NKHANI YA PACHIKUTO | KODI BAIBULO LILI NDI UTHENGA WOTANI?
“Tapeza Mesiya”
Patadutsa zaka 400 kuchokera pamene buku lomaliza la malemba a Chiheberi linamalizidwa kulembedwa, ulosi wa Mika wonena za Mesiya unakwaniritsidwa chifukwa Yesu anabadwa ndipo anabadwira ku Betelehemu. Patapita zaka zinanso 30, mu 29 C.E., mbali yoyamba ya ulosi wa Danieli yonena za kubwera kwa Mesiya inakwaniritsidwa. Yesu anabatizidwa ndipo Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyera. Mesiya yemwe anali Mbewu komanso amene anthu ankamuyembekezera, anaonekera pa nthawi imeneyi.
Kungoyambira nthawi imeneyi, Yesu anayamba utumiki wake ‘wolengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.’ (Luka 8:1) Monga mmene maulosi ananenera, Yesu anali wachifundo ndipo ankadera nkhawa anthu ena. Mfundo zimene ankaphunzitsa zinali zothandiza komanso zosonyeza kuti anali wachikondi. Anachiritsanso anthu amene anali ndi “matenda amtundu uliwonse,” ndipo zimenezi zinasonyeza kuti ankathandizidwa ndi Mulungu. (Mateyu 4:23) Anthu amisinkhu yonse ankatsatira Yesu ndipo mumtima mwawo ankatsimikiza kuti: “Tapeza Mesiya”—Yohane 1:41.
Yesu analosera kuti Ufumu wake usanayambe kulamulira dziko lonse, padzikoli padzachitika nkhondo, zivomezi, ndiponso mavuto ena osiyanasiyana. Choncho analimbikitsa anthu onse kuti ‘akhale maso.’—Maliko 13:37.
Yesu anali munthu wangwiro ndipo nthawi zonse ankamvera Mulungu, komabe panali anthu ena amene ankadana naye omwe patapita nthawi anachititsa kuti aphedwe. Imfa yakeyi inakhala nsembe yoyenerera yomwe imatipatsanso mwayi wodzakhala ndi moyo m’Paradaiso mpaka kalekale. Izi ndi zimene Adamu ndi Hava anataya chifukwa cha kuchimwa kwawo.
Imfa ya Yesu inakwaniritsa ulosi ndipo kuukitsidwa kwake patatha masiku atatu kunakwaniritsanso ulosi wina. Ataukitsidwa, anaonekera kwa ophunzira ake oposa 500. Asanabwerere kumwamba, Yesu analamula otsatira ake kuti alalikire uthenga wabwino wonena za Ufumu wake kwa “anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 28:19) Kodi otsatira a Yesu anagwira motani ntchito imeneyi?