ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?—Gawo 1: N’chifukwa Chiyani Ndimakhulupirira Kuti Kuli Mulungu?
Kodi zinthu zinachita kulengedwa kapena zinasintha kuchokera ku zinthu zina?
Kodi inuyo mumakhulupirira zoti Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse? Ngati mumakhulupirira zimenezi, simuli nokha. Pali anthu ambiri, achinyamata ndi achikulire omwe, amene amakhulupirira zimenezi. Koma anthu ena amanena kuti zinthu zamoyo komanso chilengedwechi zinakhalapo chifukwa zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina, osati zinachita kulengedwa ndi “Winawake Wamphamvu Kwambiri.”
Kodi mukudziwa? Magulu awiri onsewa a anthu nthawi zambiri amakonda kunena zimene amakhulupirira koma sadziwa chifukwa chimene chimawachititsa kukhulupirira zimene akukhulupirirazo.
Anthu ena amakhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa chifukwa n’zimene anaphunzitsidwa kutchalitchi.
Anthu ambiri amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina chifukwa n’zimene anaphunzitsidwa kusukulu.
Nkhani ino, komanso zina zotsatira, zikuthandizani kuti muzikhulupirira kwambiri zoti zinthu zinachita kulengedwa komanso kuti muzitha kufotokoza zimene mumakhulupirirazi. Koma choyamba, mukufunika kuti mudzifunse funso lofunika kwambiri ili:
N’chifukwa chiyani ndimakhulupirira kuti kuli Mulungu?
N’chifukwa chiyani funso limeneli lili lofunika kwambiri? N’chifukwa chakuti Baibulo limakulimbikitsani kuti muzigwiritsa ntchito maganizo anu, kapena kuti “luntha la kuganiza.” (Aroma 12:1) Zimenezi zikutanthauza kuti musamangokhulupirira kuti kuli Mulungu chifukwa:
chongotengeka (Ndikuona kuti payenera kukhala winawake wamphamvu kwambiri)
chongotsanzira ena (Ndimakhala m’dera limene anthu amakonda zopemphera)
chokakamizika (Makolo anga anandilera m’njira yoti ndizikhulupirira zoti kuli Mulungu. Ngati nditasankha kusakhulupirira, ndiye kuti angandikhaulitse)
Koma inuyo panokha mukuyenera kupeza zifukwa zomveka zimene zimakuchititsani kukhulupirira kuti kuli Mulungu.
Motero, kodi ndi zifukwa ziti zimene zimakuchititsani kukhulupirira kuti kuli Mulungu? Tsamba lakuti “Zoti Muchite” lomwe lili ndi nkhani yakuti “N’chifukwa Chiyani Ndimakhulupirira Zoti Kuli Mulungu?” likuthandizani kuti mukhale ndi zifukwa zomveka zokuthandizani kukhulupirira Mulungu. Tsamba limeneli lingakuthandizeninso chifukwa mungafufuze kuti mudziwe mmene achinyamata anzanu anayankhira funso limeneli.
“Ndikakhala m’kalasi n’kumamvetsera aphunzitsi athu akufotokoza mmene matupi athu amagwirira ntchito, sindimakayikira ngakhale pang’ono zoti kuli Mulungu. Chiwalo chilichonse m’thupi lathu chimagwira ntchito yake, ndipo ntchito zina n’zing’onozing’ono kwambiri. Nthawi zambiri ziwalozi zimagwira ntchito yake ife tisakudziwa n’komwe. Zoonadi, thupi la munthu n’logometsa.”—Teresa.
“Ndikaona nyumba zitalizitali kwambiri, sitima kapena galimoto, ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi anamanga zinthu zimenezi ndani?’ Kuti galimoto ipangidwe, pamafunika anthu anzeru. Izi zili choncho chifukwa galimoto ili ndi zinthu zambiri zing’onozing’ono zimene zimagwira ntchito pamodzi mogwirizana. Choncho ngati panafunika winawake kuti apange galimoto, n’zoonekeratu kuti palinso winawake amene anatilenga.”—Richard.
“Mukaganizira kuti panapita zaka mahandiredi ambiri kuti anthu anzeru kwambiri azindikire ndi kumvetsa gawo lochepa kwambiri la chilengedwechi, n’zosamveka kuganiza kuti chilengedwe chogometsachi chinangokhalako chokha.”—Karen.
