Onani zimene zilipo

Kodi Muyenela Kukhoma Misonkho?

Kodi Muyenela Kukhoma Misonkho?

Kodi Muyenela Kukhoma Misonkho?

ANTHU ambili sakonda kukhoma msonkho. Iwo amaona kuti ndalama zawo zamsonkho zimangowonongedwa pa zinthu zosafunika, zimagwilitsidwa nchito pa zinthu zosayenela, komanso zimabedwa na anthu akatangale. Ena amakana kukhoma misonkho cifukwa cakuti ndalama zamsonkho zimagwilitsidwa nchito pa zinthu zoipa. Pofotokoza cifukwa cimene sakhomela misonkho, anthu a m’tawuni ina ya ku Middle East anati: “Sitingapeleke ndalama zoti akagulile zipolopolo zophela ana athu.”

Anthu a m’madela ambili amakhalanso na maganizo amenewa ndipo izi sizinayambe lelo. Pofotokoza mmene anali kuonela mfundoyi malinga na cikumbumtima cake, malemu Mohandas K. Gandhi, yemwe anali mtsogoleli wacihindu wa ku India, anati: “Munthu amene amathandiza dziko lokonda nkhondo mwa njila iliyonse, ndiye kuti akuthandiza nawo kucita chimo. Ndipo munthu aliyense amene amakhoma msonkho, wamng’ono kapena wamkulu, amakhala kuti akuthandiza pa chimo limene boma limacita.”

Nayenso katswili wina wofufuza nzelu za anthu amene anakhalapo m’zaka za m’ma 1800, dzina lake Henry David Thoreau, anafotokoza kuti sangakhome msonkho cifukwa cakuti ndalama zamsonkho zimagwilitsidwa nchito pa zinthu zoipa. Iye anafunsa kuti: “Kodi munthu ayenela kulola kuti wopanga malamulo amusankhile pa zinthu zimene angathe kusankha yekha mogwilizana na cikumbumtima cake? Ngati ni conco, n’cifukwa ciani munthu aliyense ali na cikumbumtima?”

Nkhani imeneyi imakhudzanso Akhristu cifukwa Baibo imaphunzitsa momveka bwino kuti Akhristu ayenela kukhala na cikumbumtima coyela pa zinthu zonse. (2 Timoteyo 1:3) Komabe, Baibo imanenanso kuti maboma ali na udindo wotolela ndalama zamsonkho. Imati: “Munthu aliyense azimvela olamulila akulu-akulu [maboma a anthu], cifukwa palibe ulamulilo umene ungakhalepo kupatulapo ngati Mulungu waulola. Olamulila amene alipowa ali m’malo awo osiyana-siyana mololedwa ndi Mulungu. Cotelo pali cifukwa cabwino cakuti anthu inu mukhalile ogonjela, osati cabe cifukwa coopa mkwiyo umenewo, komanso cifukwa ca cikumbumtima canu. N’cifukwa cake mumakhomanso misonkho, pakuti iwo ndi anchito a Mulungu otumikila anthu, ndipo akukwanilitsa colinga cimeneci nthawi zonse. Pelekani kwa onse zimene amafuna. Amene amafuna msonkho, m’patseni msonkho.”—Aroma 13:1, 5-7.

Pa cifukwa cimeneci, Akhristu a m’nthawi ya atumwi anali kudziŵika kuti anali kukhoma misonkho ngakhale kuti mbali yaikulu ya ndalamazo zinali kugwilitsidwa nchito pothandizila nkhondo. N’cimodzi-modzinso na Mboni za Yehova masiku ano. a Ndiyeno, kodi n’cifukwa ciani timakhoma misonkho ngakhale kuti ndalama zamisonkhozo amazigwilitsa nchito pa zinthu zoti Mkhristu sagwilizana nazo? Kodi Mkhristu ayenela kukhomabe msonkho ngakhale pamene cikumbumtima cake cikumuletsa kutelo?

Mmene Nkhani Yokhoma Misonkho Imakhudzila Cikumbumtima

N’zocititsa cidwi kudziŵa kuti ndalama zina zamsonkho zimene Akhristu a nthawi ya atumwi anali kupeleka zinali kugwilitsidwa nchito pa zinthu zokhudzana na nkhondo. Ngakhale zinali conco, Akhristuwa anali kupelekabe msonkho n’colinga cakuti akhale na cikumbumtima coyela. Koma pa nkhani ya cikumbumtima yomweyi, Gandhi na Thoreau anali kuona kuti munthu sufunika kupeleka msonkho kuti ukhale na cikumbumtima coyela.

