Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

N’nalola Yehova Kunitsogolela Njila

N’nalola Yehova Kunitsogolela Njila

NILI mnyamata, n’nasankha nchito yakuthupi imene n’nali kuikonda kwambili. Koma Yehova ananipempha kucita nchito ina yosiyana na imeneyo. Ndipo zinali monga iye akuniuza kuti: “Ndidzakupatsa nzelu ndi kukulangiza njila yoti uyendemo.” (Sal. 32:8) Kulola Yehova kunitsogolela njila kwanipatsa mwayi wocita mautumiki ambili auzimu na madalitso, kuphatikizapo kutumikila ku Africa zaka 52.

KUCOKA KU DELA LOCHEDWA BLACK COUNTRY KUPITA KU MALAWI

N’nabadwa mu 1935 ku tauni ya Darlaston, m’dela la Black Country ku England. Dela limeneli linadziŵika na dzinali cifukwa ca utsi wakuda wocokela m’mafakitale umene unali paliponse. Pamene n’nali na zaka pafupi-fupi zinayi, makolo anga anayamba kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova. N’tafika zaka pafupifupi 14, n’nakhutila kuti ici ndico coonadi, ndipo n’nabatizika mu 1952 nili na zaka 16.

Panthawiyo, n’nali n’tayamba kuphunzila nchito pa kampani yaikulu yopanga zida zogwilitsa nchito komanso zitsulo za motoka. N’nayamba kuphunzila nchito ya ukalembela pa kampaniyo, ndipo n’naikonda kwambili.

N’nafunika kupanga cisankho cofunika kwambili pamene woyang’anila dela, ananipempha kuti nizitsogoza Phunzilo la Buku la Mpingo mu mpingo wathu wa Willenhall. Koma n’nagwila njakata. Pa nthawiyo, n’nali kusonkhana ku mipingo iŵili. Pa msonkhano wa mkati mwa mlungu, n’nali kusonkhana na mpingo wa Bromsgrove umene unali kufupi na kunchito, ndipo unali pa mtunda wa makilomita 32. Koma nikapita kunyumba kwa makolo kumapeto kwa mlungu, n’nali kusonkhana na mpingo wa Willenhall.

Pofuna kuthandizila gulu la Yehova, n’navomela pempho la woyang’anila dela, ngakhale kuti kucita zimenezo kunafuna kuti nileke nchito imene n’nali kuikonda kwambili. Kulola Yehova kunitsogolela njila pa nthawiyo, kunatsegula khomo limene sin’nadzigwilitse nalo mwala.

Pamene n’nali kusonkhana na mpingo wa Bromsgrove, n’nakumana na mlongo wauzimu komanso ciphadzuŵa, dzina lake Anne. Tinakwatilana mu 1957, ndipo capamodzi tinakhala na mwayi wocita upainiya wanthawi zonse, upainiya wapadela, nchito ya m’cigawo, na kutumikila pa Beteli. Anne wakhala akunipatsa cimwemwe mu umoyo wanga wonse.

Mu 1966, tinakondwela kwambili kukaloŵa sukulu ya Giliyadi ya kalasi nambala 42. Titatsiliza maphunzilowo, anatitumiza ku Malawi, dziko limene anthu ake amadziŵika kuti ni okoma mtima komanso olandila alendo. Koma sitinadziŵe kuti kumeneko tidzangokhalako nthawi yocepa.

KUTUMIKILA PA NTHAWI YA MGWEDE-GWEDE KU MALAWI

Motoka ya mtundu wa Jeep imene tinali kugwilitsa nchito ku Malawi m’nchito ya cigawo

Tinafika ku Malawi pa February 1, 1967. Titalimbana na kuphunzila cinenelo kwa mwezi umodzi, tinayamba utumiki monga woyang’anila cigawo. Tinali kugwilitsa nchito motoka ya mtundu wa Jeep, imene ena anali kuiganizila kuti imadutsa paliponse, ngakhale pa mitsinje. Koma zimenezo sizinali zoona. Tinali kungodutsa cabe pa madzi ocepa. Nthawi zina, tinali kukhala m’nyumba zaudzu, ndipo tinali kuika tenti pa mtenje m’nyengo ya mvula kuti zisamadonthe. Kuyamba umishonale na umoyo wovuta umenewu kunali kosasangalatsa, koma tinaukonda.

