Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndani Kwenikweni Amene Ali Kapolo Wokhulupirika ndi Wanzeru?”

“Ndani Kwenikweni Amene Ali Kapolo Wokhulupirika ndi Wanzeru?”

“Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo?”—MAT. 24:45.

1, 2. (a) Kodi Yesu akugwiritsa ntchito ndani potidyetsa masiku ano? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kudziwa yankho la funsoli?

MLONGO wina analemba kalata yoyamikira abale ogwira ntchito kulikulu lathu. M’kalatayo ananena kuti: “Ndisaname abale, nkhani zambirimbiri zimene mwalemba ndimazilandira pa nthawi imene ndikuzifuna kwambiri.” Kodi nanunso mumamva chimodzimodzi? Ambirife tingayankhe kuti inde ndipo zimenezi si zodabwitsa.

2 Chakudya chauzimu chimene timalandira pa nthawi yake ndi umboni wakuti Yesu, yemwe ndi Mutu wa mpingo, akukwaniritsa lonjezo lake. Koma kodi amatidyetsa kudzera mwa ndani? Pofotokoza chizindikiro cha kukhalapo kwake, Yesu ananena kuti adzagwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti apereke kwa antchito ake apakhomo “chakudya pa nthawi yoyenera.” * (Werengani Mateyu 24:45-47.) Masiku otsiriza ano, Yesu akugwiritsa ntchito kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kuti adyetse Akhristu oona. Choncho kudziwa kapolo wokhulupirikayu n’kofunika kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti popanda kapoloyu sitingakhale pa ubwenzi ndi Mulungu.—Mat. 4:4; Yoh. 17:3.

3. Kodi m’mbuyomu tinkafotokoza bwanji fanizo la kapolo wokhulupirika?

3 Kodi fanizo la Yesu lonena za kapolo wokhulupirikayu limatanthauza chiyani? M’mbuyomu, tinkafotokoza m’mabuku athu kuti pa Pentekosite mu 33 C.E., Yesu anaika kapoloyu kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo. Tinkafotokozanso kuti kapoloyu akuimira Akhristu odzozedwa onse amene ali moyo padziko pa nthawi ina iliyonse. Ndiye tinkanena kuti antchito apakhomo akuimira odzozedwa omwewo koma aliyense payekha. Tinkanenanso kuti mu 1919, Yesu anaika kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kuti “aziyang’anira zinthu zake zonse.” Zinthu zakezo tinkati zikuimira zinthu zonse zokhudza Ufumu padzikoli. Koma pambuyo pofufuza nkhaniyi mozama ndiponso kuipempherera,  taona kuti m’pofunika kusintha zimene tinkakhulupirira pa mawu a Yesu onena za kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. (Miy. 4:18) Kaya tikuyembekezera kupita kumwamba kapena kudzakhala padzikoli, fanizo limeneli limatikhudza. Choncho tiyeni tikambirane fanizoli.

NTHAWI YOTI FANIZOLI LIKWANIRITSIDWE

4-6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti fanizo la Yesu lonena za kapolo wokhulupirika linayamba kukwaniritsidwa pambuyo pa 1914?

4 Zinthu zina zimene Yesu ananena pa nthawi imene anatchula fanizoli zimasonyeza kuti linayamba kukwaniritsidwa m’masiku otsiriza osati pa Pentekosite mu 33 C.E. Tiyeni tione umboni wa m’Malemba wotsimikizira zimenezi.

5 Yesu ananena fanizo la kapolo wokhulupirika mu ulosi wake wonena za “chizindikiro cha kukhalapo [kwake] ndi cha mapeto a nthawi ino.” (Mat. 24:3) Mbali yoyamba ya ulosi wa pa Mateyu 24:4-22 inakwaniritsidwa koyamba kuchokera mu 33 C.E. kufika mu 70 C.E. Koma ikukwaniritsidwanso kachiwiri padziko lonse masiku ano. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti mawu a Yesu onena za kapolo wokhulupirika ayenera kukwaniritsidwanso kawiri? Ayi.

