Onani zimene zilipo

Malangizo a Msonkhano wa Umoyo na Utumiki

Malangizo a Msonkhano wa Umoyo na Utumiki

Zam’katimu

Kuseŵenzetsa Mavidiyo na Zofalitsa 14

1. Malangizo ano adzathandiza onse amene anapatsidwa nkhani pa Msonkhano wa Umoyo na Utumiki Wathu. Amene ali na nkhani azibwelelamo m’malangizo opezeka mu Kabuku ka Misonkhano ya Umoyo na Utumiki komanso amene ali m’cikalata cino asanayambe kukonzekela nkhani zawo. Muzilimbikitsa ofalitsa onse kulembetsa kuti azikambako nkhani za m’sukulu. Anthu acidwi amene amasonkhana mokhazikika, ndipo amavomeleza ziphunzitso za m’Baibo, komanso amayendela mfundo za Cikhristu pa umoyo wawo, nawonso akhoza kulembetsa. Woyang’anila Msonkhano wa Umoyo na Utumiki ayenela kukambilana ziyenelezo za wofuna kulembetsa m’sukulu na aliyense amene sanakhalebe wofalitsa koma akufuna kulembetsa. Pambuyo pa makambilanowo, amudziŵitse munthuyo ngati wayenelezedwa kapena ayi. Pa makambilano amenewa pazikhalanso amene amaphunzila Baibo na munthuyo (kapena, ngati ni mwana, kholo lake limene ni Mboni). Ziyenelezo zimenezi n’zolingana na za munthu wofuna kukhala wofalitsa wosabatizika.—od mutu 8 ndime 8.

 MAWU OYAMBA

2. Mphindi 1. Mlungu uliwonse, pambuyo pa nyimbo na pemphelo loyamba, cheyamani ayenela kukopela cidwi ca omvetsela ku msonkhanowo. Cheyamani angochula mfundo zofunika koposa zimene zingapindulile mpingo.

  CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 3Nkhani: Mphindi 10. Mutu wa nkhaniyi na mfundo zake ziŵili kapena zitatu zapelekedwa mu Kabuku ka Misonkhano ya Umoyo na Utumiki. Gaŵilani nkhaniyi kwa mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenelezedwa. Ngati pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu na mlungu paikidwa buku latsopano la m’Baibo, tambitsani vidiyo yofotokoza bukulo. Mlankhuli angagwilizanitse mfundo za mu vidiyoyo na mutu wa nkhani yake. Komabe, afunika kufotokoza mfundo zokhudza nkhani yake zimene zaikidwa m’kabuku ka misonkhano. Malinga na nthawi, agwilizanitsenso zithunzi za m’nkhani yake, pofuna kumveketsa bwino mfundo za nkhaniyo. Angaphatikizepo mfundo zina zopezeka m’zofalitsa zathu malinga ngati zithandiza kumveketsa bwino mfundo za m’nkhaniyo.

 4Kufufuza Cuma Cauzimu: Mphindi 10. Iyi ni mbali ya mafunso na mayankho yopanda mawu oyamba kapena otsiliza. Ipatsidwe kwa mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenelezedwa. Mlankhuli afunse omvetsela mafunso onse aŵili. Angasankhe kuŵelenga mavesi amene aikidwapo kapena ayi. Mayankho onse azikhala a masekondi 30 cabe olo kucepelapo.

 5Kuŵelenga Baibo: Mphindi 4. Mbali ya mwana wa sukulu imeneyi izipatsidwa kwa mwana wa sukulu mwamuna. Mwana wa sukuluyo ayenela kungoŵelenga mbali imene anapatsidwa popanda kukamba mawu oyamba kapena otsiliza. Cidwi ca cheyamani cizikhala maka-maka pa kuthandiza ana a sukuluwo kuŵelenga molondola, moonetsa kumvetsa zimene akuŵelenga, mosadodoma, momveketsa bwino ganizo, kusintha-sintha bwino mawu, kupumula moyenelela, komanso kumveka mwacibadwa. Popeza kuti nkhani zina zoŵelenga Baibo zimakhala zazitali pamene zina zimakhala zazifupi, woyang’anila Msonkhano wa Umoyo na Utumiki aziganizila luso la mwana wa sukulu pamene agaŵila nkhanizi

