Khalani na Maganizo Oyenela pa Nkhani ya Kumwa Moŵa
Khalani na Maganizo Oyenela pa Nkhani ya Kumwa Moŵa
TONY, amene wachulidwa munkhani yoyamba ija, sembe ali na moyo wosangalala akanavomeleza kuti anali na vuto lomwa mwaucidakwa. Komabe, cifukwa cakuti anali kumwa moŵa wambili popanda kudziŵika kuti waledzela, anali kuona kuti palibe vuto lililonse. N’cifukwa ciani maganizo a Tony anali olakwika?
Iye anali kulephela kuganiza bwino cifukwa comwa moŵa kwambili. Kaya Tony anali kudziŵa kapena ayi, ubongo wake unali kulephela kugwila bwino nchito akaledzela. Iye akamwa kwambili, m’pamenenso anali kulephela kudziŵa kuti ali na vuto lomwa moŵa mwaucidakwa.
Cifukwa cina cimene cinali kucititsa kuti Tony alephele kudziŵa kuti anali na vutoli cinali coti anali kufunitsitsa kuti apitilize kumwa moŵa kwambili. Allen, yemwenso tam’chula m’nkhani yapita ija, poyamba anali kukana zoti ali na vuto lomwa moŵa mwaucidakwa. Iye ananena kuti: “Sin’nali kufuna kuti ena adziŵe kuti nimamwa kwambili moŵa ndipo n’nali kupeleka zifukwa zosonyeza kuti palibe vuto lililonse na mmene nikumwela, n’nali kukondanso kunena kuti sinimwa moŵa mwaucidakwa. N’nali kucita zonsezi n’colinga coti nisasiye kumwa moŵa.” Ngakhale kuti anthu anali kuona kuti Tony na Allen akumamwa moŵa kwambili, eniakewo anali kuona kuti alibe vuto lililonse. Ndipo onsewa anafunika kuyesetsa kuti asinthe khalidwe lawo. Koma kodi anayenela kucita ciani?
Yesetsani Kupewa Kumwa Moŵa Mwaucidakwa
Anthu ambili omwe anasiya kumwa moŵa mwaucidakwa anatsatila mawu a Yesu akuti: “Ngati diso lako lakumanja limakupunthwitsa, ulikolowole ndi kulitaya. Pakuti n’kwabwino kuti ukhale wopanda ciwalo cimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse liponyedwe m’Gehena.”—Mateyo 5:29.
Pamenepa, sikuti Yesu anali kulimbikitsa kuti tizidzidula ziwalo m’lingalilo lenileni ayi, koma anali kuphunzitsa mfundo yoti tizisiyilatu khalidwe lililonse limene lingawonongetse ubale wathu na Yehova. N’zoona kuti zilizonse zimene tingacite pothana na vutoli zingatiwawe kwambili koma zingatithandize kuti tisamaganize kapena kucita zinthu zimene zingacititse kuti tizimwa moŵa mwaucidakwa. a Conco, ngati ena akuuzani kuti mwayamba kumwa moŵa mwaucidakwa, yesetsani kuti mucepetse. Ngati zikuonekelatu kuti simungathe, yesetsani kuti mungosiyilatu kumwa moŵa. Ngakhale kuti zimenezi zingakhale zopweteka kwambili, koma n’zabwino kusiyana na kukhala na moyo wosalongosoka.
Mwina inuyo sicidakwa, koma kodi mumakonda kumwa moŵa kwambili? Ngati zili conco, kodi mungacite ciani kuti muzimwa moyenela?
Zinthu Zimene Zingakuthandizeni
1. Muzipemphela kaŵili-kaŵili ndiponso mocokela pansi pa mtima. Baibo imalangiza anthu amene akufuna kusangalatsa Yehova Mulungu kuti: “Pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzero, limodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Mukatelo, mtendele wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalila, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Kodi mungachule zinthu ziti m’pemphelo kuti mukhale na mtendele wa mumtima umenewu?
Vomelezani moona mtima kuti muli na vuto lomwa moŵa mwaucidakwa ndipo muziona kuti ni udindo wanu kuthana na vutolo. Muuzeni Mulungu zimene mukufuna kucita kuti muthane na vutolo komanso kuti mupewe mavuto ena ndipo iye adzakuthandizani. Baibo imati: “Wobisa macimo ake sadzaona mwayi; koma wakuwavomeleza, nawasiya adzacitidwa cifundo.” (Miyambo 28:13) Yesu ananenanso kuti tingapemphe kuti: “Musatilowetse m’mayeselo, koma mutilanditse kwa woipayo.” (Mateyo 6:13) Ndiyeno kodi mungacite ciani kuti muzicita zinthu mogwilizana na mapemphelo anuwo? Nanga mungadziŵe bwanji kuti Mulungu wayankha mapemphelo anu?
