Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi akulu ndi atumiki othandiza amaikidwa bwanji mumpingo?
Mtumwi Paulo anauza akulu a ku Efeso kuti: “Mukhale tcheru ndi kuyang’anira gulu lonse la nkhosa, limene mzimu woyera wakuikani pakati pawo kukhala oyang’anira, kuti muwete mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi magazi a Mwana wake weniweni.” (Mac. 20:28) Koma kodi mzimu woyera umathandiza bwanji poika akulu ndi atumiki othandiza masiku ano?
Choyamba, mzimu woyera unathandiza anthu kuti alembe m’Baibulo zimene abale ayenera kuchita kuti akhale akulu ndi atumiki othandiza. Pa 1 Timoteyo 3:1-7 pali zinthu 16 zofunika kuti munthu akhale mkulu. Zinthu zina zalembedwa pa Tito 1:5-9 ndi Yakobo 3:17, 18. Koma pa 1 Timoteyo 3:8-10, 12, 13 pali zinthu zofunika kuti munthu akhale mtumiki wothandiza. Chachiwiri, abale akamakambirana kuti aone ngati munthu akuyenerera kukhala mkulu kapena mtumiki wothandiza, amapempha Yehova kuti awapatse mzimu woyera n’cholinga choti uwatsogolere. Chachitatu, munthu amene akuikidwayo amafunika kukhala ndi makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Choncho pa zifukwa zitatuzi, tingati mzimu woyera umathandiza poika akulu ndi atumiki othandiza.
Koma kodi ndani kwenikweni amaika akulu ndi atumiki othandiza? M’mbuyomu, oyang’anira madera ankatumiza ku ofesi ya nthambi mayina a anthu amene ankaona kuti akuyenerera kukhala akulu ndi atumiki othandiza. Ndiyeno kunthambiko, abale ena osankhidwa ndi Bungwe Lolamulira ankaona mayinawo ndiponso zimene zalembedwa n’kuvomereza ngati aona kuti akuyenereradi. Ndiyeno ankalemba kalata yodziwitsa akulu mu mpingo. Zikatero, akuluwo ankakambirana ndi munthu amene wavomerezedwayo kuti adziwe ngati akufunadi kutumikira komanso ngati pali chinachake chomulepheretsa. Pomaliza, akuluwo ankalengeza kumpingo.
Koma kodi akulu ndi atumiki othandiza ankaikidwa bwanji nthawi ya atumwi? Nthawi zina atumwi ndi amene ankaika anthu pa maudindo osiyanasiyana. Mwachitsanzo, iwo ndi amene anasankha anthu 7 kuti ayang’anire ntchito yogawa chakudya kwa akazi amasiye. (Mac. 6:1-6) Koma n’kutheka kuti anthu 7 amenewa anali kale akulu pamene ankasankhidwa kuti agwire ntchitoyi.
N’zoona kuti Malemba safotokoza zonse zimene zinkachitika poika munthu aliyense pa udindo koma amafotokoza zinthu zina zimene zingatithandize kudziwa mmene zinkachitikira. Mwachitsanzo, Malemba amati pamene Paulo ndi Baranaba ankabwerera pa ulendo wawo woyamba waumishonale, ‘anaika akulu mumpingo uliwonse, ndipo atapemphera ndi kusala kudya, anawapereka kwa Yehova yemwe anamukhulupirira.’ (Mac. 14:23) Patapita zaka zingapo, Paulo anauza Tito, yemwe ankayenda naye, kuti: “Ndinakusiya ku Kerete kuti ukonze zinthu zosalongosoka ndi kuti uike akulu mumzinda uliwonse, malinga ndi malangizo amene ndinakupatsa.” (Tito 1:5) Zikuonekanso kuti Timoteyo, yemwe ankayenda ndi Paulo, anauzidwanso kuti aziika anthu pa udindo. (1 Tim. 5:22) M’malemba amene takambiranawa, oyang’anira oyendayenda ndi amene ankaika anthu pa udindo, osati atumwi ndi akulu ku Yerusalemu.
Chifukwa cha mfundo zimene takambiranazi, Bungwe Lolamulira lasintha njira yoikira akulu ndi atumiki othandiza. Kuyambira pa September 1, 2014, zimene zizichitika poika akulu ndi atumiki othandiza ndi izi: Woyang’anira dera aliyense aziona mayina a anthu amene akulu akuona kuti akuyenera kuikidwa pa udindo. Ndiyeno akafika pampingo, aziyesetsa kuwadziwa bwino anthuwo ndipo ngati n’kotheka aziyenda nawo mu utumiki. Pambuyo pokambirana ndi akulu za anthuwo, woyang’anira derayo ndi amene aziwaika pa udindo. Njira imene tafotokozayi ndi yofanana ndi imene inkatsatiridwa nthawi ya atumwi.