Mu April, n’nazindikila kuti boma posacedwa lidzayamba kuvutitsa Mboni. N’namva pulezidenti wa Malawi, Dr. Hastings Banda, akulankhula pa wailesi. Iye anakamba kuti Mboni za Yehova sizikhoma misonkho, komanso kuti akubweletsa mavuto ku boma. Koma zinenezo zimenezo sizinali zoona. Tonse tinadziŵa kuti nkhani yagona pa kusakhalila mbali m’ndale, maka-makanso cifukwa cokana kugula makadi a cipani candale.

Pofika mu September, tinaŵelenga nkhani m’nyuzipepala yoonetsa kuti pulezidenti anaimba mlandu abale wakuti akubweletsa msokonezo m’dzikolo. Pa msonkhano wina wandale, iye analengeza kuti mwamsanga adzatseka nchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo. Ciletso cimeneci cinayamba kugwila nchito pa October 20, 1967. Posakhalitsa, apolisi komanso a imigileshoni anafika pa ofesi ya nthambi n’kuitseka. Ndipo anauza amishonale kuti acoke m’dzikolo.

Apolisi atatigwila na kutipitikitsa m’Malawi mu 1967, pamodzi na amishonale anzathu Jack na Linda Johansson

Pambuyo pokhala m’maselo masiku atatu, anatipitikitsa m’dzikolo ndipo tinatumizidwa ku Mauritius—dziko lolamulidwa na Britain. Koma boma la Mauritius silinatilole kukhala m’dzikolo monga amishonale. Conco tinatumizidwa ku Rhodesia (imene tsopano amati Zimbabwe). Titafika, tinapeza wa imigileshoni wouma mtima amene anakana kuti tikhale m’dzikolo. Inati: “Ku Malawi anakupitikitsani. Nakonso ku Mauritius sanakuloleni kukhala, ndiye mwaona kuti kuno ndiko kwakupusilani eti!” Anne atamva zimenezi anayamba kulila. Zinaoneka monga palibe amene anali kutifuna. Zitafika pamenepo, tinaganiza zongobwelela kwathu ku England. Potsilizila pake, boma linalola kuti tigoneko usiku umodzi pa ofesi ya nthambi. Koma anatiuza kuti tikaonekele ku likulu lawo tsiku lotsatila. Izi tinali titatopa nazo, koma tinangosiya zonse m’manja mwa Yehova. Tsiku lotsatila masana, mosayembekezela tinalandila cilolezo cakuti tingakhale monga alendo ku Zimbabwe. Sinidzaiŵala mmene n’namvela pa tsikulo. N’natsimikizila kuti Yehova anali kutitsogolela njila.

UTUMIKI WATSOPANO—KUCOKA KU ZIMBABWE KUKATUMIKILA KU MALAWI

Ine na mkazi wanga Anne pa Beteli ya Zimbabwe, mu 1968

Pa ofesi ya nthambi ya Zimbabwe, n’nali kuseŵenzela ku Service Department, ndipo n’nali kugwilila nchito pa za ku Malawi na ku Mozambique. Abale ku Malawi anali kuzunzidwa koopsa. Nchito yanga inaphatikizaponso kumasulila malipoti amene oyang’anila madela ku Malawi anali kutumiza. Usiku wina nikugwilila nchito pa lipoti, n’nalila n’taŵelenga mmene abale na alongo ku Malawi anali kucitilidwa nkhanza. * Koma n’nalimbikitsidwa kwambili poona kukhulupilika kwawo na kupilila kwawo.—2 Akor. 6:4, 5.

Tinacita zonse zotheka kuti tipeleke cakudya cauzimu kwa abale amene anatsala ku Malawi, komanso amene anathaŵila ku Mozambique cifukwa ca ciwawa. Gulu lomasulila Chichewa, cinenelo cimene anthu ambili amakamba ku Malawi, linasamutsidwila ku Zimbabwe pa famu ina yaikulu ya m’bale. M’baleyo anawamangila nyumba zokhalamo na ofesi. Kumeneko, iwo anapitiliza kugwila nchito yofunika kwambili yomasulila mabuku ophunzilila Baibo.