2. Dalilani Mawu a Mulungu. Baibo imati: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu, . . . Amathanso kuzindikila malingalilo ndi zolinga za mtima.” (Aheberi 4:12) Anthu ambili omwe poyamba anali zidakwa aona kuti kuŵelenga Baibo tsiku lililonse ndiponso kusinkhasinkha kwawathandiza kwambili. Munthu wina woopa Mulungu, yemwe analemba nawo masalmo anati: “Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimilila m’njila ya ocimwa, kapena wosakhala pansi pabwalo la onyoza. Komatu m’cilamulo ca Yehova muli cikondwelelo cake; ndipo m’cilamulo cake amalingilila usana ndi usiku. . . . Zonse azicita apindula nazo.”—Salmo 1:1-3.
Allen, yemwe anathana na vuto lake lomwa mowa mwaucidakwa cifukwa cophunzila Baibo na Mboni za Yehova, anati: “Nimakhulupilila kuti zikanakhala kuti sininaphunzile Baibo ndiponso sinitsatila mfundo zake, zomwe zinanithandiza kuti nisiye kumwa moŵa mwaucidakwa, bwenzi pano nitafa kale-kale.”
3. Muzidziletsa. Baibo imanena kuti anthu ena omwe poyamba anali zidakwa mumpingo wacikhristu anasambitsidwa “ndi mzimu wa Mulungu wathu.” (1 Akorinto 6:9-11) Kodi zimenezo zinatheka bwanji? Njila imodzi inali yoti anathandizidwa kusiya kumwa moŵa mwaucidakwa ndiponso kucita maphwando aphokoso. Iwo anakwanitsa kusiya zimenezi cifukwa cokhala na khalidwe lodziletsa lomwe munthu amakhala nalo cifukwa cothandizidwa na mzimu woyela wa Mulungu. Baibo imati: “Musamaledzele naye vinyo, mmene muli makhalidwe oipa, koma khalanibe odzala ndi mzimu.” (Aefeso 5:18; Agalatiya 5:21-23) Yesu Khristu analonjeza kuti ‘Atate wakumwamba adzapeleka mowolowa manja mzimu woyela kwa amene akum’pempha.’ Conco, “pemphanibe, ndipo adzakupatsani.”—Luka 11:9, 13.
Anthu omwe akufuna kulambila Yehova movomelezeka angathe kukhala odziletsa ngati amaŵelenga na kuphunzila Baibo ndiponso kupemphela nthawi zonse mocokela pansi pa mtima. M’malo moganiza kuti simungathe kukhala odziletsa, khulupililani lonjezo la m’Mawu a Mulungu lakuti: “Iye amene akufesela mzimu adzakolola moyo wosatha ku mzimuwo. Conco tisaleke kucita zabwino, pakuti panyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa.”—Agalatiya 6:8, 9.
4. Muziceza na anthu akhalidwe labwino. Baibo imati: “Ukayenda ndi anzelu udzakhala wanzelu: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Uzani anzanu kuti mwatsimikiza mtima kusiya kumwa moŵa mwaucidakwa. Komabe, Mawu a Mulungu amacenjeza kuti mukasiya “kumwa vinyo mopitilila muyezo, maphwando a phokoso, kumwa kwa mpikisano,” anzanu ena omwe munkamwa nawo ‘sangamvetse, conco angamakunyozeni.’ (1 Petulo 4:3, 4) Musamaceze na anthu amene sakufuna kuti mucepetse kumwa moŵa.
5. Dziikileni malile. Baibo imati: “Musamatengele nzelu za dongosolo lino la zinthu, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikile cimene cili cifunilo ca Mulungu, cabwino ndi covomelezeka ndi cangwilo.” (Aroma 12:2) Mukalola kuti mfundo za m’Mawu a Mulungu zikuthandizeni kuika malile pankhani ya kumwa moŵa, osati anzanu kapena “dongosolo lino la zinthu,” mudzacita zinthu zosangalatsa Mulungu pamoyo wanu. Koma kodi mungadziŵe bwanji kuti muyezo wa moŵa womwe mwasankhawo ni wabwino kwa inu?
Ngati mwamwa moŵa ndipo mukulephela kuganiza bwino, ndiye kuti mwamwa mopitilila malil anu. Conco ngati mwasankha kuti muzimwa moŵa, ni bwino kudziikila malile enieni pa kuculuka kwa moŵa umene muzimwa, m’malo moganiza kuti musiya mukaona kuti mwayamba kuledzela. Musalole kuti mtima wosavomeleza kuti muli ni vuto ukulepheletseni kuthana na vuto lomwa mowa mwaucidakwa. Ikani malile omwe angakuthandizeni kuti musamwe moŵa kwambili.