“Ndikamaphunzira kwambiri sayansi m’pamenenso ndimapeza umboni wamphamvu wosonyeza kuti zamoyo sizinachite kusintha kuchokera ku zinthu zina. Mwachitsanzo, ndimaganizira mmene zinthu zinasanjidwira bwino m’chilengedwechi komanso mmene anthufe tilili. Mwachitsanzo, anthufe timafuna kudziwa kuti ndife ndani, tinachokera kuti komanso tikupita kuti. Anthu amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zopanda moyo amayesa kuyankha pofotokoza zinthu mogwirizanitsa ndi zimene nyama zimachita, koma alephera kufotokoza chifukwa chake anthufe tilili apadera kwambiri poyerekezera ndi nyama. Ineyo ndimaona kuti n’zosamveka kukhulupirira kuti zinthu zinangokhalako zokha osati zinachita kulengedwa ndi Mlengi.”—Anthony.
Kufotokoza zimene ndimakhulupirira
Kodi mungatani ngati mnzanu wakusukulu atakusekani kuti mumakhulupirira zinthu zimene simuziona? Nanga mungatani ngati atanena kuti zimene asayansi apeza zikutsimikizira kuti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, osati zinachita kulengedwa?
Choyamba, musamakayikire zimene mumakhulupirira. Musachite mantha kapena manyazi. (Aroma 1:16) Ndipotu musaiwale mfundo izi:
Si inu nokha; anthu ambiri amakhulupirira kuti kuli Mulungu. Ena mwa anthu amenewa ndi anzeru kwambiri komanso ogwira ntchito za pamwamba. Mwachitsanzo, pali asayansi ambiri amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu.
Anthu akamanena kuti sakhulupirira kuti kuli Mulungu, nthawi zina amakhala akutanthauza kuti samudziwa bwino Mulunguyo. M’malo mopereka umboni wotsimikizira zimene amakhulupirira, amayamba kufunsa mafunso monga akuti, “Ngati Mulungu alipodi, n’chifukwa chiyani amalola kuti tizivutika?” Apatu iwo amatembenuza nkhani.
Mwachibadwa, anthu amafuna kulambira. (Mateyu 5:3) Izi zikuphatikizapo mtima wofuna kulambira Mulungu. Choncho munthu wina akadzakuuzani kuti kulibe Mulungu, munthu ameneyo, osati inuyo, akufunika kufotokoza zifukwa zimene zimam’chititsa kuti azikhulupirira zoti kulibe Mulungu.—Aroma 1:18-20.
Anthu amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu sikuti ndi osaganiza bwino. Pali umboni wotsimikizirika wosonyeza kuti zamoyo zinachita kulengedwa. Koma palibe umboni wotsimikizira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zopanda moyo.
Nanga mungayankhe bwanji ngati munthu wina atakufunsani kuti n’chifukwa chiyani mumakhulupirira kuti kuli Mulungu? Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni.
Ngati munthu wina wanena kuti: “Anthu osaphunzira ndi amene amakhulupirira zoti kuli Mulungu.”
Mungayankhe kuti: “Kodi umakhulupiriradi maganizo opotokawo? Ine ndiye sindikhulupirira. Ndipotu zotsatira za kafukufuku wina amene anachitika pakati pa mapulofesa a sayansi oposa 1,600 ochokera m’mayunivesite osiyanasiyana otchuka, zinasonyeza kuti munthu m’modzi pa atatu aliwonse amakhulupirira kuti kuli Mulungu.” a Kodi mapulofesa amenewa ungawaike m’gulu la anthu osazindikira chifukwa choti amakhulupirira kuti kuli Mulungu?”
Ngati munthu wina wanena kuti: “Ngati Mulungu alipodi, n’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambirimbiri?”
Mungayankhe kuti: “Mwina zimene mukutanthauza n’zakuti simumvetsa mmene Mulungu amachitira zinthu. Kapena mogwirizana ndi funso lanu, simumvetsa kuti n’chifukwa chiyani zikuoneka kuti iye sakuchitapo chilichonse. Ndi choncho, eti? [Dikirani ayankhe.] Ine ndinapeza yankho logwira mtima pa nkhani yokhudza chifukwa chimene padzikoli pali mavuto ambirimbiri. Koma kuti munthu amvetse yankho limeneli amafunika kuphunzira ndi kumvetsa mfundo zingapo zimene Baibulo limaphunzitsa. Kodi inuyo mungakonde kuti muphunzire zambiri?”
M’gawo 2 la nkhaniyi, tidzakambirana zifukwa zosonyeza kuti zimene anthu amakhulupirira zakuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina sizifotokoza momveka nkhani yokhudza kumene anthufe tinachokera.
a Zachokera ku: Social Science Research Council, “Religion and Spirituality Among University Scientists,” by Elaine Howard Ecklund, February 5, 2007.