FUNSO 8
Kodi Mulungu ndi Amene Amachititsa Kuti Anthu Azivutika?
“Nʼzosatheka kuti Mulungu woona achite zoipa, kapena kuti Wamphamvuyonse achite zinthu zolakwika.”
“Munthu akakhala pa mayesero asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Chifukwa Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.”
‘Muzimutulira nkhawa zanu zonse, chifukwa amakufunirani zabwino.’
“Yehova sakuchedwa kukwaniritsa zimene analonjeza ngati mmene anthu ena amaonera kuti akuchedwa. Koma akukulezerani mtima chifukwa sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.”