Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Kodi n’zoona kuti Yesu anaukitsa anthu?
M’Baibulo muli nkhani zonena kuti Yesu anaukitsa anthu. Nkhani zimenezi si nthano chabe chifukwa zinachitika pamalo komanso nthawi yodziwika bwino. Mwachitsanzo, m’chaka cha 31 C.E., Yesu ndi anthu ena ankachokera ku Kaperenao kupita ku Naini. Atafika ku Naini, anakumana ndi gulu la anthu litanyamula maliro ndipo Yesu anaukitsa womwalirayo. Nkhani imeneyi si yokayikitsa, chifukwa inalembedwa m’Baibulo komanso anthu ambiri anaona zimenezi zikuchitika.—Werengani Luka 7:11-15.
Yesu anaukitsanso Lazaro, yemwe anali mnzake. Lazaroyo anali atakhala m’manda masiku 4. Nkhani imeneyinso si yokayikitsa chifukwa pamene zimenezi zinkachitika, panali anthu ambiri amene anaona.—Werengani Yohane 11:39-45.
N’chifukwa chiyani Yesu ankaukitsa anthu?
Yesu ankaukitsa anthu chifukwa anali wachifundo. Ankachitanso zimenezi pofuna kusonyeza kuti Atate wake, yemwe ndi Mlengi, anamupatsa mphamvu zoukitsira akufa.—Werengani Yohane 5:21, 28, 29.
Tikamawerenga nkhani zokhudza anthu amene Yesu anawaukitsa, zimatithandiza kukhulupirira kuti zimene iye analonjeza zidzachitikadi. Iye adzaukitsa anthu ambirimbiri, kuphatikizapo amene anamwalira asakudziwa Mulungu. Anthuwa adzapatsidwa mwayi wophunzira za Yehova yemwe ndi Mulungu wachikondi.—Werengani Machitidwe 24:15.