Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Baibulo Linaneneratu za Mmene Anthu Adzidzaganizira ndi Kuchitira Zinthu Masiku Ano?

Kodi Baibulo Linaneneratu za Mmene Anthu Adzidzaganizira ndi Kuchitira Zinthu Masiku Ano?

Yankho la M’Baibulo

 Inde, Baibulo linaneneratu kuti anthu adzasintha n’kuyamba kukhala ndi makhalidwe oipa m’nthawi yathuyi. Linasonyeza kuti zimenezi zidzachititsa kuti mfundo za makhalidwe abwino zomwe anthu amatsatira zidzalowe pansi kwambiri. a (2 Timoteyo 3:1-5) Koma Baibulo linaneneratunso kuti anthu ena sadzakhala ndi makhalidwe oipa. Koma mothandizidwa ndi Mulungu, iwo azidzayesetsa kupewa zinthu zoipa n’kumaganiza komanso kuchita zimene Mulungu amasangalala nazo.—Yesaya 2:2, 3.

Zimene zili munkhaniyi

 Kodi Baibulo linaneneratu zotani zokhudza maganizo ndi zochita za anthu a m’nthawi yathuyi?

 Baibulo linafotokoza za makhalidwe oipa osiyanasiyana amene anthu ambiri adzakhale nawo chifukwa cha khalidwe la kudzikonda. Baibulo linaneneratu kuti kuwonjezera pa kukhala “odzikonda,” anthu adzakhala “osadziletsa” komanso “okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.”—2 Timoteyo 3:2-4.

 Mogwirizana ndi ulosiwu, anthu ambiri masiku ano amangoganizira za iwo okha, zimene iwo akufuna, zimene amakonda komanso zimene akuona kuti zingawathandize kuti zinthu ziziwayendera bwino. Makhalidwewa ndi ofala kwambiri ndipo akuchulukirachulukira. Anthu ambiri ndi odzikonda kwambiri moti satha ngakhale pang’ono ‘kukonda zabwino.’ Iwo ndi “osayamika” moti sazindikira kufunika koyamikira zimene ali nazo kapena kuthokoza pa zimene anthu ena amawachitira.—2 Timoteyo 3:2, 3.

 Khalidwe la kudzikonda limachititsa anthu kukhala ndi makhalidwe enanso omwe ndi ofala masiku ano:

  •   Dyera. Anthu “okonda ndalama” achulukanso masiku ano ndipo amangoona kuti zinthu zingawayendere bwino ngati atamapeza ndalama kapena chuma chambiri.—2 Timoteyo 3:2.

  •   Kunyada. Anthu ambiri ndi “odzimva, odzikweza,” “odzitukumula ndiponso onyada.” (2 Timoteyo 3:2, 4) Anthu oterewa amadzitama komanso amakokomeza luso, makhalidwe kapenanso chuma chawo.

  •   Kunenera ena zoipa. Anthu “onyoza” komanso “onenera anzawo zoipa” achuluka kwambiri. (2 Timoteyo 3:2, 3) Iwo amanyoza anthu anzawo kapena Mulungu. Amanenanso zabodza zokhudza ena kapena Mulungu.

  •   Kuuma mtima. Anthu ambiri ndi “osakhulupirika,” “osafuna kugwirizana ndi anzawo,” “achiwembu” komanso “osamva za ena.” (2 Timoteyo 3:2-4) Iwo amakana kukambirana ndi ena, kugwirizana ndi anzawo akasemphana maganizo komanso kukwaniritsa zimene anapangana ndi anthu ena.

  •   Chiwawa. Masiku ano, anthu ambiri ndi “oopsa.” Sachedwa kukwiya ndipo nthawi zambiri zimenezi zimachititsa kuti azichita zachipolowe kapena zankhanza.—2 Timoteyo 3:3.

  •   Kusamvera malamulo. Yesu analosera kuti kudzakhala “kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo” m’nthawi yathuyi. (Mateyu 24:12) Iye analoseranso kuti “zipolowe” zizidzachitikachitika.—Luka 21:9.