6. Muzikana. Baibo imati: “Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.” (Mateyo 5:37) Muzikana mwaulemu ngati wina akupitilizabe kukukakamizani kuti mumwe moŵa umene iye akukupatsani. Mawu a Mulungu amati: “Nthawi zonse mawu anu azikhala acisomo, okoleletsa ndi mcele, kuti mudziŵe mmene mungayankhile wina aliyense.”—Akolose 4:6.
7. Pemphani kuti ena akuthandizeni. Pemphani kuti anzanu ena omwe angakulimbikitseni kuti musamamwe moŵa kwambili akuthandizeni ndiponso akulimbikitseni mwauzimu. Baibo imati: “Aŵili aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphotho yabwino m’nchito zawo. Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzake.” (Mlaliki 4:9, 10; Yakobe 5:14, 16) Bungwe lina la ku America loona zoti anthu asamamwe mwaucidakwa linati: “Nthawi zina zingakhale zovuta kuti mucepetse kumwa moŵa. Conco pemphani kuti abale ndiponso anzanu akuthandizeni kuthana na vuto lomwa moŵa mwaucidakwa.”—National Institute on Alcohol Abuse and Alcoholism.
8. Musasinthe zimene mwatsimikiza kucita. Baibo imati: “Khalani ocita zimene mawu amanena, osati ongomva cabe, ndi kudzinyenga ndi malingalilo onama. Koma woyang’anitsitsa m’lamulo langwilo laufulu, amene amalimbikila kutelo, adzakhala wosangalala policita cifukwa cakuti sali wongomva n’kuiwala, koma wocita.”—Yakobe 1:22, 25.
Zimene Mungacite Kuti Muthane na Vuto la Ucidakwa
Sikuti aliyense amene amamwa kwambili moŵa ndiye kuti ni cidakwa. Koma ena amayamba kumwa kwambili ndiponso kaŵili-kaŵili moti satha kukhala osamwa. Popeza kuti anthu omwe ni zidakwa amadalila moŵa pamoyo wawo, amafunika kuthandizidwa mwapadela, osati kungodalila thandizo lauzimu komanso kungokhala na mtima wofunitsitsa kusiya moŵa. Allen ananena kuti: “Nitasiya kumwa moŵa, ninadwala kwambili. Zimenezi zinanicititsa kudziŵa kuti ninafunika kupita kucipatala kuwonjezela pa thandizo lauzimu limene n’nali kulandila.”
Anthu ambili omwe amamwa moŵa mwaucidakwa amafunika kupita kucipatala kuti athane na vuto lawolo. b Ena amafunika kugonekedwa m’cipatala kuti acile matenda amene amabwela munthu akasiya kumwa moŵa mwaucidakwa. Komanso kuti alandile mankhwala othandiza kuti asiye kulakalaka kwambili moŵa ndiponso kuti awathandize kuti asafunenso kumwa moŵa. Mwana wa Mulungu amene anali kucita zozizwitsa ananena kuti: “Anthu amphamvu safuna wocilitsa, koma odwala ndi amene amam’funa.”—Maliko 2:17.
Ubwino Wotsatila Malangizo a Mulungu
Malangizo othandiza omwe amapezeka m’Baibo ni ocokela kwa Mulungu woona, amene amatifunila zabwino. Amafuna kuti tizisangalala panopa komanso kuti zinthu zizitiyendela bwino kwa moyo wathu wonse. Allen watha zaka 24 atasiya moŵa ndipo ananena kuti: “Ninasangalala kudziŵa kuti nikhoza kusintha khalidwe komanso ninaphunzila kuti Yehova anali kufunitsitsa kunithandiza kuti nisinthe khalidwe langa loipa ndipo . . . ” Allen anadukiza kulankhula pofuna kudzigwila kuti asalile cifukwa cokumbukila nthawi imene anali kumwa moŵa mwaucidakwayo. Kenako iye anapitiriza kuti, “Kungoti, . . . zimanilimbikitsa kwambili nikakumbukila kuti Yehova amatimvetsa ndiponso amatisamalila komanso kutithandiza.”
Conco, ngati mukulephela kusiya khalidwe lomwa moŵa mwaucidakwa, musaganize kuti nimwe wolephela kapena kuti simungathenso kuthana na vutolo. Allen komanso anthu ena ambili-mbili analinso na vuto ngati lanu ndipo anacepetsa kumwa moŵa komanso ena anangosiyilatu. Iwo sadandaula kuti anasiya moŵa ndiponso inuyo simudzadandaula.
Kaya mwasankha kuti muzimwa mowa pang’ono kapena mwasankha zongosiyilatu, tsatilani malangizo a Mulungu akuti: “Bwenzi utamvela malamulo anga mtendele wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi cilungamo cako monga mafunde a nyanja.”—Yesaya 48:18.
