Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA Na. 1 2018 | Kodi Baibulo Ndi Lothandizabe Masiku Ano?

KODI BAIBULO NDI LOTHANDIZABE MASIKU ANO?

Popeza masiku ano anthu amagwiritsa ntchito kwambiri intaneti kapena njira zina zamakono pofufuza zimene akufuna, kodi Baibulo ndi lothandizabe kapena mfundo zake n’zachikale? Baibulo limanena kuti:

“Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.”​—2 Timoteyo 3:16.

Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza umboni wosonyeza kuti zimene Baibulo limanena kuti lingatithandize pa mbali iliyonse ya moyo wathu ndi zoona.

 

Kodi Malangizo a M’Baibulo ndi Othandizabe Masiku Ano?

Popeza masiku ano pamapezeka malangizo oti angolembedwa tsiku lomwelo, kodi n’kupanda nzeru kutsatira mfundo za m’Baibulo zomwe zinalembedwa zaka 2000 zapitazo?

Mfundo za M’Baibulo Sizikalamba

Zimene anthu atulukira panopa sizinachititse kuti malangizo a m’Baibulo akhale osathandiza. Malangizowa ndi ochokera pa mfundo zomwe ndi zothandiza komanso sizitha ntchito.

Kodi Ndi Lachikale Kapena Limanena Zinthu Zoti Ena Sanazitulukire?

Baibulo si buku la sayansi koma mungadabwe ndi zimene limanena pa nkhani za sayansi.

1 Lingakuthandizeni Kupewa Mavuto

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene malangizo a m’Baibulo athandizira anthu kupewa mavuto aakulu kwambiri.

2 Lingakuthandizeni Kuthetsa Mavuto

M’Baibulo muli malangizo amene angatithandize pa mavuto aakulu komanso osatherapo monga kuda nkhawa kwambiri, kuzengereza komanso kusowa wocheza naye.

3 Lingakuthandizeni Kupirira Mavuto

Nanga bwanji za mavuto oti sitingathe kuwapewa kapena kuwathetsa, monga matenda okhalitsa kapena imfa?

Baibulo Lingakuthandizeni Kuti Mukhale ndi Tsogolo Labwino

Baibulo lingatithandize kudziwa zoyenera kuchita pa mavuto amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku m’dziko loipali. Koma si zokhazi. Limafotokozanso zimene zidzachitike m’tsogolo.

Kodi Inuyo Mukuganiza Bwanji?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene ena amakhulupirira komanso yankho la Baibulo pa nkhaniyi.