  •   Kusakonda achibale. Anthu “osamvera makolo” komanso “osakonda achibale awo” nthawi zambiri sasamalira a m’banja lawo, amawachitira nkhanza komanso zachiwawa.— 2 Timoteyo 3:2, 3.

  •   Ochita zachipembedzo mwachiphamaso. Anthu ambiri masiku ano ‘amangooneka ngati odzipereka kwa Mulungu.’ (2 Timoteyo 3:5) M’malo mochita zimene Mulungu amafuna, amatsatira atsogoleri achipembedzo omwe amangowauza zimene akufuna kumva.—2 Timoteyo 4:3, 4.

 Kodi zochita za anthu odzikonda zimakhudza bwanji anthu ena?

 Khalidwe lodzikonda lachititsa anthu ambiri kukhala ndi matenda a nkhawa komanso kuvutika maganizo. (Mlaliki 7:7) Mwachitsanzo, anthu ena amene amakonda ndalama amachitira anthu ena chiwembu. Anthu amene sakonda achibale awo amatha kuchitira nkhanza anthu a m’banja lawo ndipo zimenezi zingachititse kuti anthu enawo azivutika maganizo kapenanso kufuna kudzipha.

 Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri ayamba kukhala ndi makhalidwe oipa?

 Baibulo limafotokoza zimene zimachititsa anthu kukhala ndi makhalidwe oipa:

  •   Anthu ambiri asiya kukonda Mulungu komanso anthu anzawo. (Mateyu 24:12) Ndipo zimenezi zachititsa kuti khalidwe lodzikonda lizifala kwambiri.

  •   Satana Mdyerekezi anachotsedwa kumwamba ndipo ali padziko lapansili. (Chivumbulutso 12:9, 12) Kuyambira nthawi imene anabwera padzikoli, wakhala akutsogolera anthu kuti akhale odzikonda.—1 Yohane 5:19.

 Kodi tizichita chiyani tikaona kuti anthu ali ndi makhalidwe oipa?

 Mawu a Mulungu amanena kuti: “Anthu amenewa uwapewe.” (2 Timoteyo 3:5) Izi sizikutanthauza kuti tiyenera kupeweratu anthu. Koma tiyenera kupewa kugwirizana kwambiri ndi anthu odzikonda komanso osakonda Mulungu.—Yakobo 4:4.

 Kodi Baibulo linaneneratu kuti anthu onse adzakhala oipa?

 Ayi. Baibulo linaneneratu kuti anthu ena adzakhala “akuusa moyo ndi kubuula chifukwa cha zonyansa zonse zimene zikuchitika.” (Ezekieli 9:4) Iwo adzakana kukhala odzikonda ndipo azidzatsatira mfundo za Mulungu. Zolankhula ndi zochita zawo zidzakhala zosiyana kwambiri ndi anthu ena. (Malaki 3:16, 18) Mwachitsanzo, adzayesetsa kukhala pa mtendere ndi anthu onse komanso adzakana kumenya nawo kunkhondo kapena kuchita zachiwawa.—Mika 4:3.

 Kodi anthu adzaipiraipirabe mpaka dziko lonse kudzaza ndi zoipa zokhazokha?

 Ayi. Dzikoli silidzadzaza ndi zoipa zokhazokha. M’malomwake, posachedwapa Mulungu adzachotsa anthu amene amakana kutsatira mfundo zake. (Salimo 37:38) Iye adzakhazikitsa “dziko lapansi latsopano,” kapena kuti dziko latsopano la anthu ofatsa omwe adzakhala mwamtendere mpaka kalekale. (2 Petulo 3:13; Salimo 37:11, 29) Zimenezi si maloto chabe ayi. Ngakhale panopa, Baibulo likuthandiza anthu kuti asinthe n’kuyamba kuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo zachilungamo za Mulungu.—Aefeso 4:23, 24.

a Ulosi wa m’Baibulo komanso mmene zinthu zili padzikoli zimasonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ ndipo nthawi imeneyi ndi “yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti “Kodi Chizindikiro cha ‘Masiku Otsiriza’ Kapena Kuti ‘Nthawi ya Mapeto’ N’chiyani?