6 Kuyambira pa Mateyu 24:29, Yesu anayamba kufotokoza kwambiri zinthu zimene zikuchitika masiku ano. (Werengani Mateyu 24:30, 42, 44.) Pofotokoza zimene zidzachitike pa chisautso chachikulu, iye ananena kuti anthu “adzaona Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba.” Kenako anasonyeza kuti anthu okhala m’masiku otsiriza adzafunika kukhala tcheru. Iye anati: “Simukudziwa tsiku limene Ambuye wanu adzabwere.” Ananenanso kuti: “Pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzabwera.” * Ndiyeno pamene ankafotokoza zokhudza masiku otsirizazi, m’pamene ananena fanizo la kapolo wokhulupirika. Choncho mawu ake onena za kapolo wokhulupirika anayamba kukwaniritsidwa pambuyo poti masiku otsiriza ayamba mu 1914. Zimenezitu n’zomveka. N’chifukwa chiyani tikutero?

7. Kodi pamene nyengo yokolola inkayamba, panali funso liti ndipo chifukwa chiyani linalipo?

7 Ndiye taganizirani za funso lija lakuti: “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?” M’nthawi ya atumwi panalibe chifukwa chofunsira zimenezi. Monga taonera m’nkhani yapita ija, atumwi ankachita zozizwitsa komanso ankapatsa anthu mphatso za mzimu woyera. (Mac. 5:12) Umenewu unali umboni wakuti Mulungu anali kuwagwiritsa ntchito. Choncho panalibedi chifukwa choti wina azifunsa za anthu amene Yesu wasankha kuti azitsogolera. Koma si mmene zinalili mu 1914. Nyengo yokolola inayamba m’chaka chimenechi ndipo inali nthawi yoti tirigu ndi namsongole zisiyanitsidwe. (Mat. 13:36-43) Pamene nthawi yokololayi inkayamba, panali Akhristu ambiri onyenga omwe ankati akutsatira Yesu. Choncho funso linali lakuti: Kodi Akhristu odzozedwa, kapena kuti tirigu, angadziwike bwanji? Yankho lake likupezeka m’fanizo la kapolo wokhulupirika. Akhristu odzozedwa akanadziwika chifukwa chodyetsedwa bwino mwauzimu.

KODI KAPOLO WOKHULUPIRIKA NDI WANZERU NDI NDANI?

8. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Akhristu odzozedwa okha ndi amene ali m’gulu la kapolo wokhulupirika?

8 Akhristu odzozedwa padzikoli ndi amene ayenera kukhala m’gulu la kapolo wokhulupirika. Iwo amatchedwa “ansembe achifumu” ndipo apatsidwa ntchito ‘yolengeza makhalidwe abwino kwambiri a amene anawaitana kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.’ (1 Pet. 2:9) M’pake kuti anthu a m’gulu la “ansembe achifumu” amenewa, ndi amene ali ndi udindo wophunzitsa Akhristu anzawo Mawu a Mulungu.—Mal. 2:7; Chiv. 12:17.

9. Kodi odzozedwa onse ali m’gulu la kapolo wokhulupirika? Fotokozani.

9 Koma kodi ndi odzozedwa onse padzikoli amene ali m’gulu la kapolo wokhulupirika? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti si odzozedwa onse amene amagwira nawo ntchito  yopereka chakudya chauzimu kwa Akhristu padziko lonse. N’zoona kuti abale odzozedwa ena amatumikira monga akulu kapena atumiki othandiza m’mipingo yawo. Iwo amaphunzitsa kunyumba ndi nyumba komanso mu mpingo ndipo amatsatira malangizo ochokera kulikulu lathu. Koma sikuti amagwira nawo ntchito yopereka chakudya chauzimu kwa abale ndi alongo padziko lonse. Palinso alongo odzozedwa amene ndi odzichepetsa ndipo sangaganize zoyamba kuphunzitsa mu mpingo.—1 Akor. 11:3; 14:34.