 CITANI KHAMA PA ULALIKI

6. Mphindi 15. Colinga ca mbaliyi n’kutipatsa mwayi woyeseza zokacita mu ulaliki, komanso kunola maluso athu okambilana na anthu polalikila na pophunzitsa. Akulu nawonso angamapatsidweko nkhani za m’sukulu mwa apa na apo. Mwana wa sukulu aliyense aseŵenzele pa phunzilo locokela mu bulosha ya Kuphunzitsa kapena yakuti Kondani Anthu. Phunzilolo lalembedwa m’mabulaketi pa nkhani mu Kabuku ka Misonkhano ya Umoyo na Utumiki. Nthawi zina paziikidwa nkhani yokambilana. Zikakhala conco, mbaliyo izisamalidwa na mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenelela.—Kuti mudziŵe mocitila mbali zokambilana onani  ndime 15.

 7Kuyambitsa Makambilano: Nkhani ya m’sukulu imeneyi ingapatsidwe kwa mwana wa sukulu mwamuna kapena mkazi. Wothandiza wake azikhala mwamuna mnzake kapena mkazi mnzake, kapena wacibale. Angakambilane cokhala kapena coimilila.—Kuti mudziŵe zambili za mocitila mbali imeneyi, onani ndime 12 na 13.

 8Kubwelelako: Nkhani ya m’sukulu imeneyi ingapatsidwe kwa mwana wa sukulu wammuna kapena wamkazi. Wothandiza wake azikhala mwamuna mnzake kapena mkazi mnzake. (km 5/97 tsa. 2) Angakambilane cokhala kapena coimilila. Mwininkhani aonetse zofunika kukamba popitiliza makambilano amene anayamba paulendo wapita.—Kuti mudziŵe zambili za mocitila mbali imeneyi, onani ndime 12 na 13.

 9Kupanga Ophunzila: Nkhani ya m’sukulu imeneyi ingapatsidwe kwa mwana wa sukulu wammuna kapena wamkazi. Wothandiza wake azikhala mwamuna kapena mkazi mnzake. (km 5/97 tsa. 2) Angakambilane cokhala kapena coimilila. Mbali imeneyi izionetsa phunzilo la Baibo limene lili kale mkati. N’kosafunika kukamba mawu oyamba kapena othela, kusiyapo ngati ndiyo mfundo imene akumuyang’anilapo. N’kosafunikila kuŵelenga mapalagilafu onse, koma akhoza kutelo nthawi zina.

 10Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila: Ngati idzakambidwa monga nkhani, mbaliyi ipatsidwe kwa mwana wa sukulu wammuna. Koma ngati idzakhala citsanzo, ipatsidwe kwa mwana wa sukulu wammuna kapena wamkazi. Wothandiza wake azikhala mwamuna mnzake kapena mkazi mnzake, kapena wacibale wake. Poyankha funso limene lili pa mutu wa nkhani yake, mwana wa sukulu azipeleka yankho momveka bwino komanso mosamala pogwilitsa nchito malifalensi omwe aikidwapo. Mwana wa sukulu angasankhe kuchula lifalensi ya nkhani yake kapena ayi.

11Nkhani: Mbali ya mwana ya sukulu imeneyi izipatsidwa kwa wophunzila wammuna, ndipo izikambidwa monga nkhani ku mpingo. Ngati nkhaniyo yacokela pa Zakumapeto A m’bulosha yakuti Kondani Anthu, wophunzila aonetse mmene tingagwilitsile nchito mavesiwo mu ulaliki. Mwa citsanzo, angafotokoze nthawi imene tingagwilitse nchito vesilo, zimene litanthauza, komanso mmene tingaligwilitsile nchito pokambilana na munthu. Ngati nkhaniyo yacokela pa mfundo ya m’phunzilo lina m’bulosha yakuti Kondani Anthu, cidwi ca mwana wa sukulu cikhale pa kuonetsa mmene tingaseŵenzetsele mfundoyo mu ulaliki. Angafotokoze citsanzo copezeka pa mfundo 1 ya phunzilo limenelo, kapena kufotokoza mavesi ena owonjezela othandiza m’phunzilo limenelo.

