Baibo Imasintha Anthu
MTSIKANA wina anali pa nchito yapamwamba koma analibe cidwi na za Mulungu. Kodi n’ciani cinathandiza mtsikana ameneyu kuti ayambe kukonda za Mulungu? Nanga ni zinthu ziti zokhudza imfa zimene mnyamata wina, yemwe anali wakatolika, anaphunzila zomwe zinam’thandiza kuti asinthe moyo wake? Komanso kodi ni zinthu ziti zokhudza Mulungu zimene mnyamata wina, yemwe sanali kusangalala na moyo, anaphunzila zomwe zinacititsa kuti asinthe n’kukhala wa Mboni? Ŵelengani nkhaniyi kuti mumve zimene anthuwa ananena.
“Kwa zaka zambili n’nali kudzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu anatilengelanji anthufe?’”—ROSALIND JOHN
CAKA COBADWA: 1963
DZIKO: BRITAIN
POYAMBA: N’NALI PA NCHITO YAPAMWAMBA
KALE LANGA:
N’nabadwila kudela la Croydon, ku South London. M’banja mwathu tilipo ana 9 ndipo ine nine wa nambala 6. Makolo anga kwawo ni kucilumba ca Caribbean ca ku St. Vincent. Mayi anga anali kupita kuchalichi ca Methodist. Koma ineyo n’nalibe cidwi na za Mulungu ngakhale kuti mwacibadwa n’nali kukonda kuŵelenga kuti nidziŵe zinthu zosiyana-siyana. Nthawi zambili nikakhala pa holide n’nali kupita kunyanja ndipo n’nali kukonda kuŵelenga mabuku osiyana-siyana amene n’nali kubweleka kulaibulale.
N’tamaliza sukulu, n’nayamba kuganizila mmene ningathandizile anthu ovutika. Conco n’nayamba kuthandiza anthu osowa pokhala komanso olumala. Kenako n’nayamba kucita maphunzilo azacipatala. N’tamaliza maphunzilo apamwambawa, n’nakhala na mwayi wogwila nchito zapamwamba zosiyana-siyana ndipo n’nali kukhala moyo wawofuwofu. Ngakhale kuti nchito yanga inali ya ndalama zambili ndipo n’nali kugwilila nchito makampani komanso mabungwe osiyana-siyana ngati mlangizi, inali yofewa moti n’nali kungogwilitsa nchito kompyuta ya laputopu komanso Intaneti. N’nali kupita kumayiko akunja pa ndege n’kukakhala milungu ingapo kuhotelo yodula ni yokongola komanso yokhala na malo ocitila masewela olimbitsa thupi. Kunena zoona moyo unali kunikomela kwambili. Komabe sin’naiwale colinga canga cofuna kuthandiza anthu ovutika.
MMENE BAIBO INASINTHILA MOYO WANGA:
Kwa zaka zambili n’nali kudzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu anatilengelanji anthufe, nanga colinga ca moyo n’ciani?’ Koma n’nali nisanayesepo kupeza mayankho a mafunso amenewa m’Baibo. Tsiku lina mu 1999, mbale wanga wamng’ono dzina lake Margaret na mnzake wina, omwe ni Mboni za Yehova anabwela kudzaniona. Mnzakeyo anali wacikondi komanso wokoma mtima ndipo anan’pempha kuti ayambe kun’phunzitsa Baibo. N’navomela, komabe n’nalibe cidwi kwenikweni na phunziloli cifukwa nchito yanga komanso moyo umene n’nali kukhala zinali kupangitsa kuti nisamakhale na nthawi yokwanila yophunzila.