Koma kodi ndani amathandiza pa ntchito yoika anthu pa udindo? Choyamba, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi amene amathandiza chifukwa ali ndi udindo wodyetsa antchito apakhomo. (Mat. 24:45-47) Kuti achite zimenezi, kapoloyu amafufuza Malemba mothandizidwa ndi mzimu woyera n’kupeza mfundo zoyenera kutsatira poyendetsa gulu la Yehova. Kapolo wokhulupirikayu ndi amenenso amaika oyang’anira madera komanso abale a m’Komiti ya Nthambi. Ndiyeno ofesi ya nthambi ndi imene imaonetsetsa kuti malangizo onse ochokera kwa kapoloyu akutsatiridwa. Bungwe la akulu mumpingo uliwonse lili ndi udindo wofufuza bwinobwino Malemba n’kuona ngati anthu ena akuyenerera kukhala pa udindo mumpingo. Kenako limapereka mayina a abalewo kwa woyang’anira dera. Ndiyeno woyang’anira dera ali ndi udindo woona bwinobwino zimene akuluwo alemba zokhudza anthuwo. Iye akafufuza bwinobwino za anthuwo ndiponso kupemphera, amawaika pa udindo ngati akuyeneradi.
Kumvetsa mfundo zonsezi n’kofunika kuti tidziwe mmene mzimu woyera umathandizira poika akulu ndi atumiki othandiza. Izi zimathandiza kuti tizilemekeza ndiponso kudalira kwambiri anthu amene aikidwa pa udindo mumpingo.—Aheb. 13:7, 17.
Kodi mboni ziwiri za m’chaputala 11 cha Chivumbulutso ndi ndani?
Pa Chivumbulutso 11:3 pali ulosi wonena za mboni ziwiri zimene zidzanenera kwa masiku 1,260. Chaputala 11 chimanenanso kuti chilombo “chidzazigonjetsa ndi kuzipha.” Koma patadutsa “masiku atatu ndi hafu” mboni ziwirizi zidzaukitsidwa ndipo anthu oona zimenezi adzadabwa kwambiri.—Chiv. 11:7, 11.
Kodi mboni ziwirizi ndi ndani? Mfundo zina za m’chaputala chimenechi zingatithandize kudziwa. Choyamba, vesi 4 imanena kuti: “Mboni zimenezi zikuimiridwa ndi mitengo iwiri ya maolivi, ndi zoikapo nyale ziwiri.” Zimenezi zikutikumbutsa za choikapo nyale ndi mitengo iwiri ya maolivi zimene zatchulidwa mu ulosi wa Zekariya. Ulosiwu umanena kuti mitengo iwiri ya maoliviyi ikuimira “odzozedwa awiri” amene ‘amaimirira limodzi ndi Ambuye wa dziko lonse lapansi.’ Odzozedwa awiriwa ankaimira Zerubabele ndi Yoswa. (Zek. 4:1-3, 14) Chachiwiri, pa vesi 5 ndi 6 timamva kuti mboni ziwirizi zikuchita zinthu zina zazikulu zofanana ndi zimene Mose ndi Eliya anachita.—Yerekezerani ndi Numeri 16:1-7, 28-35 ndiponso 1 Mafumu 17:1; 18:41-45.
Kodi nkhani ya pa Chivumbulutso 11 ndi Zekariya 4:1-3, 14 ikufanana bwanji? Malemba onsewa akufotokoza za odzozedwa a Mulungu amene ankatsogolera pa nthawi yovuta. Choncho chaputala 11 cha Chivumbulutso chimanena za abale odzozedwa amene ankatsogolera pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914. Iwo analalikira kwa zaka zitatu ndi hafu ‘atavala ziguduli.’
Pambuyo pake, abale odzozedwawa anamangidwa kwa kanthawi. Apa zinali ngati aphedwa ndipo padutsa masiku atatu ndi hafu. Adani awo anasangalala kwambiri poganiza kuti ntchito ya mbonizi yatha.—Chiv. 11:8-10.
Koma malinga ndi ulosiwu, mboni ziwirizi zinaukitsidwa patadutsa masiku atatu ndi hafu. Izi zinachitika pamene abale odzozedwawo anamasulidwa kundende ndipo amene anakhalabe okhulupirika anapatsidwa udindo wapadera. Tikutero chifukwa chakuti mu 1919, Yehova anagwiritsa ntchito Yesu kuti asankhe abale kuti akhale “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” n’cholinga choti azisamalira anthu a Mulungu m’masiku otsiriza ano. Ndiyeno abale okhulupirikawa anali m’gululo.—Mat. 24:45-47; Chiv. 11:11, 12.
Chochititsa chidwi n’chakuti lemba la Chivumbulutso 11:1, 2 limanenanso za kuyeza kachisi wauzimu. Chaputala 3 cha Malaki chimanenanso za kuyendera kachisi wauzimu komanso kumuyeretsa. (Mal. 3:1-4) Kuyendera kachisi ndi kumuyeretsa kunachitika kuyambira mu 1914 mpaka chakumayambiriro kwa 1919. Nthawiyi ikuimiridwa ndi masiku 1,260 (kapena kuti miyezi 42) kuphatikiza ndi masiku atatu ndi hafu otchulidwa m’chaputala 11 cha Chivumbulutso.
Tikusangalala kwambiri kuti Yehova ‘anayeretsa anthu ake odzipereka pa ntchito zabwino.’ (Tito 2:14) Timayamikiranso chitsanzo cha abale odzozedwa amene anatsogolera pa nthawi yovutayo ndipo anali ngati mboni ziwirizo. *
^ ndime 18 Kuti mudziwe zambiri, onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2013, tsamba 22, ndime 12.