Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Mayiko Amene a Mboni za Yehova Akumangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Mayiko Amene a Mboni za Yehova Akumangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

A Mboni za Yehova amene amangidwa chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira pofika mu February 2023

DZIKO

KUMANGIDWA

CHIFUKWA

Crimea

9

  • Kuchita zinthu zokhudzana ndi chipembedzo chawo

Eritrea

20

  • Kuchita zinthu zokhudzana ndi chipembedzo chawo

  • Zifukwa zosadziwika bwinobwino

Russia

105

  • Kuchita zinthu zokhudzana ndi chipembedzo chawo

Singapore

14

  • Kukana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira

Tajikistan

1

  • Kuchita zinthu zokhudzana ndi chipembedzo chawo

Mayiko Ena

Oposa 26

  • Kuchita zinthu zokhudzana ndi chipembedzo chawo

Onse pamodzi

Oposa 175

Gawo 18 lomwe lili m’Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale a limanena kuti aliyense ali ndi “ufulu wonena maganizo ake, ufulu wotsatira zimene amakhulupirira ndiponso ufulu wopembedza.” M’mayiko ena a Mboni za Yehova akumamangidwa ndiponso kuchitidwa zinthu zankhanza kwambiri akamagwiritsa ntchito ufuluwu. A Mboni za Yehova ambiri anamangidwa chifukwa chotsatira zimene amakhulupirira. Ndipo ena akumangidwa chifukwa chokana usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

a Onaninso zimene Gawo 18 la chikalata cha mfundo za ufulu wachibadwidwe cha Universal Declaration of Human Rights limanena ndiponso Gawo 9 la chikalata chotchedwa Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Europe.