[Mau apansi]
a Onani bokosi lakuti, “Kodi Nimamwa Moŵa Mwaucidakwa?” patsamba 8.
b Pali zipatala zambili ndiponso malo ena othandizila anthu amene ali na vuto lomwa moŵa mwaucidakwa. Nsanja ya M’londa sisankhila anthu mankhwala. Aliyense ayenela kufufuza bwino za mankhwala n’kusankha yekha mankhwala amene satsutsana na zimene Baibo imaphunzitsa
[Bokosi]
Kodi Nimamwa Moŵa Mwaucidakwa?
• Dzifunseni kuti:
• Kodi pali pano nimamwa moŵa kwambili kuposa kale?
• Kodi nimamwa kaŵili-kaŵili kuposa kale?
• Kodi pali pano nimafuna kuti moŵa wake uzikhala wamphamvu kwambili?
• Kodi nimamwa moŵa n’colinga coti niiwale mavuto?
• Kodi mnzanga kapena wacibale wina wanicenjezapo kuti nikumwa mowa kwambili?
• Kodi nakumanapo na mavuto panyumba, kunchito kapena paulendo cifukwa comwa moŵa mwaucidakwa?
• Kodi zimanivuta kutha mlungu wonse osamwako moŵa?
• Kodi sinisangalala anthu ena akamakana kumwa moŵa?
• Kodi nimabisila anthu ena kuculuka kwa moŵa umene nimamwa?
Ngati pamafunso amenewa mwayankha funso limodzi kapena angapo kuti inde, ndiye kuti mukufunika kusintha.
[Bokosi]
Citani Zinthu Mwanzelu pa Nkhani ya Kumwa Moŵa
Musanamwe moŵa, dzifunseni kuti:
• Kodi nikuyeneladi kumwa moŵa?
Malangizo: Munthu amene amalephela kudziletsa ayenela kupewelatu kumwa moŵa.
• Kodi nizimwa moŵa woculuka bwanji?
Malangizo: Dziŵani pamene muyenela kusiyila kumwa moŵa musanayambe kuledzela.
• Kodi nizimwa nthawi yanji?
Malangizo: Musamwe moŵa n’kuyendetsa motoka kapena kugwila nchito inayake imene imafuna kusamala kwambili. Musamwe moŵa kenako n’kupita kolambila Mulungu; musamwe moŵa ngati muli na pakati komanso ngati mukulandila cithandizo ca mankhwala a matenda enaake.
• Kodi nizikamwela kuti?
Malangizo: Pamalo amene pali anthu amakhalidwe abwino; musamwele kwanokha pofuna kuti ena asakuoneni; musamwele pamalo pamene pali anthu omwe amadana na moŵa.
•Kodi nizimwa na ndani?
Malangizo: Ni anzanu kapena abale anu omwe ali na makhalidwe abwino. Musamwe moŵa na zidakwa.
[Bokosi]
Mawu a Mulungu Anam’thandiza Kusiya Ucidakwa
Mwamuna wina ku Thailand dzina lake Supot anali cidakwa. Poyamba, iye anali kukonda kumwa madzulo cabe. Koma pang’ono-n’pang’ono anayamba kumamwanso m’mawa komanso masana. Iye anali kumwa moŵa n’colinga coti aledzele. Kenako anayamba kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova ndipo ataphunzila kuti Yehova Mulungu sasangalala na anthu amene amamwa moŵa mwaucidakwa, Supot anasiya kumwa moŵa. Koma patapita kanthawi, anayambilanso kumwa ndipo banja lake linakhumudwa kwambili.
Komabe, Supot anali akukondabe Yehova ndipo anali kufunitsitsa kuti azimutumikila m’njila yoyenelela. Akhristu anzake anapitiliza kumuthandiza ndipo iwo anauza mkazi na ana ake kuti aziceza naye kwambili komanso kuti asasiye kumuthandiza. Nthawi imeneyo, mawu osapita m’mbali a pa 1 Akorinto 6:10 onena kuti ‘zidakwa sizidzalowa mu ufumu wa Mulungu,’ anamuthandiza kwambili kuona kuti kumwa moŵa mwaucidakwa ni nkhani yaikulu. Supot anazindikila kuti anayenela kuyesetsa kuthana na vuto lakelo.
Panthawi imeneyi Supot anaganiza zongosiyilatu kumwa moŵa. Pamapeto pake, mothandizidwa na mzimu woyela wa Mulungu, Mawu a Mulungu, banja lake komanso mpingo, Supot analigonjetsa vuto lake laucidakwa. Anthu a m’banja lake anasangalala kwambili iye atabatizika posonyeza kuti wadzipeleka kuti atumikile Mulungu. Masiku ano Supot amasangalala kwambili cifukwa ali paubwenzi wabwino na Mulungu womwe anali kufunitsitsa kwambili pamoyo wake. Tsopano iye amagwilitsa nchito nthawi yake pophunzitsa anthu Mawu a Mulungu.