Tinapanga makonzedwe akuti oyang’anila madela a ku Malawi azibwela ku Zimbabwe kudzapezeka msonkhano wacigawo m’Chichewa caka ciliconse. Akabwela anali kupatsidwa maautilaini a nkhani za msonkhano wacigawo. Ndiyeno akabwelela ku Malawi, anali kulimbikitsa abale na alongo m’mipingo pogwilitsa nchito maautilaini amenewo. Caka cina atabwela ku Zimbabwe, tinalinganiza Sukulu ya Utumiki wa Ufumu n’colinga cakuti tilimbikitse oyang’anila madela olimba mtima amenewa.

ikukamba nkhani m’Chichewa pa msonkhano wacigawo wa Chichedwa komanso Cishona ku Zimbabwe

Mu February 1975, n’napita ku Mozambique kukaona Mboni zimene zinathaŵila ku misasa kucokela ku Malawi. Abale amenewo anali kuyenda nalo pamodzi gulu, kuphatikizapo makonzedwe atsopano akuti pa mpingo pazikhala bungwe la akulu. Akuluwo anakonza zinthu zambili zauzimu monga kukamba nkhani za anthu onse, kukambilana lemba la tsiku na Nsanja ya Mlonda, komanso ngakhale kucita misonkhano ikulu-ikulu. M’misasa imeneyo anakhazikitsa dongosolo monga la ku msonkhano wacigawo. Munali dipatimenti yoyeletsa, yogaŵila cakudya, komanso ya zaulonda. Abale okhulupilikawo anacita zambili cifukwa ca dalitso la Yehova, ndipo n’nalimbikitsidwa ngako.

Ca kumapeto kwa 1970, ofesi ya nthambi ya Zambia inayamba kusamalila nchito za Mboni ku Malawi. Ngakhale n’telo, nthawi zonse n’nali kuganizila abale ku Malawi na kuwapemphelela. N’zimenenso abale ena anali kucita. Popeza kuti n’nali m’Komiti ya Nthambi ya Zimbabwe, kangapo konse, n’nakumana na oimilako likulu lathu, komanso abale a paudindo a ku Malawi, South Africa, na Zambia. Nthawi zonse tikamakambilana, tinali kufunsa kuti: “N’ciyani cina cimene tingawacitile abale athu ku Malawi?”

M’kupita kwa nthawi, cizunzo cinayamba kucepa. Abale amene anathaŵa, anayamba kubwelela ku Malawi. Ndipo amene sanathaŵe, pang’ono-m’pang’ono anayamba kupezako mpumulo ku nkhanza zimene boma linali kuwacita. Maiko oyandikana na Malawi, amene nawonso munali ziletso, analola kuti Mboni za Yehova ziyambenso kulalikila na kusonkhana, ndipo anacotsa ziletsozo. Izi n’zimenenso dziko la Mozambique linacita mu 1991. Koma tinali kudzifunsa kuti, ‘Kodi Mboni za Yehova ku Malawi adzazimasula liti?’

KUBWELELA KU MALAWI

Pamapeto pake, zandale zinasintha ku Malawi ndipo mu 1993, boma linacotsa ciletso pa Mboni za Yehova. Ciletso citangocotsedwa, n’nali kuceza na mmishonale wina, amene ananifunsa kuti: “Kodi mudzabwelelanso ku Malawi?” Pa nthawiyo n’nali na zaka 59, conco n’namuyankha kuti, “Ayi, nakalamba!” Koma tsiku lomwelo tinalandila uthenga kucokela ku Bungwe Lolamulila wotipempha kuti tibwelele ku Malawi.

Utumiki wathu ku Zimbabwe tinali kuukonda kwambili. Conco zinali zovuta kupanga cisankho. Tinali titamanga mudzi, ndipo tinapeza mabwenzi abwino kwambili. Bungwe Lolamulila linatiuza kuti ngati tifuna, tingakhalebe ku Zimbabwe komweko. Motelo, zinali zosavuta kusankha njila yathu na kukhalabe ku Zimbabwe. Koma tinasinkha-sinkha citsanzo ca Abulahamu na Sara. Ali okalamba, iwo anasiya malo awo abwino pofuna kutsatila citsogozo ca Yehova.—Gen. 12:1-5.

Tinasankha kutsatila citsogozo ca gulu la Yehova, ndipo tinabwelela ku Malawi pa February 1, 1995. Panthawiyi n’kuti zakwana ndendende zaka 28, kucoka pamene tinafika koyamba ku Malawi. Komiti ya Nthambi yokhala na abale atatu inakhazikitsidwa. Ine na abale ena aŵili ndife tinali ziwalo za komitiyo. Posakhalitsa, tinali kalikiliki kukhazikitsanso nchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo.