M’caka ca 2002, n‘nasamukila kum’mwela cakumadzulo kwa England. Kumeneko, n’nayambanso sukulu ina n’colinga coti niwonjezele maphunzilo anga kuti nipezenso digili ina yapamwamba. Ine na mwana wanga tinayamba kusonkhana na Mboni za Yehova mlungu uliwonse ku Nyumba ya Ufumu. Ngakhale kuti n’nali kusangalala na zimene n’nali kuphunzila kuyunivesite, n’nali kuona kuti kuphunzila Baibo kunali kun’thandiza kumvetsa mavuto amene timakumana nawo pa moyo komanso zimene tingacite tikakumana na mavutowo. N’nazindikila kuti mfundo ya palemba la Mateyu 6:24, yoti sungatumikile ambuye aŵili, ni yoona. Uyenela kusankha kutumikila Mulungu kapena cuma. Conco n’naona kuti niyenela kusankha zinthu mwanzelu.
M’caka ca 2001, n’nali kukonda kukasonkhana ku kagulu ka phunzilo la Baibo ka Mboni za Yehova komwe tinali kuphunzila buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You? a N’nayamba kukhulupilila kuti ni Mlengi yekha Yehova, amene angathetse mavuto a anthu. Koma kusukulu kuja anali kutiphunzitsa kuti moyo wabwino sumadalila Mlengi. Zimenezi zinan’kwiyitsa kwambili. Conco n’tangophunzila miyezi iŵili yokha n’naganiza zosiya kuphunzila kuyunivesiteko kuti nizikhala na nthawi yokwanila yocitila zinthu zauzimu.
Lemba limene linan’thandiza kwambili kuti nisinthe moyo wanga ni la Miyambo 3:5, 6, limene limati: “Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalile luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukila m’njila zako zonse, ndipo iye adzawongola njila zako.” N’naona kuti n’napeza madalitso ambili cifukwa cophunzila za Mulungu wacikondi kuposa kukhala na cuma kapena kuchuka cifukwa ca maphunzilo apamwamba. Pamene n’napitiliza kuphunzila za colinga ca Mulungu cokhudza dziko lapansi komanso zimene Yesu anacita popeleka moyo wake cifukwa ca anthufe, m’pamenenso n’nali kufuna kudzipeleka kuti niyambe kutumikila Mlengi wathu Yehova. Ndipo mu April 2003, ninabatizika. N’tabatizika n’nayamba kusintha zina ni zina pa moyo wanga.
PHINDU LIMENE NAPEZA
N’maona kuti ubwenzi wanga na Yehova ni cinthu ca mtengo wapatali. Kudziŵa Yehova komanso kusonkhana ni a Mboni anzanga kwan’thandiza kuti nikhale na mtendele wamumtima komanso kuti nikhale wosangalala.
Zimene n’maphunzila m’Baibo komanso pamisonkhano ya Mboni ziman’thandiza kupeza zosowa zanga zauzimu. Nimasangalalanso nikamaphunzitsa ena za Yehova. Nchito yothandiza anthu kudziŵa za Yehova, nimaitenga ngati nchito yanga. Panopo nimaona kuti n’kuthandizadi anthu cifukwa nchito imeneyi imawathandiza kukhala na moyo wabwino panopo ndiponso kukhala ni ciyembekezo codzakhala na moyo wosatha m’dziko latsopano. Kuyambila mu June 2008, nakhala nikuthela nthawi yambili nikugwila nchito yotumikila Mulungu ndipo nikuona kuti zimenezi zapangitsa kuti nikhale wosangalala kwambili kuposa kale. Tsopano napeza colinga ceniceni ca moyo ndipo nimayamikila kwambili Yehova cifukwa ca zimenezi.
“Imfa ya mnzanga inanikhudza kwambili.”—ROMAN IRNESBERGER
CAKA COBADWA: 1973
DZIKO: AUSTRIA
POYAMBA: N’NALI KUCHOVA JUGA
KALE LANGA:
N’nakulila m’tawuni ina yaing’ono yochedwa Braunau, ku Austria. Anthu a m’dela limeneli anali olemela kwambili ndipo m’delali simunali kucitikacitika zaciwawa. Banja lathu linali lakatolika ndipo inenso n’nali wakatolika.
Zimene zinacitika nili wamng’ono zinanikhudza kwambili. Tsiku lina mu 1984 nili na zaka 11, n’nali kusewela mpila na mnzanga. Koma masana a tsiku lomwelo, mnzangayo anafa pa ngozi yagalimoto. Imfa ya mnzangayu inanikhudza kwambili. Kwa zaka zambili cicitikileni ngozi imeneyi, n’nali kudzifunsa kuti kodi cidzanicitikile n’ciani nikadzamwalila?
