Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani zigawenga ankazithyola miyendo akamazipha?

Ponena za imfa ya Yesu komanso zigawenga ziwiri, zomwe zinapachikidwa pamitengo yozunzikirapo, Uthenga Wabwino wa Yohane umanena kuti Ayuda “anapempha Pilato kuti opachikidwawo awathyole miyendo ndi kutsitsa mitemboyo.”—Yohane 19:31.

Lamulo lachiyuda linkanena kuti zigawenga zikafera pamtengo wozunzikirapo, mitembo yawo ‘isamakhale pamtengopo usiku wonse.’ (Deuteronomo 21:22, 23) Aroma akagamula munthu kuti apachikidwe pamtengo, Ayuda ayenera kuti ankatsatiranso lamulo lomweli. Ankaona kuti kum’thyola munthu miyendo kunkachititsa kuti afe msanga, ndipo izi zinkapangitsa kuti aikidwe m’manda tsiku la Sabata lisanayambe.

Nthawi zambiri munthu wopachikidwayo ankam’khomerera manja ndi mapazi ake kumtengo. Kenako ankaimiritsa mtengowo, ndipo izi zinkachititsa kuti amve ululu woopsa chifukwa cha kulemera kwa thupi lake. Kuti apume, munthuyo ankakhala ngati akudzikankhira m’mwamba pogwiritsa ntchito miyendo yake. Koma akakhala kuti amuthyola miyendo, ankalephera kuchita zimenezi choncho sankachedwa kufa.

Kodi kale gulaye ankagwiritsidwa ntchito bwanji pa nkhondo?

Davide anagwiritsa ntchito gulaye kupha Goliyati, yemwe anali chiphona. Zikuoneka kuti Davide anaphunzira luso loponya gulaye ali mnyamata pa nthawi imene ankaweta nkhosa.—1 Samueli 17:40-50.

Chithunzi chosonyeza asilikali a ku siriya akugwiritsa ntchito gulaye pomenyana ndi Ayuda

Gulaye amaonekanso pa zithunzi zakale za ku Iguputo ndi za ku Siriya. Chidachi chinkapangidwa ndi chikopa kapena kansalu komwe kankaoneka ngati kathumba, ndipo kankakhala ndi zingwe ziwiri. Munthu woponya gulaye ankatenga mwala wosalala wobulungira n’kuuika pa chikopacho. Kenako ankavukuza m’mwamba gulayeyo mwamphamvu atagwira zingwe zija. Ndiyeno ankasiya chingwe chimodzi ndipo mwalawo unkafwamphuka mwamphamvu n’kukagenda chinthu chimene akufunacho.

Ofukula zinthu zakale ku Middle East anapeza miyala yambirimbiri yomwe inkaponyedwa pogwiritsa ntchito gulaye pa nkhondo. Asilikali odziwa kugwiritsa ntchito bwino gulaye ankatha kuvukuza gulaye n’kuponya mwala womwe unkathamanga paliwiro la makilomita pafupifupi 240 pa ola. Akatswiri ena amanena kuti gulaye anali wamphamvu moti ankagwiritsidwa ntchito pophera munthu kapena nyama ngati mmene uta umachitira. Koma akatswiri ena amatsutsa mfundo imeneyi. Komatu zikuoneka kuti gulaye anali woopsa kwambiri, mwinanso kuposa uta.—Oweruza 20:16.