Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Zidzatheka Kukhala m’Dziko Lopanda Nkhanza?

Kodi Zidzatheka Kukhala m’Dziko Lopanda Nkhanza?

Kodi inu kapena munthu wina wa m’banja lanu anacitilidwapo nkhanza? Kodi mumaopa kuti mungadzacitilidwe nkhanza mtsogolo? Nkhanza ili ngati matenda oopsa amene akufalikila pa dziko lonse. Onani zitsanzo izi.

NKHANZA ZA PANYUMBA NDI KUGONEDWA MWACIKAKAMIZO: “Mkazi mmodzi pa akazi atatu aliwonse, anacitidwapo nkhanza ya panyumba kapena kugwililidwa ndi mnzake wa pamtima nthawi ina pa umoyo wake.” Inatelo lipoti ya United Nations. Inanenanso kuti, “mtsogolomu zioneka kuti padziko lonse, mmodzi pa akazi 5 adzakakamizidwa kugonedwa.”

UCIFWAMBA: Lipoti ionetsa kuti zigaŵenga zoposa 30,000 zimavutitsa anthu ku United States. Ku Latin America, pafupifupi munthu mmodzi pa anthu atatu aliwonse, anakamba kuti anacitidwapo za ucifwamba.

KUPHANA: Zioneka kuti anthu pafupifupi 500,000 amene anaphedwa m’caka ca 2012, anali oculuka kuposa amene anafa pa nkhondo. Kum’mwela kwa Africa ndi ku Central America, ndi kumene kunaphedwa anthu ambili (anthu 30 pa anthu 100, 000 aliwonse ku Southern Africa, ndi anthu 26 pa anthu 100, 000 ku Central America.) M’caka cimodzi cabe, anthu oposa 100,000 anaphedwa ku Latin America, ndipo anthu pafupifupi 50,000 anaphedwa ku Brazil kokha. Kodi pangakhale njila yothetsela nkhanza imeneyi?

KODI NKHANZA INGATHE?

N’cifukwa ciani nkhanza ni yofala? N’zinthu zambili zimene zimapangitsa anthu kucita nkhanza. Zina mwa izo ndi: Kusiyana kwa maumunthu ndi vuto la zandalama, ana kuona acikulile akucita zinthu zankhanza, ucidakwa, kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza ubongo, kusaŵelengela moyo wa ena, ndi kusalanga anthu amene amacita za nkhanza.

Komabe, anthu m’mbali zina za dzikoli akuyesetsa kuthetsa nkhanza. Mwacitsanzo, mzinda wa São Paulo, ku Brazil uli ndi anthu ambili. Koma kunacoka lipoti lakuti kupha anthu kwacepekela ndi 80 pelesenti m’zaka 10 zapita. Ngakhale n’telo, nkhanza za mtundu uliwonse zikucitikabe mumzinda umenewo. Ndipo anthu 10 pa anthu 100,000 aliwonse okhala kumeneko, amaphedwa. Nanga n’ciani cingathandize kuti nkhanza itheletu?

Kuti nkhanza itheletu cidalila pa maganizo a anthu ndi khalidwe lawo. Kuti anthu a nkhanza asinthe, afunika kuleka kukhala onyada, aumbombo, ndi odzikonda. M’malomwake, afunika kukhala acikondi, aulemu, ndi oganizila ena.

N’ciani cingathandize munthu kuti asinthe? Onani zimene Baibulo imaphunzitsa:

  • “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake.”—1 Yohane 5:3.

  • “Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.” *Miyambo 8:13.

Kukonda Mulungu ndi kuopa kum’khumudwitsa, kungathandize anthu ankhanza kusintha umoyo wao, osati mwaciphamaso, koma kusinthilatu umunthu wawo. Kodi zimenezi zimacitikadi? Inde.