N’tasiya sukulu n’nayamba kugwila nchito ya zamagetsi. Ngakhale kuti n’nali kukonda kuchova juga ndipo nthawi zina n’nali kuluza ndalama zambili, sinali kusowa ndalama. N’nali kukondanso kwambili masewela komanso n’nayamba kukonda nyimbo zaphokoso kwambili za mawu otukwana. N’nali kungokhalila kupita kumalo azisangalalo, kumapate komanso n’nali kukonda kucita zaciwelewele. N’nali kucita zonsezi kuti nizisangalala koma sizinanithandize kukhala wosangalala.
MMENE BAIBO INASINTHILA MOYO WANGA:
Mu 1995, bambo ena acikulile a Mboni anafika panyumba panga ndipo ananipatsa buku limene linali na yankho la m’Baibo la funso lakuti, Kodi n’ciani cimacitika munthu akamwalila? Cifukwa coti n’nali kuganizilabe za imfa ya mnzanga uja, n’nalandila bukuli. N’naŵelenga buku lonse osati mutu wokha umene unali na nkhani yokhudza imfa.
Zimene n’naŵelenga zinayankha mafunso anga okhudza imfa. Komanso n’naphunzila zambili m’bukuli. Popeza n’nakulila m’banja lakatolika, n’nali kukhulupilila kwambili Yesu ndipo n’nali kumuona ngati Mulungu. Koma kuphunzila Baibo kunanithandiza kuti nikhale pa ubwenzi na Yehova Mulungu, yemwe ni Atate wa Yesu. N’nasangalala kwambili nitadziŵa kuti Yehova sadzibisa ndipo aliyense amene akufuna kumudziŵa akhoza kumudziŵa. (Mateyu 7:7-11) N’naphunzilanso kuti Yehova amasangalala kapena kukhumudwa na zocita zathu komanso kuti iye amakwanilitsa zimene walonjeza. Zimenezi zinacititsa kuti nizicita cidwi kwambili na maulosi a m’Baibo komanso kuti niyambe kufufuza mmene maulosi ena anakwanilitsidwila. Zimene n’napeza, zinacititsa kuti nizikhulupilila kwambili Mulungu.
Pasanapite nthawi ninazindikila kuti a Mboni za Yehova okha ni amene amathandiza anthu kumvetsa zimene Baibo imaphunzitsa. N’nali kuŵelenga m’Baibo langa lacikatolika mavesi amene n’nali kuwapeza m’mabuku a Mboni ndipo nikamacita zimenezi m’pamenenso n’nali kuona kuti napezadi coonadi.
Zimene n’naphunzila m’Baibo zinanithandiza kudziŵa kuti Yehova amafuna kuti nizitsatila mfundo za m’Baibo. N’taŵelenga lemba la Aefeso 4:22-24 n’naona kuti niyenela kuvula “umunthu wakale” umene ‘unali kugwilizana ni khalidwe langa lakale,’ ndipo niyenela “kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu.” Conco n’nasiya khalidwe langa laciwelewele. N’naonanso kuti niyenela kusiya juga cifukwa imacititsa munthu kukhala wokonda ndalama komanso wadyela. (1 Akorinto 6:9, 10) Koma n’nazindikila kuti zimenezi zingatheke pokha-pokha nitasiya kuceza na anzanga akale n’kuyamba kuceza na anthu amene amatsatila mfundo za m’Baibo.
Koma sizinali pepuka kuti nisinthe. Komabe n’nayamba kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova ndiponso n’nayamba kuceza ni a Mboniwo. N’napitilizanso kuphunzila Baibo panekha. Zonsezi zinanithandiza kuti nisiye kumvetsela nyimbo zoipa zija, nisinthe zolinga zanga pa moyo komanso kaonekedwe kanga. M’caka ca 1995, n’nabatizika n’kukhala wa Mboni za Yehova.