10. Kodi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ndi ndani?

10 Ndiyeno kodi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ndi ndani? Pajatu Yesu amadyetsa anthu ambiri kudzera mwa anthu ochepa. Choncho m’gulu la kapoloyu muli abale odzozedwa ochepa amene amagwira nawo ntchito yokonza ndiponso yopereka chakudya chauzimu pa nthawi ino ya kukhalapo kwa Khristu. M’masiku otsiriza ano, abale odzozedwa amene ali m’gulu la kapolo wokhulupirika akhala akugwira ntchito limodzi kulikulu lathu. Masiku ano, kapoloyu akuimira abale amene ali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Komatu Yesu anangoti “kapolo” osati akapolo. Izi zikusonyeza kuti kapoloyu ndi gulu la anthu osati munthu aliyense payekha. Choncho abale a m’Bungwe Lolamulira amasankhira limodzi zinthu akakumana.

KODI ANTCHITO APAKHOMO NDI NDANI?

11, 12. (a) Kodi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ayenera kupatsidwa maudindo awiri ati? (b) Kodi ndi liti pamene Yesu anaika kapolo wokhulupirika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo? (c) Kodi Yesu anasankha ndani kuti akhale kapoloyu?

11 M’fanizo la Yesu, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru anapatsidwa maudindo awiri. Poyamba anaikidwa kuti aziyang’anira antchito apakhomo. Kachiwiri, anaikidwa kuti aziyang’anira zinthu zonse za Mbuye. Kumbukirani kuti fanizo lonseli likukwaniritsidwa m’masiku otsiriza ano. Choncho kapoloyo ayenera kuikidwa pa maudindo onse awiri m’nthawi ya kukhalapo kwa Yesu monga mfumu, yomwe inayamba mu 1914.

12 Kodi ndi liti pamene Yesu anaika kapolo wokhulupirika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo? Kuti tipeze yankho, tiyenera kuganiziranso zimene zinachitika mu 1914 pamene ntchito yokolola inayamba. Monga tanenera kale, panali magulu ambiri amene ankati ndi Akhristu. Ndiyeno funso linali lakuti: Kodi Yesu adzasankha kapolo wokhulupirikayu kuchokera m’gulu liti? Funsoli linayankhidwa pambuyo poti Yesu ndi Atate wake abwera kudzayendera kachisi, amene akuimira dongosolo lokhudza  kulambira. Paja iwo anachita zimenezi kuyambira mu 1914 mpaka chakumayambiriro kwa 1919. * (Mal. 3:1) Iwo anasangalala ndi kagulu ka Ophunzira Baibulo amene anasonyeza kuti ankakonda kwambiri Yehovayo ndiponso Mawu ake. N’zoona kuti ankafunika kusintha zinthu zina ndipo modzichepetsa analolera kuchita zimenezi pa nthawi yoyesedwa ndi kuyeretsedwa imeneyi. (Mal. 3:2-4) Ophunzira Baibulo okhulupirika amenewa analidi tirigu weniweni. Zinthu zinayamba kuyenda bwino m’chaka cha 1919. M’chakachi, Yesu anasankha abale odzozedwa oyenerera pa kagulu ka Ophunzira Baibulowa kuti akhale kapolo wokhulupirika ndi wanzeru n’kuwaika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo.

13. Kodi ndi ndani amene ali m’gulu la antchito apakhomo ndipo n’chifukwa chiyani tikutero?

13 Nanga antchito apakhomo ndi ndani? Mwachidule, ndi anthu odyetsedwa. Kumayambiriro kwa masiku otsiriza, antchito apakhomowo anali odzozedwa okhaokha. Patapita nthawi, khamu lalikulu la nkhosa zina linakhalanso m’gulu la antchito apakhomo. Masiku ano, anthu ambiri amene ali m’gulu loyang’aniridwa ndi Khristu ndi a nkhosa zina. (Yoh. 10:16) Odzozedwa ndiponso a nkhosa zina amalandira chakudya chauzimu chofanana kuchokera kwa kapolo wokhulupirika. Nanga bwanji za abale a m’Bungwe Lolamulira omwe ali m’gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru? Abale amenewa amafunikanso kudyetsedwa mwauzimu. Iwo ndi odzichepetsa ndipo amadziwa kuti a m’Bungwe Lolamulirawo aliyense payekha ali m’gulu la antchito apakhomo ngati mmene zilili ndi Akhristu onse oona.

