimenezi zikusonyeza kuti anthu onse amene Yehova akuwakumbukira adzakhalanso ndi moyo. Koma kuti Yehova aukitse munthu, afunika kukumbukira zinthu zonse zokhudza munthuyo. Kodi angakwanitse kuchita zimenezi? Kuti tipeze yankho, taganizirani za nyenyezi zambirimbiri zimene zili kumwamba. Baibulo limanena kuti Yehova amadziwa dzina la nyenyezi iliyonse. (Werengani Yesaya 40:26.) Ngati amatha kukumbukira mayina a nyenyezi zonse, ndiye kuti akhozanso kukumbukira mosavuta chilichonse chokhudza anthu amene akufuna kudzawaukitsa. Mfundo inanso yofunika kwambiri ndi yakuti Yehova ndi amene analenga zinthu zonse, choncho ali ndi mphamvu youkitsa anthu amene anamwalira.

14, 15. Kodi zimene Yobu ananena zimatiphunzitsa chiyani pa nkhani ya kuukitsidwa kwa akufa?

14 Yobu, yemwe anali munthu wokhulupirika, ankakhulupirira kuti akufa adzauka. Iye anafunsa kuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?” Kenako anauza Yehova kuti: “Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha. Mudzalakalaka ntchito ya manja anu.” Mawu amenewa akusonyeza kuti Yobu ankadziwa kuti Yehova adzaukitsa akufa ndipo amachita kulakalaka kuti nthawi imeneyi ifike.—Yobu 14:13-15.

15 Kodi inuyo mumamva bwanji chifukwa chodziwa kuti akufa adzauka? Mwina mungamadzifunse kuti, ‘Kodi abale anga komanso anzanga amene anamwalira nawonso adzaukitsidwa?’ Zimatilimbikitsa kudziwa kuti Yehova amafunitsitsa kuukitsa anthu amene anamwalira. Tiyeni tione zimene Baibulo limanena pa nkhani ya anthu amene adzaukitsidwe komanso kumene adzakhale akadzaukitsidwa.

“ADZAMVA MAWU AKE NDIPO ADZATULUKA”

16. Kodi anthu amene adzaukitsidwe kuti akhale ndi moyo padziko lapansi adzasangalala ndi zinthu zotani?

16 Anthu amene ankaukitsidwa m’mbuyomu, ankapitiriza kukhala ndi achibale awo komanso anzawo padziko lapansi pompano. Zimenezi ndi zomwe zidzachitikenso m’tsogolomu, kungoti nthawi imeneyo zidzakhala bwino kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti anthu amene adzaukitsidwe n’kumakhala padziko lapansili, adzakhala ndi mwayi wosangalala ndi moyo mpaka kalekale ndipo sadzafanso. Dziko limene azidzakhala lidzakhala losiyana kwambiri ndi lomwe tikukhalali. Nthawi imeneyo sikudzakhala nkhondo, uchigawenga ndiponso matenda.

17. Kodi ndi ndani amene adzaukitsidwe?

17 Koma kodi ndi ndani amene adzaukitsidwe? Yesu ananena kuti “onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Lemba la Chivumbulutso 20:13 limanena kuti: “Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndi Manda zinapereka akufa amene anali mmenemo.” Zimenezi zikusonyeza kuti anthu ambirimbiri amene anamwalira adzaukitsidwa. Mtumwi Paulo ananenanso kuti “olungama ndi osalungama omwe” adzaukitsidwa. (Werengani Machitidwe 24:15.) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

M’Paradaiso, anthu amene anamwalira adzaukitsidwa n’kumakhala limodzi ndi abale awo komanso anzawo

18. Kodi anthu “olungama” amene adzaukitsidwe ndi ati?

18 “Olungama” akuphatikizapo atumiki a Yehova okhulupirika omwe anakhala ndi moyo Yesu asanabwere padziko lapansi. Anthu monga Nowa, Abulahamu, Sara, Mose, Rute ndi Esitere adzaukitsidwa kuti adzapitirize kukhala ndi moyo padzikoli. Mungawerenge zokhudza amuna ndi akazi amenewa m’chaputala 11 cha buku la Aheberi. Nanga bwanji za atumiki okhulupirika a Yehova amene akumwalira nthawi yathu ino? Nawonso ndi “olungama,” choncho adzaukitsidwa.

19. Kodi anthu “osalungama” ndi ati? Nanga Yehova adzawapatsa mwayi wotani?

19 “Osalungama” akuphatikizapo anthu ambirimbiri omwe analibe mwayi wophunzira za Yehova. Ngakhale kuti anthu amenewa anamwalira, Yehova sanawaiwale. Iye adzawaukitsa n’kuwapatsa mwayi woti amudziwe komanso kumutumikira.

