Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kuyelekezela Zinthu Kopindulitsa Kwambili

Kuyelekezela Zinthu Kopindulitsa Kwambili

KODI ndinu Mkhiristu? Ngati n’conco, ndinu mmodzi mwa anthu oposa 2 biliyoni pa dziko lapansi amene amakamba kuti ndi Akhiristu. Ciŵelengelo cimeneci cionetsa kuti pafupifupi munthu mmodzi pa atatu aliwonse amakamba kuti ndi otsatila a Khiristu. Masiku ano, pali machechi ambili amene amati ndi Acikhiristu. Koma machechi amenewa ni ogaŵikana kaamba ka kusiyana pa zimene amakhulupilila, ndi mmene amaonela zinthu. Conco, zimene mumakhulupilila zingakhale zosiyana kwambili ndi za anthu ena amene amati ni Akhiristu. Kodi zimene inu mumakhulupilila n’zofunika kwenikweni? Inde, malinga ngati mufuna kucita zimene Baibulo imaphunzitsa.

Otsatila oyambilila a Yesu Khiristu, anali kudziŵika ndi dzina lakuti “Akhiristu.” (Machitidwe 11:26) Iwo sanali kufunikila dzina lina lapadela cifukwa Akhiristu onse anali ndi cikhulupililo cimodzi. Akhiristu onse anali kutsatila zimene Yesu Khiristu, Woyambitsa Cikhiristu, anali kuphunzitsa. Nanga bwanji chechi yanu? Kodi mukhulupilila kuti zimene imaphunzitsa n’zimene Khiristu anali kuphunzitsa, ndiponso n’zimene otsatila ake oyambilila anali kukhulupilila? Kodi mungadziŵe bwanji kuti n’zoona? Njila yokha imene mungadziŵile, ndi kuseŵenzetsa Baibulo.

Dziŵani izi: Yesu Khiristu anali kulemekeza kwambili Malemba. Anali kuwaona kuti ni Mawu a Mulungu. Sanali kukondwela ndi anthu amene anali kupeputsa zimene Baibulo imaphunzitsa mwa kulemekeza miyambo ya anthu. (Maliko 7:9-13) Conco, tingakambe motsimikiza kuti otsatila oona a Yesu akhulupilila zimene Baibulo imakamba. Cotelo, Mkhiristu aliyense ayenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene chechi yanga imaphunzitsa zigwilizana ndi zimene Baibulo imakamba?’ Kuti mupeze yankho, muyenela kuyelekezela zimene chechi yanu imaphunzitsa ndi zimene Baibulo imakamba.

Yesu anakamba kuti tiyenela kulambila Mulungu m’coonadi. Coonadi cimeneci cipezeka m’Baibulo. (Yohane 4:24; 17:17) Ndipo mtumwi Paulo anakamba kuti ngati tifuna kukapulumuka tiyenela ‘kudziŵa coonadi molondola.’ (1 Timoteyo 2:4) Motelo, zimene timakhulupilila zifunika kukhala zogwilizana ndi coonadi ca m’Baibulo. N’cifukwa ciani? Cifukwa ngati munthu sakhulupilila zimene Baibulo imaphunzitsa sangapulumuke.

MMENE MUNGAYELEKEZELE ZIMENE MUMAKHULUPILILA NDI ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA

Tikupemphani kuŵelenga mafunso 6 amene ali m’nkhani ino, n’kuona mmene Baibulo iyankhila mafunso amenewa. Onani mau ocokela m’Baibulo, ndi kuganizila mayankho amene apelekedwa. Ndiyeno, dzifunseni kuti, ‘Kodi zimene chechi yanga imaphunzitsa zigwilizana ndi zimene Baibulo ikamba?’

Mafunso aŵa ndi mayankho ake angakuthandizeni kuyelekezela zimene mumaphunzila ku chechi kwanu na zimene Baibulo imaphunzitsa. Kucita izi n’kofunika kwambili. Kodi mungakonde kudziŵa zinthu zina zimene Baibulo imakamba ndi kuziyelekezela na zimene mumaphunzila kuchechi kwanu? A Mboni za Yehova angakuthandizeni kudziŵa bwino coonadi ca m’Baibulo. Mungapemphe wa Mboni kuti aziphunzila nanu Baibulo kwaulele. Mungapitenso pa webusaiti yathu ya, jw.org.