Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Paradaiso

Paradaiso

Kodi Paradaiso n’chiyani?

ZIMENE ANTHU AMAGANIZA

Anthu ena amaganiza kuti nkhani ya Paradaiso ndi yongopeka. Ndipo ena amakhulupirira kuti ndi malo enaake omwe anthu abwino amakhalako kwamuyaya mosangalala.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Nthawi zambiri mawu akuti “paradaiso” amanena za munda wa Edeni womwe Mulungu anaikamo Adamu kuti akhalemo. (Genesis 2:7-15) Baibulo limasonyeza kuti munda umenewu unalikodi ndipo Adamu ndi Hava ankakhala mosangalala popanda matenda komanso imfa. (Genesis 1:27, 28) Koma chifukwa chakuti sanamvere Mulungu, Adamu ndi Hava anathamangitsidwa m’Paradaiso. Komabe m’Baibulo muli maulosi ambiri ofotokoza kuti m’tsogolomu, anthu adzakhalanso mosangalala m’Paradaiso.

KODI INUYO MUYENERA KUCHITA CHIYANI?

Chifukwa chakuti Mulungu ndi wachikondi, n’zomveka kunena kuti adzapatsa anthu okhulupirika moyo wosatha m’Paradaiso. Komanso Mulungu wadziwitsa anthu zimene ayenera kuchita kuti adzapeze moyo wosatha. Baibulo limanena kuti munthu ayenera kuphunzira za Yehova komanso kumvera malamulo ake kuti adzapeze moyo wosatha.—Yohane 17:3; 1 Yohane 5:3.

“Yehova Mulungu . . . anakonza munda ku Edeni, . . . ndipo m’mundamo anaikamo munthu amene anamuumbayo.”Genesis 2:8.

 Kodi Paradaiso adzakhala kuti?

ZIMENE ANTHU AMAGANIZA

Anthu ena amakhulupirira kuti Paradaiso ali kumwamba pomwe ena amanena kuti Paradaiso adzakhala padziko lapansi pompano.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Paradaiso amene anaikamo Adamu anali padziko lapansi pompano. Mulungu analenga dziko lapansi n’cholinga choti anthu adzakhalemo mpaka kalekale. Ndipo Baibulo limanena kuti Mulungu anakonza dziko lapansi kuti lidzakhalepo mpaka kalekale. (Salimo 104:5) Limanenanso kuti: “Kumwamba ndi kwa Yehova, koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.”—Salimo 115:16.

N’chifukwa chake n’zosadabwitsa kuti Baibulo limati anthu adzakhala m’Paradaiso padziko lapansi. Anthu amene adzakhalemo adzadalitsidwa ndi moyo wosatha. M’Paradaiso mudzakhala mtendere ndipo anthu azidzakhala mogwirizana. Mavuto onse adzatha ndipo anthu adzasangalala ndi zinthu zachilengedwe.—Yesaya 65:21-23.

“Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. . . .  Ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”Chivumbulutso 21:3, 4.

Kodi ndani adzakhale m’Paradaiso?

ZIMENE ANTHU AMAGANIZA

Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti anthu abwino okha ndi amene adzakhale m’Paradaiso. Koma anthu ambiri sadziwa kuti munthu wabwino ayenera kuchita chiyani. Ena amaganiza kuti munthu wabwino ndi amene amapita kutchalitchi kapena kuchita miyambo ya chipembedzo chawo basi.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limaphunzitsa kuti “olungama” adzakhala m’Paradaiso. Koma kodi ndi anthu ati amene Mulungu amawaona kuti ndi olungama? Anthu amene amangochita miyambo yachipembedzo kwinaku n’kumachita zinthu zosemphana ndi zimene Mulungu amafuna, Mulungu samawaona kuti ndi olungama. Baibulo limati: “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina kuposa kumvera mawu a Yehova? Taona! Kumvera kuposa nsembe.” (1 Samueli 15:22) Pamenepa tinganene kuti “olungama” omwe adzakhale m’Paradaiso, ndi amene amamvera malamulo a Mulungu omwe ali m’Baibulo.

ZIMENE MUNGACHITE

Pali zambiri zimene munthu ayenera kuchita kuti asonyeze kuti akumvera Mulungu, osati kungopita kutchalitchi kapena kuchita miyambo ya chipembedzo kokha basi. Zimene mumachita tsiku lililonse zingachititse kuti musangalatse Mulungu kapena ayi. Koma mukhoza kudziwa zoyenera kuchita kuti musangalatse Mulungu ngati mukuphunzira Baibulo. Ndipotu sizovuta kumusangalatsa Mulungu chifukwa Baibulo limati: “Malamulo [a Mulungu] ndi osalemetsa.” (1 Yohane 5:3) Mulungu akufunitsitsa kuti mudzakhale m’Paradaiso koma zikudalira ngati mumamvera malamulo ake.

“Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.