20. Kodi anthu ena sadzaukitsidwa chifukwa chiyani?

20 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti munthu aliyense amene anamwalira adzaukitsidwa? Ayi. Yesu ananena kuti anthu ena sadzaukitsidwa. (Luka 12:5) Kodi ndani adzasankhe anthu oyenera kuukitsidwa? Yehova ndi amene ali Woweruza wamkulu koma waperekanso mphamvu kwa Yesu yokhala “woweruza anthu amoyo ndi akufa.” (Machitidwe 10:42) Aliyense amene angaweruzidwe kuti ndi woipa ndipo sakufuna kusintha sadzaukitsidwa.—Onani Mawu Akumapeto 19.

ENA AMAUKITSIDWA N’KUPITA KUMWAMBA

21, 22. (a) Kodi anthu amene adzaukitsidwe n’kupita kumwamba adzaukitsidwa ndi thupi lotani? (b) Kodi ndi ndani anali woyamba kuukitsidwa n’kupita kumwamba?

21 Baibulo limanenanso kuti anthu ena adzapita kukakhala kumwamba. Munthu amene wapatsidwa mwayi woti adzapite kumwamba, saukitsidwa ndi thupi lofanana ndi limene anali nalo poyamba. Anthu amene amapita kumwamba amaukitsidwa ndi thupi lauzimu.

22 Yesu ndi amene anali munthu woyamba kuukitsidwa mwanjira imeneyi. (Yohane 3:13) Patadutsa masiku atatu kuchokera pamene Yesu anaphedwa, Yehova anamuukitsa. (Salimo 16:10; Machitidwe 13:34, 35) Yesu sanaukitsidwe ndi thupi limene anali nalo ali padziko lapansi. Mtumwi Petulo anafotokoza kuti Yesu “anaphedwa m’thupi, koma anaukitsidwa monga mzimu.” (1 Petulo 3:18) Yesu anaukitsidwa ngati munthu wamphamvu wauzimu. (1 Akorinto 15:3-6) Koma Baibulo limafotokoza kuti palinso anthu ena amene adzaukitsidwe ndi thupi lotereli.

23, 24. Kodi anthu amene Yesu anawatchula kuti “kagulu ka nkhosa” ndi ndani, ndipo alipo angati?

23 Yesu asanamwalire anauza ophunzira ake okhulupirika kuti: “Ndikupita kukakukonzerani malo.” (Yohane 14:2) Zimenezi zikusonyeza kuti anthu ena okhulupirika adzaukitsidwa n’kupita kumwamba kukakhala ndi Yesu. Kodi anthu amenewa adzakhala ochuluka bwanji? Yesu ananena kuti kadzakhala “kagulu ka nkhosa,” kutanthauza kuti adzakhala ochepa. (Luka 12:32) Mtumwi Yohane anatchula chiwerengero chawo chenicheni chifukwa anaona Yesu “ataimirira [kumwamba] paphiri la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000.”—Chivumbulutso 14:1.

24 Kodi Akhristu 144,000 amenewa adzaukitsidwa liti? Baibulo limafotokoza kuti zimenezi zidzachitika Yesu akadzayamba kulamulira kumwamba. (1 Akorinto 15:23) Panopa tikukhala mu nthawi imeneyi ndipo anthu ochuluka a m’gulu limeneli anaukitsidwa kale n’kupita kumwamba. Akhristu a m’gulu limeneli omwe adakali ndi moyo panopa ngati atamwalira amaukitsidwa nthawi yomweyo n’kupita kumwamba. Komabe anthu ambiri adzaukitsidwa m’tsogolo ndipo adzasangalala ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi.

25. Kodi tidzakambirana zotani m’mutu wotsatira?

25 Posachedwapa Yehova amasula anthu ku ukapolo wa imfa ndipo imfa sidzakhalaponso mpaka kalekale. (Werengani Yesaya 25:8.) Koma kodi anthu amene adzapite kumwamba azikachita chiyani? Baibulo limanena kuti azikalamulira ndi Yesu mu Ufumu wake. Tidzakambirana zambiri zokhudza ufumu umenewu m’mutu wotsatira.

^ ndime 9 M’Baibulo muli nkhani zinanso za anthu amene anaukitsidwa. Anthu amenewa anali ana, akuluakulu, amuna, akazi, Aisiraeli komanso anthu amitundu ina. Mukhoza kuwerenga nkhani zimenezi pa 1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:32-37; 13:20, 21; Mateyu 28:5-7; Luka 7:11-17; 8:40-56; Machitidwe 9:36-42; 20:7-12.