Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhawa Zokhudza Banja

Nkhawa Zokhudza Banja

“Atate atangomwalila, mwamuna wanga anandiuza kuti wapeza mkazi wina. Posapita nthawi, iye anatenga zovala zake zonse n’kupita osandilaila ndipo anandisiya ndi ana aŵili.” Anatelo Janet. Janet anapeza nchito, koma ndalama zimene anali kulandila sizinali zokwanila kusamala banja lake. Iye anakumana ndi mavuto ambili kuonjezela pa vuto la ndalama. Janet akukumbukila kuti: “Ndinali ndi nkhawa kwambili kaamba ka maudindo amene ndinali kufunika kucita. Ndinali kudziimba mlandu wolephela kupezela ana anga zinthu zambili monga mmene makolo ena amacitila. Ngakhale pano ndimavutikabe maganizo ndikaganizila mmene anthu amandionela limodzi ndi ana anga. Ndimadzifunsa kuti, kodi anthu amaona kuti ndinalephela kuteteza cikwati canga?”

Janet

Pemphelo limathandiza Janet kukhazikika maganizo ndi kulimbitsa ubwenzi wake ndi Mulungu. Janet anati: “Usiku m’pamene ndimakhala ndi nkhawa kwambili. Koma kupemphela ndi kuŵelenga Baibulo kumandithandiza kuti ndigone. Ndimakonda kuŵelenga lemba la Afilipi 4:6, 7. Lembali limati: ‘Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Mukatelo, mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.’ Ndimapemphela usiku uliwonse ndipo Yehova amanditonthoza.”

Pa Ulaliki wake wa pa Phili, Yesu anakamba mau olimbikitsa onena za pemphelo amene angatithandize kulimbana ndi nkhawa zosiyanasiyana. Iye anati: “Atate wanu amadziŵa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.” (Mateyu 6:8) Timafunika kumupempha. Pemphelo ndi njila yabwino kwambili ‘yoyandikila Mulungu.’ Nanga pamakhala zotsatilapo zotani tikatelo? ‘Iyenso amatiyandikila.’—Yakobo 4:8.

Tikauza Mulungu nkhawa zathu m’pemphelo timamvako bwino. Yehova ndi “Wakumva pemphelo,” ndipo amathandiza onse omufunafuna mwa cikhulupililo. (Salimo 65:2) N’cifukwa cake Yesu anauza ophunzila ake kuti, “azipemphela nthawi zonse, osaleka.” (Luka 18:1) Tiyenela kupitiliza kupempha Mulungu kuti azititsogolela ndi kutithandiza, tikatelo tidzakhala ndi cikhulupililo. Tisakaikile kuti iye adzatithandiza kapena kucitapo kanthu. Conco, tiyeni ‘tizipemphela mosalekeza.’ Kucita zimenezi kudzaonetsa kuti cikhulupililo cathu n’colimba.—1 Atesalonika 5:17.

ZIMENE KUKHALA NDI CIKHULUPILILO KUMATANTHAUZA

Kodi cikhulupililo n’ciani? Cikhulupililo cimaphatikizapo “kudziŵa” Mulungu monga munthu. (Yohane 17:3) Timacita zimenezo mwa kudziŵa maganizo a Mulungu kudzela m’Baibulo. Timadziŵa kuti iye amatiyang’anila ndipo amafuna kutithandiza. Koma, kukhala ndi cikhulupililo ceniceni sikutanthauza kudziŵa cabe zinthu zinazake zokhudza Mulungu. M’malo mwake, kumatanthauza kukhala paubwenzi wolimba ndi iye. Mwacitsanzo, munthu akakhala ndi mnzake, ubwenzi wao umakula pang’onopang’ono. Mofananamo, cikhulupililo cathu ‘cimaonjezeka’ tikamaphunzila za Mulungu komanso tikamacita “zinthu zomukondweletsa,” ndipo timalandila thandizo lake. (2 Akorinto 10:15; Yohane 8:29) Cikhulupililo cotelo, n’cimene cimathandiza Janet kulimbana ndi nkhawa.

Janet anati: “Cimene candithandiza kulimbitsa cikhulupililo canga, ndi kuona mmene Yehova wandithandizila. Nthawi zambili timakumana ndi zopanda cilungamo zimene zimavuta kuzipilila. Koma mwapemphelo, Yehova anandithandiza kulimbana ndi zinthu zimene pandekha sindikanatha kulimbana nazo. Ndikamamuyamikila m’pemphelo, ndimakumbukila zinthu zimene wandicitila. Iye amandithandiza nthawi zonse. Wandipatsanso anzanga enieni amene ndi amuna ndi akazi Acikristu. Iwo amandithandiza nthawi zonse ndipo ndi zitsanzo zabwino kwa ana anga.” *

“Tsopano ndazindikila cifukwa cake Yehova anakambila mau a pa Malaki 2:16 akuti: ‘Ndimadana ndi zakuti anthu azithetsa mabanja.’ Kwa munthu wosalakwayo, limakhala vuto lalikulu. Tsopano papita zaka kucoka pamene mwamuna wanga anandisiya, koma ndimasungulumwabe ndipo ndimadziona kuti ndine wacabecabe. Koma cimene cimandithandiza ndikayamba kuganiza zimenezo, ndi kuthandiza munthu winawake kugwila nchito iliyonse.” Janet amagwilitsila nchito mfundo ya m’Baibulo mwa kupewa kudzipatula kuti acepetseko nkhawa zake. *Miyambo 18:1.

Mulungu ndi “tate wa ana amasiye ndi woweluzila akazi amasiye milandu.”—Salimo 68:5

Janet anati: “Ndimatonthozedwa kwambili kudziŵa kuti Mulungu ndi ‘tate wa ana amasiye ndi woweluzila akazi amasiye milandu.’ Iye sadzandisiya monga mmene mwamuna wanga anacitila.” (Salimo 68:5) Janet amadziŵa kuti Mulungu satiyesa ndi “zinthu zoipa.” M’malo mwake, amapeleka nzelu “moolowa manja kwa onse” ndipo amatipatsa “mphamvu yoposa yacibadwa” kuti itithandize kulimbana ndi nkhawa zathu.—Yakobo 1:5, 13; 2 Akorinto 4:7.

Nanga bwanji ngati tili ndi nkhawa cifukwa cakuti moyo wathu uli pa ngozi?

^ par. 8 Onani 1 Akorinto 10:13; Aheberi 4:16.

^ par. 9 Kuti mudziŵe zambili zokhudza mmene mungalimbanilane ndi nkhawa, onani nkhani ya pacikuto ya mutu wakuti: “Kodi Mumatani Mukakumana ndi Mavuto?” mu Galamukani! ya July 2015 ikupezekanso pa webusaiti yathu pa www.pr418.com.