12Zocita: Mfundo zimene zili mu ndime ino komanso yotsatila zifotokoza mmene tiyenela kucitila mbali yakuti ”Kuyambitsa Makambilano” komanso yakuti ”Kubwelelako”. Kupatulapo ngati paikidwa malangizo ena, colinga ca mwana wa sukulu ni kufotokoza mfundo zacidule za coonadi ca m’Baibo zothandiza kwa munthu amene akukamba naye. Ayenelanso kupanga maziko a ulendo wobwelelako. Mwana wa sukulu asankhe nkhani imene ingaŵafike pamtima anthu a m’delalo. Angasankhe kugaŵila cofalitsa kapena kutambitsa vidiyo. M’malo mongoloŵeza zoti akakambe, mwana wa sukulu ayenela kukulitsa luso lake lokambilana na anthu, monga kuonetsa cidwi anthu ena komanso kukamba mwacibadwa.

13Mtundu wa Ulaliki: Mwana wa sukulu aseŵenzetse mtundu wa ulaliki umene wapatsidwa mwa njila imene angasankhe malinga na mmene zinthu zilili. Mwa citsanzo:

  1.  (1) Kunyumba na Nyumba: Mtundu wa ulaliki umenewu uphatikizapo ulaliki wa khomo na khomo, kaya kucita kuyendela anthu, kuŵatumila foni, kapena kuŵalembela kalata. Umaphatikizaponso kubwelelanso kwa anthu amene tinakambilana nawo pocita ulaliki wa khomo na khomo.

  2.  (2) Ulaliki Wamwayi: Ulaliki umenewu umacitika potengela mwayi maceza amene muli nawo n’kuloŵetsapo ulaliki. Ungaphatikizepo kufotokoza mfundo ya coonadi kwa anzanu a kunchito, kusukulu, maneba anu, anthu omwe mwakwela nawo galimoto, kapena anthu okumana nawo pocita zinthu za tsiku na tsiku.

  3.  (3) Ulaliki Wapoyela: Ulaliki umenewu uphatikizapo ulaliki wa pa kasitandi, wa kumalo a malonda, wa m’misewu, m’mapaki, koimika magalimoto, kapena kulikonse kumene kungapezeke anthu ambili.

14Kuseŵenzetsa Mavidiyo na Zofalitsa: Malinga na mmene zinthu zilili, mwana wa sukulu angasankhe kutambitsa vidiyo kapena kugaŵila cofalitsa. Ngati nkhaniyo ili na vidiyo kapena mwana wa sukulu wasankha kutambitsa vidiyo, ayelekezele kutambitsa vidiyo imeneyo na kukambilana mfundo zake, koma asaitambitse.

   UMOYO WATHU WACIKHRISTU

  15. Pambuyo pa nyimbo, mphindi 15 zotsatila za cigawoci zizikhala na nkhani imodzi kapena ziŵili zothandiza omvetsela kugwilitsa nchito Mawu a Mulungu pa umoyo wawo. Nkhanizi zingapatsidwe kwa mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenelezedwa, kusiyapo ngati papelekedwa malangizo osiyana. Koma mbali ya zofunikila za mpingo izipatsidwa kwa akulu okha. Ngati nkhani ni yokambilana, mlankhuliyo angamafunsenso mafunso ena m’nkhaniyo kuwonjezela pa mafunso olembedwa. Mawu ake oyamba azikhala acidule kuti akhale na nthawi yokwanila yokambilana mfundo zonse komanso kupeleka mwayi kuti omvela apelekepo ndemanga. Ngati nkhaniyo ili na mbali yofunsa munthu wina mafunso, zingakhale bwino kuti wofunsidwayo azipeleka ndemanga zake ali ku pulatifomu m’malo mokhala mu gulu.