PHINDU LIMENE NAPEZA:
Palipano nimaona ndalama na cuma moyenela. Komanso poyamba n’nali wosacedwa kupsa mtima koma pano n’nasintha. Tsopano sinidelanso nkhawa kwambili za m’tsogolo.
Nikusangalala kwambili kukhala m’gulu la anthu amene akutumikila Yehova. Pa anthu amenewa, pali ena omwe ali na mavuto osiyana-siyana koma akupitilizabe kutumikila Mulungu mokhulupilika. Nimasangalala kwambili cifukwa panopa nikugwilitsa nchito nthawi na mphamvu zanga potumikila Yehova na kucitila ena zabwino osati pokwanilitsa zofuna zanga basi.
“Tsopano n’napeza colinga ca moyo wanga.”—IAN KING
CAKA COBADWA: 1963
DZIKO: ENGLAND
POYAMBA: SIN’NALI KUSANGALALA NA MOYO
KALE LANGA:
N’nabadwila ku England, koma nili na zaka 7 banja lathu linasamukila ku Australia. Tinakakhala kudela lina lochedwa Gold Coast, m’cigawo ca Queensland. Kudelali kumapita alendo ambili okaona malo. Ngakhale kuti banja lathu silinali lolemela, sitinali kusowa zinthu zofunika pa moyo.
Ngakhale kuti sininakule movutika, sin’nali kusangalala na moyo. Bambo anga anali cidakwa cadzaoneni. Sin’nali kuwakonda cifukwa ca khalidwe lawoli komanso cifukwa coti anali kucitila nkhanza amayi anga. N’takula n’namva zimene bambo anga anakumana nazo pa nthawi imene anali msilikali ku Malaya, ndipo zimenezi zinanithandiza kuti nimvetse cifukwa cake anali cidakwa komanso ankhanza.
N’tayamba maphunzilo a ku sekondale, inenso n’nayamba kumwa mowa mwaucidakwa. Nili na zaka 16 n’nasiya sukulu ndipo n’nalowa m’gulu la asilikali apanyanja. N’nayamba kugwilitsa nchito mankhwala osokoneza bongo komanso kukoka kwambili fodya. Ndipo sininali kukwanitsakukhala popanda kumwa mowa. Poyamba ninali kumwa kumapeto kwa mlungu basi, koma tsopano n’nayamba kumwa tsiku lililonse.
Nili na zaka pafupifupi 20 n’nayamba kukayikila ngati Mulungu alikodi. N’nali kuganiza kuti: ‘Ngati kulidi Mulungu, n’cifukwa ciani amalola kuti anthu azivutika?’ N’nafika mpaka polemba ndakatulo yoimba mlandu Mulungu cifukwa ca zoipa zimene zili padzikoli.
Nili na zaka 23, n’nacoka m’gulu la asilikali lija. Kenako n’nagwila nchito zosiyana-siyana ndipo mpaka n’napita kunja komwe n’nakakhalako kwa caka cimodzi, koma sin’nali kusangalalabe na moyo. N’nalibe colinga ciliconse pa moyo wanga ndipo palibe comwe cinali kunisangalatsa. N’nalibe nazo nchito zoti nikhale na nyumba yanga-yanga, nipeze nchito yokhazikika kapena nikwezedwe pa nchito. Zimene n’nali kuona ngati zikunisangalatsako zinali kumwa mowa komanso kumvetsela nyimbo basi.
Nimakumbukila nthawi imene n’nalakalaka nitadziŵa colinga ca moyo. N’nali nili ku Poland pamene n’napita kundende ina yochedwa Auschwitz, imene inali kudziŵika kuti anali kuzunzako anthu. N’nali n’taŵelenga nkhani zosiyana-siyana zonena za zinthu zoipa zimene zinali kucitika pandendeyi. Koma n’tafika kundendeyi n’kuona kukula kwake komanso zimene zinali kucitika, zinanikhudza kwambili. Sininamvetse kuti n’cifukwa ciani anthu anali kucitila nkhanza anthu anzawo conco. Nikukumbukila kuti pomwe n’nali kuyenda n’kumaona zimene zinali kucitika pandendeyi, misozi inali kungotsika ndipo n’nali kudzifunsa kuti ‘Kodi n’cifukwa ciani zinthu zimenezi zikucitika?’