Mwacitsanzo, Alex  * anamangidwa m’ndende ya ku Brazil kwa zaka 19 kaamba ka nkhanza. Iye anayamba kuphunzila Baibulo na Mboni za Yehova. Ndipo m’caka ca 2000, anakhala wa Mboni za Yehova. Kodi iye analekadi khalidwe lake lankhanza? Inde, anasinthadi ndipo amadziimba mlandu akaganizila zoipa zimene anali kucita. Iye anakamba kuti: “Nimayamikila kwambili Mulungu cifukwa cakuti ananikhululukila. Kuyamikila Yehova ndi kum’konda, kwanithandiza kuti nileke kucita zankhanza.”

César amene amakhala ku Brazil, anali kawalala wa mfuti. Kwa zaka 15, iye anali kuba. Koma analeka. N’ciani cinamupangitsa kuleka? Ali m’ndende anakamba ndi Mboni za Yehova ndipo anayamba kuphunzila Baibulo. César anakamba kuti: “Kwa nthawi yoyamba, n’nadziŵa colinga ca moyo. Conco, n’nayamba kukonda Mulungu ndi kumuopa. N’nali kuopa kucita zinthu zoipa poganiza kuti ningakhumudwitse Yehova. Sin’nafune kuti nioneke ngati munthu wosayamikila pa kukoma mtima kumene Mulungu wanionetsa. Cikondi ndi kuopa Mulungu zinan’thandiza kuti nisinthe.”

Phunzilani zimene mungacite kuti mudzakhale m’dziko lopanda nkhanza

Kodi zocitika zimenezi zitiphunzitsa ciani? Zitiphunzitsa kuti Baibulo ili ndi mphamvu zotha kusintha anthu; inde, kusintha kaganizidwe kawo. (Aefeso 4:23) Alex, amene tamuchula poyamba anakambanso kuti: “Zimene n’nali kuphunzila m’Baibulo zinali monga madzi oyela amene anali kucotsa litsilo langa. Maganizo anga oipa anayamba kucoka pang’ono-pang’ono. N’nali kuganiza kuti zinthu zoipa zimene n’nali kucita sinidzakwanitsa kuzileka.” Kukamba zoona, uthenga woyela wocokela m’Baibulo ukadzala m’maganizo athu, ukhoza kutiyeletsa ndi kucotselatu zoipa zonse. Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu yotha kuyeletsa munthu. (Aefeso 5:26) Ngati anthu ankhanza ndi odzikonda aphunzila Baibulo, angasinthe n’kukhala okoma mtima ndi amtendele. (Aroma 12:18) Akamatsatila mfundo za m’Baibulo, amakhala ndi umoyo wacimwemwe.—Yesaya 48:18.

Anthu oposa 8 miliyoni a Mboni za Yehova, ocokela m’maiko oposa 240, apeza njila yabwino yothetsela nkhanza. Iwo acokela m’mitundu yosiyanasiyana, m’maiko osiyanasiyana, ndipo aphunzila kukonda ndi kuopa Mulungu. Amakondana kwambili ndipo amakhala mwamtendele monga banja la pa dziko lonse. (1 Petulo 4:8) Citsanzo cawo cawonetsa kuti n’zotheka kukhala m’dziko limene mulibe nkhanza.

DZIKO LOPANDA NKHANZA LILI PAFUPI

Baibulo imalonjeza kuti posacedwa Mulungu adzayeletsa dziko lino lankhanza. Nkhanza zimene zilipo masiku ano pa dziko lapansi zidzathelatu pa “tsiku laciweluzo ndi ciwonongeko ca anthu osaopa Mulungu.” (2 Petulo 3:5-7) Anthu ankhanza sadzavutitsanso ena. Tingatsimikize bwanji kuti Mulungu afuna kuthetselatu nkhanza?

Baibulo imakamba kuti, “Mulungu amadana kwambili ndi aliyense wokonda ciwawa.” (Salimo 11:5) Mlengi amakonda mtendele ndi cilungamo. (Salimo 33:5; 37:28) N’cifukwa cake sangalole anthu ankhanza kukhalapo mpaka kalekale.

Ndithudi, dziko lamtendele likubwela. (Salimo 37:11; 72:14) Kodi simungafune kudziŵa zimene mungacite kuti muyenelele kudzakhala m’dziko lopanda nkhanza?

^ par. 14 Maina tawasintha.