16Phunzilo la Baibo la Mpingo: Mphindi 30. Mbali ino izipatsidwa kwa mkulu woyenelezedwa. (Ngati akulu ni ocepa, atumiki othandiza oyenelezedwa angapatsidweko mbaliyi.) Bungwe la akulu liyenela kucita kusankha awo amene angayenelezedwe kutsogoza Phunzilo la Baibo la Mpingo. Oyenelezedwawo afunika kukhala okhoza kuphunzitsa mwaluso, odziwa kusunga nthawi, kugogomeza malemba ofunika, komanso odziwa kuthandiza omvetsela kuona mfundo zothandiza. Abale osankhidwo azibwelelamo m’malangizo ofalitsidwa a motsogozela mbali ya mafunso na mayankho. (w23.04 tsa. 24, bokosi) Pambuyo pakuti nkhani ya mlungu umenewo yamveketsedwa bwino, palibe cifukwa cotalikitsila phunzilolo. Ngati n’zotheka, ni bwino kumakhala na wotsogoza komanso woŵelenga mapalagilafu wosiyana mlungu uliwonse. Ngati cheyamani wa Msonkhano wa Umoyo na Utumiki wapempha kuti phunzilo licitidwe mofupikitsa, wotsogoza ayenela kuona mmene angacitile zimenezo. Mwina angasankhe kusaŵelenga mapalagilafu ena.

  MAWU OTHELA

17. Mphindi 3. Cheyamani wa Msonkhano wa Umoyo na Utumiki abweleze mfundo zina zothandiza zimene taphunzila. Achulekonso zina za mlungu wotsatila. Ngati nthawi ilola, angachulenso maina a omwe adzakhale m’sukulu mlungu wotsatila. Zilengezo zonse zofunikila, kapena makalata ofunika kuŵelenga ku mpingo, aŵelengedwe na cheyamani m’mawu ake othela, kusiyapo ngati pelekedwa malangizo ena. Zilengezo za nthawi zonse, monga makonzedwe a ulaliki, komanso ndandanda za kuyeletsa, siziyenela kulengezedwa pa pulatifomu, koma ziziikidwa pa notisibodi. Ngati cheyamani waona kuti nthawi yake ya mawu otsiliza idzacepa kuti aŵelenge makalata kapena zilengezo, apempheletu abale amene ali na mbali m’cigawo ca Umoyo Wathu Wacikhristu kuti afupikitseko nkhani zawo. (Onani  mapalagilafu 16 na  19.) Msonkhanowu udzatha na nyimbo komanso pemphelo.

  CIYAMIKILO NA UPHUNGU

18. Pambuyo pa nkhani iliyonse ya m’sukulu, Cheyamani wa Msonkhano wa Umoyo na Utumiki ali na nthawi pafupi-fupi mphindi imodzi yoyamikila komanso kupeleka uphungu wothandiza kwa ana a sukulu, wocokela m’bulosha ya Kuphunzitsa. Poitanila mwana wa sukulu kuti akakambe nkhani yake, cheyamani asachule mfundo imene akumuyang’anilapo. Koma pambuyo pa nkhaniyo, cheyamani afunika coyamba kuyamikila mwana wa sukuluyo. Kenako, achule mfundo imene anali kumuyang’anila. Achulenso cifukwa cake iye wacita bwino, kapena afotokoze mokoma mtima cifukwa cake afunikila kugwililapobe nchito pa mfundoyo komanso mmene angacitile zimenezo. heyamani angafotokozekonso mbali zina za nkhaniyo, zimene waona kuti zingakhale zothandiza kwa mwana wa sukuluyo kapena omvetsela. Uphungu wothandiza woonjezela wocokela m’bulosha yakuti Kondani Anthu, komanso wa m’bulosha ya Kuphunzitsa kapena m’buku la Pindulani, ungapelekedwe mseli pambuyo pa misonkhano, kapena tsiku lina. Uphunguwo ungakhale wokhudza phunzilo limene anali kumuyang’anilapo kapena phunzilo lina.—Kuti mumve zambili zokhudza udindo wa cheyamani wa Msonkhano wa Umoyo na Utumiki, komanso mlangizi wothandiza, onani  mapalagilafu 19,  24, na  25.

     KUSUNGA NTHAWI

19Palibe amene ayenela kudya nthawi, ngakhale cheyamani amene. Olo kuti Kabuku ka Msonkhano wa Umoyo na Utumiki kamaikilatu nthawi pa nkhani iliyonse, mukatsiliza kufotokoza mfundo zonse, palibe cifukwa cowonjezela mfundo zina kungofuna kutsilizitsa nthawi yanu. Munthu akadya nthawi, cheyamani wa Msonkhano wa Umoyo na Utumiki kapena mlangizi wothandiza am’patse uphungu mseli. (Onani  ndime 24 and  25) Msonkhano wonse, kuphatikizapo nyimbo na mapemphelo, uyenela kutenga ola limodzi na mphindi 45.

