Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pambuyo pa chivomezi chomwe chinachitika kumpoto chakummawa kwa Japan, miyala inagumuka ku Fukushima

FEBRUARY 23, 2021
JAPAN

Chivomezi Champhamvu Zokwana 7.3 Chinawononga Kumpoto Chakummawa kwa Japan

Chivomezi Champhamvu Zokwana 7.3 Chinawononga Kumpoto Chakummawa kwa Japan

Malo

Kumpoto chakummawa kwa Japan makamaka madera a Fukushima ndi Miyagi

Ngozi yake

  • Pa 13 February 2021, chivomezi champhamvu zokwana 7.3 chinachititsa kuti magetsi azime komanso madzi asiye m’madera ena. Chivomezichi chinachitika m’madera ambiri omwe munachitikanso chivomezi champhamvu zokwana 9.0 mu 2011.

Mmene chivomezichi chinakhudzira abale ndi alongo athu

  • Ofalitsa 11 anavulala

  • Abale ambiri analibe magetsi kapena madzi kwa kanthawi

Nyumba zomwe zinawonongedwa

  • Nyumba za Ufumu 10 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba 205 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba 13 zinawonongeka kwambiri

Ntchito yothandiza anthu

  • Oyang’anira madera komanso akulu a m’madera omwe anakhudzidwa ndi chivomezichi, akuthandiza abale ndi alongo kuti apitirize kuchita zinthu zokhudza kulambira. Akuchita zimenezi potsatira njira zonse zopewera mliri wa COVID-19

  • Abale oimira Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga, komanso abale ena ongodzipereka othandiza dipatimentiyi, akufufuza kuti aone mmene nyumba zomwe zakhudzidwa zawonongekera

Tikupempha Yehova kuti apitirize kulimbikitsa anthu onse omwe akhudzidwa ndi chivomezichi.—Afilipi 4:13.