MMENE BAIBO INASINTHILA MOYO WANGA:
M’caka ca 1993, n’tabwelelanso ku Australia, n’nayamba kuŵelenga Baibo kuti nipeze yankho la funso limeneli. Pasanapite nthawi, a Mboni za Yehova aŵili anafika panyumba panga ndipo ananiitanila kumsonkhano wawo womwe unacitikila kusitediyamu yapafupi. N’naganiza zopita kumsonkhanowu.
Miyezi ingapo m’mbuyomo, n’nalinso pasitediyamu yomweyi kuonela mpila, koma zimene n’naona pa nthawi ya msonkhanowu zinali zosiyana kwambili. N’naona kuti a Mboni anali anthu aulemu komanso anavala bwino ndipo ana awo anali akhalidwe labwino. Komanso n’nadabwa kwambili na zimene n’naona pa nthawi yopuma. Anthu ambili amene anali pamsonkhanowu anadyela pagalaundi koma pamene cigawo camasana cinali kuyamba, pagalaundipo panalibe ngakhale cinyalala cimodzi. Comwe cinanicititsa cidwi kwambili n’coti anthuwa anali kuoneka kuti ali na cimwemwe komanso mtendele wamumtima, zinthu zomwe ineyo n’nali kuzilakalaka kwa nthawi yaitali. Sinikumbukila nkhani iliyonse imene inakambidwa pamsonkhanowu, koma sinidzaiwala khalidwe labwino lomwe a Mboni anasonyeza.
Tsiku limenelo n’nakumbukila msuweni wanga amene anali kuŵelenga Baibo komanso kufufuza zokhudza zipembedzo zosiyana-siyana. Zaka zingapo m’mbuyomo iye ananiuza kuti Yesu ananena kuti tingathe kuzindikila cipembedzo coona malinga na zipatso zake. (Mateyu 7:15-20) N’naganiza zofufuza zimene zimacititsa kuti a Mboni akhale osiyana na ena onse. Zotsatila zake zinali zoti, kwa nthawi yoyamba, n’nayamba kuona kuti ningathe kukhala na tsogolo labwino.
Mlungu wotsatila, a Mboni amene ananiitanila kumsonkhano aja anabwelanso kunyumba kwathu. N’navomela atanipempha kuti niziphunzila nawo Baibo. N’nayambanso kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova.
N’tayamba kuphunzila Baibo, maganizo anga pa nkhani yokhudza Mulungu anasintha kwambili. N’naphunzila kuti Mulungu si amene amacititsa mavuto padzikoli ndipo iye sasangalala anthu akamacita zoipa. (Genesis 6:6; Salimo 78:40, 41) Sin’nali kafuna kucitanso zinthu zokhumudwitsa Yehova koma n’nali kafunitsitsa kumusangalatsa. (Miyambo 27:11) N’nasiya kumwa mowa mwaucidakwa, kukoka fodya komanso kucita zaciwelewele. M’March 1994, n’nabatizika n’kukhala wa Mboni za Yehova.
PHINDU LIMENE NAPEZA:
Panopa ndine wosangalala komanso wokhutila na zimene nikucita. Sinimwanso mowa pofuna kuti niiwale mavuto cifukwa n’naphunzila kupemphela kwa Yehova kuti azinithandiza nikakhala na nkhawa.—Salimo 55:22.
Zaka 10 zapitazo n’nakwatila mkazi wokongola yemwenso ni wa Mboni, dzina lake Karen. Ine na mkazi wangayu timasangalala kulela mwana wanga wopeza, dzina lake Nella. Tonse timatha nthawi yathu yambili tikulalikila komanso kuthandiza anthu kuti adziŵe Mulungu. N’kuona kuti panopa nd’apeza colinga ca moyo wanga.
a Lofalitsidwa na Mboni za Yehova.