 KUCEZELA KWA WOYANG’ANILA DELA

20. Mpingo ukakhala na woyang’anila dela, mapulogilamu ayenela kucitikabe motsatila Kabuku ka Misonkhano ya Umoyo na Utumiki, kupatulapo Phunzilo la Baibo la Mpingo. M’malo mwake, woyang’anila dela adzakamba nkhani yake yautumiki ya mphindi 30. Koma coyamba, cheyamani wa Msonkhano wa Umoyo na Utumiki adzasankhulapo na kubweleza mfundo zina zimene taphunzila, kuchulako zina za mlungu wotsatila, kupeleka zilengezo zilizonse zofunikila, komanso kuŵelenga makalata ofunikila. Pambuyo pake, m’pamene adzaitanila woyang’anila dela. Nkhani yautumiki ikatha, woyang’anila dela amalize misonkhano na nyimbo imene angasankhe. Angasankhenso m’bale wina kutseka na pemphelo. Pa mlungu wapadela sikukhala kilasi B. Koma kagulu kangacite misonkhano yawo pamene wadela akucezela mpingo wawo. Komabe, kaguluko kayenela kubwelelanso m’gulu pamene wadela akamba nkhani ya utumiki.

 MLUNGU WA MSONKHANO WA DELA KAPENA WA CIGAWO

21. Mkati mwa mlungu wa msonkhano wa dela kapena wa cigawo, misonkhano yonse ya mpingo siicitika. Mpingo uyenela kukumbutsidwa kuti nkhani za mlungu umenewo tiyenela kuziŵelenga patekha, kapena kuzikambilana monga banja.

 MLUNGU WA CIKUMBUTSO

22. Ngati Cikumbutso cili pa tsiku la mkati mwa mlungu, ndiye kuti Msonkhano wa Umoyo na Utumiki sudzacitika.

 WOYANG’ANILA MSONKHANO WA UMOYO NA UTUMIKI

23. Bungwe la akulu ndilo limasankha mkulu amene adzakhala woyang’anila Msonkhano wa Umoyo na Utumiki. Ni udindo wake kuonetsetsa kuti msonkhanowu ukucitika mwandondomeko yake potsatila malangizo ali m’cikalata cino. Afunika azilumikizana nthawi zonse na mlangizi wothandiza. Woyang’anila Msonkhano wa Umoyo na Utumiki akangolandila Kabuku ka Misonkhano ya Umoyo na Utumiki, mwamsanga agaŵile nkhani zonse za miyezi iŵiliyo. Izi ziphatikizapo nkhani za ana a sukulu, nkhani zinazo, komanso amene adzakhala cheyamani (Onani ndime  ndime 3-16 na  24.) Pogaŵila nkhani za m’sukulu ayenela kuganizila zaka za mwana wa sukuluyo, luso lake, komanso ufulu wake wa kulankhula pa nkhani imene angapatsidwe. Aganizilenso mfundo zimenezi pogaŵila nkhani zinanso za msonkhanowu. Nkhani izigaŵilidwa kukali milungu itatu lisanafike tsiku lokamba nkhaniyo. Pogaŵila nkhani za m’sukulu, seŵenzetsani fomu yakuti Mbali Yanu pa Msonkhano wa Umoyo na Utumiki (S-89). Woyang’anila Msonkhano wa Umoyo na Utumiki atsimikizile kuti ndandanda ya msonkhano wonse yaikidwa pa notisibodi. Bungwe la akulu lingasankhe mkulu wina kapena mtumiki wothandiza kuti azimuthandiza. Komabe akulu okha ni amene ayenela kugaŵila mbali zimene sizipatsidwa kwa ana a sukulu.

