Kodi Anthu Oipa Akamwalira, Amakawotchedwa Kumoto?
Yankho la m’Baibulo
Anthu ambiri amakhulupirira kuti anthu oipa akamwalira amakawotchedwa kumoto, monga mmene chithunzi cha zipembedzo zosiyanasiyanachi, chikusonyezera. Komabe Baibulo limaphunzitsa zosiyana ndi zimenezi. Taonani mfundo zotsatirazi:
Akufa sadziwa chilichonse choncho sangamve kupweteka. “Kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Manda.”—Mlaliki 9:10.
Nawonso anthu abwino amapita kumanda. Yakobo ndi Yobu, omwe anali anthu okhulupirika, ankayembekezera kuti akamwalira adzapita kumanda.—Genesis 37:35; Yobu 14:13.
Malipiro a uchimo ndi imfa, osati kukawotchedwa kumoto. “Munthu amene wafa wamasuka ku uchimo wake.”—Aroma 6:7.
Mulungu angaoneke wopanda chilungamo ngati angawotche anthu. (Deuteronomo 32:4) Adamu, yemwe anali munthu woyamba kulengedwa, atachimwa Mulungu anamuuza kuti: “Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Mawu amenewa akanakhala abodza zikanakhala kuti Adamu atamwalira anapita kumoto.
Mulungu saganiza n’komwe zowotcha anthu oipa. Zimene anthu ena amakhulupirira kuti Mulungu amawotcha anthu oipa kumoto n’zosiyana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa zoti “Mulungu ndiye chikondi.”—1 Yohane 4:8; Yeremiya 7:31.