Kaya tikuyembekezera kupita kumwamba kapena kudzakhala padzikoli, tonse ndife antchito apakhomo ndipo timafunika chakudya chauzimu chofanana

14. (a) Kodi kapolo wokhulupirika wapatsidwa udindo uti? Tchulani zinthu zimene akuyang’anira. (b) Kodi Yesu anapereka chenjezo lotani kwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru? (Onani bokosi lakuti “Ngati Kapolo Woipayo . . .”)

14 Baibulo limasonyeza kuti kale, mtumiki woyang’anira nyumba, kapena kuti kapolo wodalirika, ankayang’anira nyumba yonse ya mbuye wake. (Luka 12:42) Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wapatsidwanso udindo waukulu woyang’anira zinthu zonse za Khristu zapadzikoli. Kapoloyu akuyang’anira chuma, ntchito yolalikira ndiponso ntchito yophunzitsa pa misonkhano ikuluikulu. Akuyang’aniranso ntchito yopanga mabuku ogwiritsa ntchito polalikira, pophunzira patokha ndiponso pa misonkhano ya mpingo. Antchito apakhomo amadalira chakudya chauzimu chimene gulu la kapololi limapereka.

 NTHAWI YOTI AIKIDWE KUTI AZIYANG’ANIRA ZINTHU ZONSE ZA MBUYE

15, 16. Kodi Yesu adzaika liti kapolo wokhulupirika kuti aziyang’anira zinthu zake zonse?

15 Kodi Yesu adzaika liti kapoloyu kuti aziyang’anira “zinthu zake zonse”? Yesu ananena kuti: “Kapolo ameneyu adzakhala wodala ngati mbuye wake pobwera adzam’peza akuchita zimenezo! Ndithu ndikukuuzani, Adzamuika kuti aziyang’anira zinthu zake zonse.” (Mat. 24:46, 47) Lembali likusonyeza kuti Yesu adzaika kapoloyu pa udindo wachiwiriwu akadzabwera n’kupeza kuti “akuchita zimenezo,” kapena kuti akupereka chakudya chauzimu mokhulupirika. Izi zikusonyeza kuti payenera kudutsa nthawi kuchokera pa nthawi yomuika pa udindo woyamba kufika pa nthawi yomuika pa udindo wachiwiri. Kuti tidziwe nthawi yomuika kuti aziyang’anira zinthu zake zonse komanso mmene adzachitire zimenezi, tiyenera kudziwa zinthu ziwiri. Tiyenera kudziwa nthawi yomwe mbuye ‘adzabwere’ ndiponso tanthauzo la “zinthu zake zonse.”

16 Kodi Yesu adzabwera liti? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione malemba ena m’chaputala chomwechi. Kumbukirani kuti Yesu asananene za kubwera kwake pa nkhani ya kapoloyi anali atanena kale za ‘kubwera’ m’mavesi ena. Pa mavesi enawo ankanena za kubwera kudzaweruza dziko loipali pa nthawi ya chisautso chachikulu. * (Mat. 24:30, 42, 44) Choncho kubwera kwa Yesu kudzaika kapoloyu pa udindo wake wachiwiri, kudzachitika pa nthawi ya chisautso chachikulu yomweyo.

17. Kodi zinthu zonse za Yesu zikuphatikizapo chiyani?

17 Nanga ‘zinthu zonse za Yesu’ zikuimira chiyani? Yesu sanasonyeze kuti ‘zinthu zake zonsezo’ zikungoimira zinthu zapadziko zokha. Yesu wapatsidwanso mphamvu zambiri kumwamba. Pajatu ananena kuti: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.”  (Mat. 28:18; Aef. 1:20-23) Kuyambira mu 1914, zinthu zake zonse zikuphatikizapo Ufumu wa Mesiya ndipo adzalamulira mu Ufumuwo limodzi ndi otsatira ake odzozedwa.—Chiv. 11:15.

