Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Anali mkaidi kundende ya Gaeta ku Italy, komwe abale athu ena anaikidwa m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo

9 JULY 2020
ITALY

A Mboni za Yehova ku Italy Anathandiza Kuti Akhale Ndi Ufulu Wokana Usilikali

A Mboni za Yehova ku Italy Anathandiza Kuti Akhale Ndi Ufulu Wokana Usilikali

Mofanana ndi mayiko ambiri, dziko la Italy nalonso limadziwa kuti nzika zake zili ndi ufulu wokana kugwira ntchito ya uslilikali chifukwa cha chikhulupiriro. Komabe, m’mbuyomu zinthu sizinali choncho. Dziko la Italy linayamba kuvomereza ufulu umenewu chifukwa cha zimene a Mboni za Yehova anachita.

Pambuyo pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, kwa zaka zambiri dziko la Italy linkafuna kuti amuna onse azilowa usilikali. Mu 1946, nkhondoyi itangotha kumene, ku Italy kunali a Mboni za Yehova okwana 120 okha basi. Koma anthu ambiri anayamba kudzipereka kwa Yehova ndipo kunapezeka kuti kuli achinyamata ambiri a Mboni omwe ankakana kulowa usilikali. Iwo ankachita zimenezi potsatira mfundo za m’Baibulo zokhudza kusalowerera za m’dziko, kupewa zachiwawa ndiponso kukonda anthu ena.

Kafukufuku yemwe ofesi ya nthambi ya ku Italy yapanga posachedwa akusonyeza kuti panopa pali abale osachepera 14,180 omwe anamangidwapo n’kukagwira ukaidi chifukwa chokana kulowa usilikali. Zaka zonse zimene abalewa anakhala m’ndende zikaphatikizidwa pamodzi zikukwana 9,732 ndipo ambiri anaikidwa m’ndende chakumapeto kwa zaka za m’ma 1960 kudzafika kumapeto kwa zaka za m’ma 1990.

Wolemba mbiri wina wa ku Turin, Italy dzina lake Sergio Albesano, ananena kuti a Mboni za Yehova ndi amene anali ndi “achinyamata ambiri omwe anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali.” Iye ananenanso kuti tikuthokoza kuti achinyamatawa sanasunthike pa nkhaniyi ndipo “anathandiza kuti vutoli lidziwike ndi anthu ambiri ku Italy.”

Pa nthawi imene mtsogoleri wakale wa dziko la Italy a Giulio Andreotti anali nduna yazachitetezo kuyambira mu 1959 mpaka mu 1966, anakonza zokakumana ndi a Mboni omwe anali m’ndende kuti akamvetse chifukwa chimene anakanira kulowa usilikali. Iye analemba kuti: “Ndinachita chidwi kwambiri kuti [Amboniwa] anakana kulowa usilikali chifukwa chosafuna kusiya zimene amakhulupirira m’chipembedzo chawo ndiponso kusafuna kulowerera ndale m’njira iliyonse; sikuti zinangochitika mwangozi kuti akanitsitse kulowa usilikali komanso kuti apirire moyo wam’ndende kwa zaka zonsezi.”

Lamulo loyamba lopatsa anthu ufulu wogwira ntchito zina m’malo mwa usilikali linavomerezedwa mu 1972. Komabe, ngakhale kuti lamuloli linkalola anthu kugwira ntchito zina, koma linali lidakali m’manja mwa asilikali choncho zinali zovuta kuti abale athu azilitsatira.

Kenako, pa 8 July 1998, boma la Italy linavomereza lamulo latsopano lopatsa nzika zake ufulu wogwira ntchito zina ndipo lamuloli silinalinso m’manja mwa asilikali. Choncho a Mboni za Yehova anali ndi mwayi wogwira ntchitozi. Mu August 2004, boma la Italy linapanga lamulolo lakuti amuna asamakakamizidwenso kulowa usilikali. Lamuloli linayamba kugwira ntchito mu January 2005.

Pali akatswiri ambiri azamalamulo ku Italy amene ananena kuti lamuloli lakhazikitsidwa chifukwa cha kulimba mtima kwa a Mboni za Yehova. Mmodzi wa iwo ndi Sergio Lariccia yemwenso ndi loya komanso katswiri wazamalamulo pa Sapienza University of Rome. Iye anati: “M’mbuyomu, atsogoleri achipembedzo opempherera asilikali ananena kuti kukana kulowa usilikali kunali ‘kunyoza dziko, ndipo si kogwirizana ndi lamulo lachikhristu loti tizikondana ndiponso anthu opepera okha ndi amene angachite zimenezi.’ Koma a Mboni za Yehova anathandiza kuti malamulowa asinthe komanso kuti anthu asinthe mmene ankaganizira chifukwa chosasunthika pa zimene amakhulupirira.”

Kulimba mtima kwa abale athu sikunangothandiza kuti malamulo asinthe ku Italy koma oyang’anira ndende ambiri anakhala a Mboni za Yehova poona khalidwe labwino la akaidi a Mboni. Mmodzi wa iwo ndi Giuseppe Serra, yemwe anati: “Khalidwe labwino la anyamata a Mboni linandithandiza kwambiri . . . kuyamba kuphunzira Baibulo.” Iye anabatizidwa n’kukhala wa Mboni mu 1972. (Onani bokosi lili m’munsili.)

Tikusangalala ndi zitsanzo zabwino zimene abale athu limodzi ndi mabanja awo anasonyeza ku Italy komanso padziko lonse lapansi poyesetsa kumvera lamulo lakuti sitiyenera ‘kuphunziranso nkhondo.’—Yesaya 2:4.