Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndingatani Ngati Makolo Anga Akuthetsa Banja?

Kodi Ndingatani Ngati Makolo Anga Akuthetsa Banja?

 Chimodzi mwa zinthu zimene zimavutitsa maganizo achinyamata ndi kutha kwa banja la makolo awo. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kupirira?

Nkhaniyi ikufotokoza

 Zinthu zitatu zimene mukuyenera kupewa

 1. Kudziimba mlandu

 “Mayi anga anandiuza kuti mavuto pakati pa iwowo ndi bambo anga anayamba nditangobadwa. Zimenezi zinandichititsa kuganiza kuti ineyo ndi amene ndinachititsa kuti banja lawo lithe.”—Diana.

 Kumbukirani izi: Makolo anu sakuthetsa banja chifukwa cha inu. Akuchita zimenezo chifukwa cha mavuto awo. Inuyo si amene munayambitsa mavutowo ndipo simungakwanitsenso kuwathetsa. Iwowo ndi amene ali ndi udindo wothetsa mavuto am’banja lawo.

 “Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.”—Agalatiya 6:5.

 2. Kusunga zifukwa

 “Ndinakwiyira kwambiri bambo anga chifukwa chokhala wosakhulupirika kwa mayi anga. Ndipo zidzakhala zovuta kuti ndiyambirenso kuwakhulupirira.”—Rianna.

 Kumbukirani izi: N’kutheka kuti munakhumudwa ndiponso kukwiya ndi zimene zinachitikira bambo ndi mayi anu, ndipo n’zomveka kutero. Koma kuwasungira zifukwa kukhoza kukuvulazani. Kungawononge thanzi lanu komanso kungachititse kuti muzivutika maganizo. N’chifukwa chake kusunga zifukwa kumayerekezedwa ndi kumwa poizoni n’kumayembekezera kuti munthu winayo adwale. a

 “Usapse mtima ndipo uzipewa kukwiya.”—Salimo 37:8.

 3. Kukayikira ngati inuyo mungadzakhale ndi banja losangalala

 “Ndimada nkhawa kuti mwina ndikhoza kudzachita zimene bambo anga anachita. Ndimaopa kuti ngati nditakwatiwa n’kukhala ndi ana, ndingadzachite zimene zinachititsa kuti banja la makolo anga lithe.”—Jessica.

 Kumbukirani izi: Kutha kwa banja la makolo anu, sikukutanthauza kuti lanunso lidzatha. Ndipotu, mukhoza kuphunzira mfundo zofunika kuchokera pa zimene zinachitikira makolo anuzo. Mwachitsanzo, mungazindikire makhalidwe amene munthu yemwe mukufuna kudzakwatirana naye angafunike kukhala nawo. Mungathenso kuona makhalidwe amene mukufunika kukhala nawo amene angachititse kuti mudzakhale mwamuna kapena mkazi wabwino.

 “Aliyense payekha ayese zochita zake.”—Agalatiya 6:4.

Kusiya kuvutika maganizo chifukwa cha kutha kwa banja la makolo anu kuli ngati kuchira fupa lanu likathyoka. Nthawi ikamapita muzisiya pang’onopang’ono kumva kupweteka

 Zinthu zitatu zimene mungachite

 1. Muzifotokozera wina. Anthu amene amangokhala osauzako ena zinthu zimene zikuwadetsa nkhawa, amachita zinthu zimene zingawononge moyo wawo monga kumwa kwambiri mowa kapena mankhwala osokoneza ubongo. M’malo mochita zimenezo, tayesani kuchita izi:

 Lankhulani ndi makolo anu. Ngati kholo limodzi kapena onse akufuna kuti mukhale mbali yawo, afotokozereni modekha koma mwamphamvu mmene zochita zawozo zikukukhudzirani. Ngati mukuona kuti simungakwanitse kuwauza zimenezi pamasom’pamaso, mukhoza kulemba kalata n’kuipereka kwa mmodzi wa iwo kapena onsewo.

 Muzifotokozera mnzanu wodalirika. Kukhala ndi munthu woti akhoza kukumvetserani kungakuthandizeni kwambiri. Baibulo limanena kuti “mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse, ndipo ndi m’bale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.”​—Miyambo 17:17.

 Muzifotokozera Mlengi wanu. Yehova Mulungu yemwe ndi “Wakumva pemphero,” amakhala wokonzeka kukumvetserani. (Salimo 65:2) Baibulo limanena kuti ‘mungamutulire nkhawa zanu zonse, chifukwa amakufunirani zabwino.’—1 Petulo 5:7.

  •   Ndi kholo liti limene mungalankhulane nalo modekha mtima uli m’malo?

  •   Ndi mnzanu wodalirika uti (wamsinkhu wanu kapena wamkulu) amene mukuona kuti angakuthandizeni?

  •   Ndi zinthu ziti zimene mungazitchule m’mapemphero anu?

 2. Muzivomereza kusintha

 Kusiyana kwa makolo anu kungachititse kuti zinthu zina zisinthe monga kokhala, sukulu imene mumaphunzira, ndalama zimene banja lanu limapeza komanso anthu ocheza nawo. Zimenezi zingakukhumudwitseni komanso kukuchititsani kukhala ndi nkhawa ndipo mungamakayikire ngati zinthu zingadzakhalenso bwino. Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muzolowere mosavuta kusinthako? Yesani kuganizira zimene mungachite kuti muzolowere moyo watsopanowo.

  •   Kodi ndi zinthu ziti zimene mungafunike kusintha kwambiri chifukwa choti banja la makolo anu latha?

  •   Kodi mungachite zinthu ziti kuti muzolowere kusinthako?

 “Ndaphunzira kukhala wokhutira ndi zimene ndili nazo posatengera mmene zinthu zilili pa moyo wanga.”—Afilipi 4:11.

 3. Muzidziwa zimene mumachita bwino

 N’zoona kuti kutha kwa banja la makolo anu kungakuchititseni kukhala ndi nkhawa, komabe kukhozanso kukuthandizani kudziwa zinthu zimene mumachita bwino. Kungakuthandizeninso kuti muyambe kuchita bwino pa zinthu zina. Jeremy, yemwe banja la makolo ake linatha ali ndi zaka 13, ananena kuti: “Kutha kwa banja la makolo anga kunawonjezera udindo wanga. Ndine mwana wamkulu m’banja lathu, choncho ndinkafunika kumathandiza kwambiri amayi komanso mng’ono wanga.”

Kutha kwa banja la makolo anu kungachititse kuti udindo wanu wosamalira ena uwonjezeke

  •   Kodi zimene zachitikira makolo anu zakuthandizani kudziwa zinthu ziti zimene mumachita bwino?

  •   Kodi mukufuna mutakhala ndi makhalidwe ati?

 “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi othandiza . . . kukonza zinthu.”—2 Timoteyo 3:16.

a Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti “Kodi Ndingatani Kuti Ndisamapse Mtima?