18. N’chifukwa chiyani Yesu adzasangalala n’kuika kapoloyu kuti aziyang’anira zinthu zake zonse?

18 Malinga ndi zimene takambiranazi, kodi Yesu adzaika liti kapoloyu kuti aziyang’anira “zinthu zake zonse”? Iye akadzabwera kudzaweruza dzikoli pa chisautso chachikulu, adzapeza kapolo wokhulupirika akupereka chakudya chauzimu pa nthawi yake kwa antchito apakhomo. Ndiyeno Yesu adzasangalala n’kuika kapoloyo pa udindo wake wachiwiri woyang’anira zinthu zake zonse. Anthu amene ali m’gulu la kapolo wokhulupirikayu adzapatsidwa udindowu pamene adzalandira mphoto yawo yolamulira limodzi ndi Khristu kumwamba.

19. Kodi kapolo wokhulupirika adzalandira mphoto yaikulu kumwamba kuposa odzozedwa ena? Fotokozani.

19 Kodi kapolo wokhulupirika adzalandira mphoto yaikulu kumwamba kuposa odzozedwa ena onse? Ayi. Anthu ochepa akalonjezedwa mphoto sizitanthauza kuti anthu ena sangailandirenso. Mwachitsanzo, taganizirani zimene Yesu anauza ophunzira ake 11 usiku woti aphedwa mawa lake. (Werengani Luka 22:28-30.) Yesu anawalonjeza kuti adzalandira mphoto yabwino kwambiri chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Iye anawauza kuti adzalamulira naye kumwamba. Koma patapita zaka zambiri, Yesu anasonyeza kuti anthu onse 144,000 adzakhala m’mipando yachifumu n’kumalamulira naye limodzi. (Chiv. 1:1; 3:21) N’chimodzimodzinso ndi lonjezo lake la pa Mateyu 24:47. Pa lembali iye analonjeza anthu ochepa amene ali m’gulu la kapolo wokhulupirika kuti adzawaika kuyang’anira zinthu zake zonse. Koma zoona zake n’zakuti anthu onse 144,000 adzayang’anira zinthu zake zonse kapena kuti adzalamulira naye limodzi kumwamba.—Chiv. 20:4, 6.

Anthu onse a 144,000 adzalamulira ndi Yesu kumwamba (Onani ndime 19)

20. (a) N’chifukwa chiyani Yesu anaika kapolo wokhulupirika? (b) Nanga inuyo mukufunitsitsa kuchita chiyani?

20 Mofanana ndi nthawi ya atumwi, Yesu akudyetsa ambiri kudzera mwa anthu ochepa. Akuchita zimenezi pogwiritsa ntchito kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Yesu anaika kapoloyu n’cholinga choti Akhristu oona, kaya akhale odzozedwa kapena a nkhosa zina, azilandira chakudya chauzimu pa nthawi yake m’masiku onse otsiriza. Tiyeni tizisonyeza kuti timayamikira zimenezi pomvera ndi mtima wonse abale odzozedwa amene ali m’gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.—Aheb. 13:7, 17.

 

^ ndime 2 Ndime 2: [1] Pa nthawi ina, Yesu anali atanena fanizo lofanana ndi limeneli. M’fanizolo, anagwiritsa ntchito mawu oti “mtumiki woyang’anira nyumba” ponena za “kapolo” ndiponso mawu oti “gulu la atumiki ake” ponena za “antchito ake apakhomo.”—Luka 12:42-44.

^ ndime 6 Ndime 6: [2] Ponena za Khristu, mawu achigiriki amene anawamasulira kuti ‘kubwera’ (er′kho·mai) ndi osiyana ndi amene anawamasulira kuti “kukhalapo” (pa·rou·si′a). Kukhalapo kwake kunayamba kale koma adzabwera kudzaweruza m’tsogolo.

^ ndime 12 Ndime 12: [3] Onani nkhani ya m’magazini ino yakuti “Dziwani Kuti Ine Ndili Pamodzi ndi Inu Masiku Onse” patsamba 10 mpaka 12, ndime 5 mpaka 8.

^ ndime 16 Ndime 16: [4] Onani nkhani ya m’magazini ino yakuti “Tiuzeni, Kodi Zinthu Zimenezi Zidzachitika Liti?” patsamba 7 ndi 8, ndime 14 mpaka 18.