Onani kuti Akhristu anali kumvela lamulo lopezeka mu Aroma caputala 13, osati cabe cifukwa coopa kulangidwa komanso ‘cifukwa ca cikumbumtima cawo.’ (Aroma 13:5) Kuti Mkhristu akhale na cikumbumtima cabwino amayenela kukhoma misonkho ngakhale zitakhala kuti ndalama zamsonkhozo zikagwilitsidwa nchito pa zinthu zimene Mkhristuyo amaona kuti ni zoipa. Kuti timvetse bwino nkhani imeneyi, tiyenela kumvetsa mfundo yofunika kwambili yokhudza cikumbumtima. Cikumbumtima ni mphamvu yacibadwa imene imatiuza ngati tacita zabwino kapena zoipa.

Monga Thoreau ananenela, munthu aliyense ali na cikumbumtima ngakhale kuti si nthawi zonse pamene cimakhala codalilika. Kuti tikondweletse Mulungu, cikumbumtima cathu ciyenela kugwilizana na mfundo zake. Nthawi zambili timafunika kusintha mmene timaonela zinthu kuti maganizo athu agwilizane na maganizo a Mulungu, cifukwa maganizo ake ni apamwamba kuposa athu. (Salimo 19:7) Conco, tiyenela kuyesetsa kumvetsa mmene Mulungu amaonela maboma amene alipowa. Kodi iye amawaona bwanji?

Mtumwi Paulo ananena kuti mabomawa ni “anchito a Mulungu otumikila anthu.” (Aroma 13:6) Kodi zimenezi zikutanthauza ciani? Zikutanthauza kuti iwo amathandiza kuti m’dziko mukhale mtendele komanso amagwila nchito zofunika kwambili zothandiza anthu. Ngakhale boma limene limacita zinthu zakatangale zambili, nthawi zambili limathandizabe anthu pa nkhani monga zotumiza makalata, zamaphunzilo, zozimitsa moto komanso kukhazikitsa mtendele. Mulungu amadziŵa zinthu zonse zoipa zimene maboma amenewa amacita. Ngakhale zili conco, walola kuti mabomawo akhalepo kwa kanthawi ndipo amafuna kuti tizikhoma misonkho posonyeza kulemekeza dongosolo limeneli.

Komabe Mulungu walola mabomawa kuti angolamulila kwa kanthawi. Iye wakonza zoti adzacotse maboma amenewa n’kukhazikitsa Ufumu wake wakumwamba. Ufumuwo udzathetsa mavuto onse amene maboma a anthu abweletsa padzikoli pa zaka zonse zimene akhala akulamulila. (Danieli 2:44; Mateyu 6:10) Koma panopa Mulungu sanalamule Akhristu kuti asamamvele boma mwa kukana kukhoma misonkho kapena kucita zinthu zina.

Koma bwanji ngati mukuonabe kuti kupeleka ndalama zamsonkho zimene zimagwilitsidwa nchito pa nkhondo n’kucimwa ngati mmene Gandhi anali kuonela? Mofanana na mmene kuima pamalo okwela kumatithandizila kuona zinthu bwino-bwino, kuzindikila kuti maganizo a Mulungu ni apamwamba kwambili kuposa athu kungatithandize kusintha maganizo athu kuti agwilizane na ake. Kudzela mwa mneneli Yesaya, Mulungu anati: “Monga momwe kumwamba kulili pamwamba kuposa dziko lapansi, momwemonso njila zanga n’zapamwamba kuposa njila zanu, ndiponso maganizo anga ndi apamwamba kuposa maganizo anu.”—Yesaya 55:8, 9.

Kodi Tiyenela Kumvela Boma pa Ciliconse?

Zimene Baibo imaphunzitsa zoti tiyenela kumakhoma misonkho sizikutanthauza kuti maboma ali na mphamvu zolamula nzika zawo kucita ciliconse comwe mabomawo angafune. Yesu anaphunzitsa kuti ulamulilo umene Mulungu wapeleka kwa maboma amenewa uli na malile. Iye atafunsidwa ngati Mulungu anali kuona kuti ni zoyenela kupeleka msonkho ku boma la Aroma lomwe linali kulamulila pa nthawiyo, anayankha kuti: “Pelekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma zinthu za Mulungu muzizipeleka kwa Mulungu.”—Maliko 12:13-17.