YEHOVA NDIYE AMAKULITSA

Ndine wokondwa kwambili kuona kuti Yehova akudalitsa nchito yolalikila, ndipo ikupita patsogolo mofulumila. Ciŵelengelo ca ofalitsa cinakwela kwambili kucoka pa 30,000 mu 1993, kufika 42,000 mu 1998. * Bungwe Lolamulila linavomeleza kuti pamangidwe ofesi ya nthambi yatsopano, cifukwa ciŵelengo ca ofalitsa cinali kukwelela-kwelela. Tinagula malo okwana mahekitala 12 ku Lilongwe, ndipo n’nasankhidwa kuti nizitumikila m’komiti yomanga.

M’bale Guy Pierce wa m’Bungwe Lolamulila ndiye anakamba nkhani yopatulila ofesi ya nthambi yatsopano mu May 2001. Mboni zoposa 2 sauzande zinapezeka pa cocitikaco, ndipo ambili anali atakhala m’coonadi zaka zoposa 40. Abale na alongo okhulupilika amenewo anali atapilila mazunzo osaneneka panthawi ya ciletso. Kuthupi, anali osoŵa, koma kuuzimu, anali olemela kwambili. Ndipo iwo anali okondwa kudzaona Beteli yawo yatsopano. Anali kuimba nyimbo za Ufumu m’cinenelo cawo mogwilizana kulikonse kumene apita pa Betelipo. Zimenezi zinapangitsa cocitikaco kukhala colimbikitsa kwambili pa umoyo wanga. Ndipo zinapeleka umboni wakuti Yehova amadalitsa anthu amene amapilila mayeso mokhulupilika.

Ofesi ya nthambi itatha kumangidwa, n’nakondwela kuyamba kupatsidwa mwayi wokamba nkhani zopatulila Nyumba za Ufumu. Mipingo ku Malawi inapindula na pulogilamu ya gulu yomanga Nyumba za Ufumu m’madela ambili amene abale ni osauka. Kale, mipingo ina inali kusonkhana m’Nyumba za Ufumu zaudzu, ndipo anali kupanga mabenchi oumba. Koma tsopano abale amagwila nchito mwakhama kuumba nchelwa na kuziocha mu uvuni kuti amange malo okongola atsopano osonkhanamo. Abalewa anasankha kugwilitsabe nchito mabenchi m’nyumba za Ufumu m’malo mwa mipando, cifukwa benchi imakhala anthu ambili.

Nimacitanso cidwi nikaona mmene Yehova amathandizila anthu ake kukula mwauzimu. Abale acinyamata acikuda ananikondweletsa kwambili cifukwa ca kudzipeleka kwawo kuti acite mautumiki osiyana-siyana, ndipo anali kugwila zinthu msanga gulu la Yehova likamawaphunzitsa nchito. Zotulukapo zake, anakwanitsa kusenza maudindo akulu-akulu pa Beteli komanso m’mipingo. Mipingo inalimbikitsidwanso na oyang’anila madela ongoikidwa kumene, amene ambili mwa iwo anali okwatila. Mabanja amenewo anasankha kutumikila Yehova popanda zoceutsa posakhala na ŵana, ngakhale kuti anthu ambili amayembekezela okwatilana kukhala na ŵana.

N’NAKHUTILA NA ZISANKHO ZIMENE N’NAPANGA

Ine na mkazi wanga Anne pa Beteli ya Britain

N’tatumikila ku Africa zaka 52, n’nayamba kudwala. Bungwe Lolamulila linavomeleza pempho la Komiti ya Nthambi lakuti tikatumikile ku Beteli ya Britain. Sitinakondwele kusiya utumiki umene tinali kuukonda kwambili. Koma banja la Beteli kuno ku Britain likutisamalila bwino kwambili pa ukalamba wathu.

Naona kuti kulola Yehova kunitsogolela njila pa umoyo wanga cinali cisankho cabwino ngako! Nikanadalila luso langa lomvetsa zinthu, sembe nili na umoyo wosiyana na umene nili nawo palipano. Yehova nthawi zonse anali kudziŵa zimene n’nali kufunikila kuti iye ‘awongole njila zanga.’ (Miy. 3:5, 6) Nili mnyamata n’nali kufunitsitsa kuphunzila nchito pa kampani yaikulu. Koma gulu la Yehova la padziko lonse linanipatsa nchito yauzimu imene nakhutila nayo kwambili. Nakhala wokhutila kwambili cifukwa cotumikila Yehova, ndipo nidzapitilizabe kutelo.

^ Mbili ya Mboni za Yehova ku Malawi, inafalitsidwa mu Buku Lapacaka la Mboni za Yehova, mas. 148-223.

^ Lomba, ku Malawi kuli ofalitsa oposa 100,000.