    CHEYAMANI WA MSONKHANO WA UMOYO NA UTUMIKI

24. Mlungu uliwonse, mkulu mmodzi adzakhala cheyamani wa msonkhano wonse. (Ngati akulu ni ocepa, atumiki othandiza oyenelezedwa angapatsidweko ucheyamani.) Iye afunika kukonzekela bwino mawu otsegulila komanso otsekela msonkhano. Ni amenenso ayenela kuitanila nkhani zonse za msonkhanowu. Malinga na ciŵelengelo ca akulu, cheyamani nayenso akhoza kumakambako nkhani zina, maka-maka mbali zongoitanila mavidiyo popanda kukambilana. Azicita mwacidule poyamikila nkhani yacokapo, komanso poitanila ina. Bungwe la akulu liyenela kusankha mwacilungamo akulu amene angayenelele bwino kumakhala macheyamani. Akuluwo azipatsidwa ucheyamani mwa apa na apo. Malinga na mikhalidwe ya kwanuko, woyang’anila Msonkhano wa Umoyo na Utumiki angamakhale cheyamani moculukilapo kuposa akulu enawo. Ngati mkulu anayenelezedwa kutsogoza Phunzilo la Baibo la Mpingo, ni woyenelelanso kukhala cheyamani wa msonkhanowu. Kumbukilani kuti mkulu amene ni cheyamani, afunika kumayamikila komanso kupeleka uphungu wacikondi kwa okamba nkhani zam’sukulu. Azionetsetsanso kuti misonkhano ikumatha panthawi yake. (Onani  ndime 17 na  19.) Ngati cheyamani akufuna, ndipo ngati malo okwanila alipo papulatifomu, angamuikile maikolofoni ina yapadela imene aziimililapo poitanila nkhani, pamene m’bale wokamba nkhaniyo akubwela ku maikolofoni ya mkambi. Ndiponso, cheyamani angasankhe kukhala pa mpando pakathebulo kupulatifomu kuyambila pankhani ya kuwelenga Baibo, mpaka kumapeto kwa cigawo cakuti Citani Khama pa Ulaliki. Izi zimasungitsa nthawi

   MLANGIZI WOTHANDIZA

25. Ngati n’kotheka, sankhani mkulu wofikapo wokamba bwino nkhani kuti asamalile mbali imeneyi. Udindo wake ni kupeleka uphungu wamseli kukakhala kofunikila, kwa akulu na atumiki othandiza, pa mbali iliyonse imene angasamalile. Izi ziphatikizapo nkhani za pa Msonkhano wa Umoyo na Utumiki, nkhani za anthu onse, kutsogoza kapena kuwelenga Phunzilo la Nsanja ya Mlonda, kapena Phunzilo la Baibo la Mpingo. (Onani  ndime 19.) Ngati pa mpingo pali akulu angapo ofikapo, odziwa kukamba bwino nkhani na kuphunzitsa, caka ciliconse mungasankhe mkulu wina woyenelela kukhala mlangizi wothandiza. Si nthawi zonse pamene mlangizi wothandiza afunika kupeleka uphungu kwa mkulu kapena mtumiki wothandiza pamene wakamba nkhani.

 KALASI B

26. Malinga na ciŵelengelo ca amene ali m’sukulu, mpingo ungakhalenso na kalasi B. Kalasi B iliyonse izikhala na mlangizi wake, maka-maka mkulu. Kukakhala kofunikila, mtumiki wothandiza woyenelezedwa angapatsidwe udindo umenewu. Bungwe la akulu ndilo limasankha m’baleyu, na kuonanso ngati pangafunike kumasinthana-sinthana. Mlangiziyo afunika kutsatila malangizo a  m’ndime 18. Ngati mpingo uli na kalasi B, muzipempha ana a sukulu kupita ku kalasiyo ikatha mbali ya Kufufuza Cuma Cauzimu, imene ili pansi pa Cuma Copezeka m’Mawu a Mulungu. Azibwelelanso m’gulu pambuyo pa nkhani yothela ya mwana wa sukulu.

 MAVIDIYO

27. Mavidiyo osankhidwa azionetsedwa pamsonkhano wa mkati mwa mlungu. Mavidiyo a pa msonkhanowu azipezeka pa JW Library®, ndipo mungayacite daunilodi pazipangizo zosiyana-siyana.

© 2023 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

S-38-CIN 11/23