Boma, kapena kuti “Kaisara,” ni limene limapanga ndalama. Conco Mulungu amaona kuti boma lili na ufulu wouza anthu kuti azibwezela ndalamazo ku boma mwa kukhoma misonkho. Komabe Yesu anasonyeza kuti boma lililonse siliyenela kutiuza kuti tilipatse “zinthu za Mulungu,” zomwe ni moyo ndiponso kulambila kwathu. Malamulo a boma kapena zimene likufuna kuti ticite zikakhala kuti zikutsutsana na malamulo a Mulungu, Akhristu ayenela “kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.”—Machitidwe 5:29.

Akhristu masiku ano akhoza kukhumudwa na mmene ndalama zawo zamsonkho zimagwilitsidwila nchito, komabe sayesa kusintha zinthu kapena kuukila boma mwa kukana kukhoma misonkho kapena kukana kucita zinthu zina zimene boma lingawauze. Kucita zimenezi kungasonyeze kuti iwo sakhulupilila kuti Mulungu adzathetsa mavuto onse a anthu. M’malomwake, iwo amayembekeza moleza mtima nthawi imene Mulungu adzasinthe zinthu kudzela mu Ufumu wa Mwana wake, Yesu, amene ananena kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.”—Yohane 18:36.

Ubwino Wotsatila Mfundo za M’Baibo

Kutsatila zimene Baibo imanena pa nkhani ya msonkho, kungakuthandizeni kwambili. Mungapewe kulandila cilango cimene cimapelekedwa kwa anthu ophwanya malamulo komanso simungamakhale na mantha oti mugwidwa. (Aroma 13:3-5) Ndipo cofunika kwambili n’coti mudzakhala na cikumbumtima coyela ndiponso mudzalemekeza Mulungu cifukwa ca khalidwe lanu lotsatila malamulo. N’zoona kuti kukhoma misonkho kungapangitse kuti muziwononga ndalama zambili poyelekeza na anthu amene amazemba misonkho kapena kucita cinyengo. Komabe, kucita zimenezi kungalimbitse cikhulupililo canu pa zimene Mulungu amalonjeza atumiki ake kuti adzawasamalila. Davide, yemwe analemba nawo Baibo, anafotokoza mfundo imeneyi motele: “Ndinali mwana, ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha cakudya.”—Salimo 37:25.

Komanso kumvetsa ndiponso kutsatila lamulo la m’Baibo lakuti muzikhoma misonkho kudzakuthandizani kukhala na mtendele wa mumtima. Mulungu sadzakuimbani mlandu cifukwa ca zimene boma limacita na ndalama zanu zamsonkho. Izi ni zofanana na zimene zimacitika ngati mwini wake wa nyumba imene mumacita lendi angagwilitse nchito ndalama zimene mumapeleka pa zinthu zoipa. Boma silingakuimbeni inuyo mlandu cifukwa ca zocita zakezo. Asanaphunzile coonadi, Stelvio, yemwe amakhala m’dziko lina la kum’mwela kwa Ulaya anali kufunitsitsa kusintha zinthu m’dziko lawo. Pofotokoza cifukwa cimene anasiyila kucita zimenezo, iye anati: “Ndinazindikila kuti munthu sangathe kukhazikitsa cilungamo, mtendele, na ubale weniweni m’dzikoli. Ufumu wa Mulungu wokha ni umene ungasinthe zinthu kuti dzikoli likhale labwino.”

Mofanana na Stelvio, inunso ngati mokhulupilika ‘mutamapeleka zinthu za Mulungu kwa Mulungu,’ mungakhale na cikhulupililo cakuti mudzakhalapo Mulungu akamadzabweletsa ulamulilo wolungama padzikoli. Ulamulilowu udzathetsa zinthu zonse zopanda cilungamo zimene ulamulilo wa anthu wabweletsa.

[Mau apansi]

a Kuti mudziŵe zambili pa nkhani yakuti a Mboni za Yehova amakhoma misonkho, onani Nsanja ya Olonda ya November 1, 2002, tsamba 13, ndime 15, ndiponso ya May 1, 1996, tsamba 17, ndime 7.

[Mau okopa]

Timafunika kusintha mmene timaonela zinthu kuti maganizo athu agwilizane na maganizo a Mulungu, cifukwa maganizo ake ni apamwamba kuposa athu

[Mau okopa]

Akhristu akamakhoma misonkho mokhulupilika, amakhala na cikumbumtima coyela ndipo amasonyeza kuti akudalila Mulungu kuti awathandiza pa zosowa zawo

[Mau okopa]

Pelekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma zinthu za Mulungu muzizipeleka kwa Mulungu

[Eni ake]

Copyright British Museum