Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Sukulu

Mukamapita kusukulu, mumayesedwa pa zinthu monga kukhala oganiza, odekha kapenanso osangalala ndiponso pa nkhani yokhala okhulupirika kwa Mulungu. Mungatani kuti mukwanitse kuphunzira bwinobwino popanda kuvutika ndi nkhawa?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwirizana Ndi Aphunzitsi Anga?

Ngati mphunzitsi wanu ndi wovuta, simufunika kusiya sukulu, m’malomwake pali mfundo zimene zingakuthandizeni kuti moyo musaumve kuwawa. Tayesani kuchita zotsatirazi.

Ndingatani Kuti Ndimalize Homuweki Yanga?

Ngati mukulephera kumaliza homuweki yanu, simukufunika kuchita kudzipanikiza. Koma mukungofunika kumachita zinthu mwadongosolo.

Kodi Ndingatani Kuti Ndizipindula ndi Sukulu Ngakhale Pamene Ndikuphunzirira Kunyumba?

Ana asukulu ambiri ayamba kuphunzirira kunyumba. Pali mfundo 5 zomwe zingakuthandizeni kuti muzipindula ndi maphunziro pamene mwasiya kaye kupita kusukulu.

Zimene Mungachite Ngati Simukusangalalanso ndi Sukulu

Ngati sukulu simakusangalatsani, dziwani kuti simuli nokha. Onani zomwe mungachite kuti muzisangalala ndi sukulu.

Ndingatani Ngati Ndimalephera ku Sukulu?

Musanaganize zosiya kulimbikira kusukulu, ganizirani mfundo 6 zomwe zingakuthandizeni kuti muzikhoza m’kalasi.

Kodi Ndisiye Sukulu?

Pali zambiri zimene munthu ayenera kuganizira poyankha funsoli.

Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa?

Anthu ambiri amene akuvutitsidwa amaona kuti palibe chimene angachite. Nkhaniyi ikufotokoza zimene mungachite kuti anthu asiye kukuvutitsani.

Ndingatani Ngati Anzanga Amandivutitsa?

Simungathe kuchititsa kuti anthu asamakuvutitseni, koma mungathe kusintha mmene mumawayankhira.

Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani?

Onerani vidiyoyi kuti mudziwe chifukwa chake anthu amavutitsa anzawo komanso zimene mungachite kuti asiye kukuvutitsani.

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuphunzira Chinenero China?

Kodi pamakhala mavuto otani? Nanga pamakhala mapindu otani?

Zimene Zingakuthandizeni Kuphunzira Chinenero China

Kuphunzira chinenero china kumafunika kuyeserera, nthawi ndi khama. Zoti muchitezi zikuthandizani kudziwa zoyenera kuchita pophunzira chinenero china.

Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?—Gawo 1: N’chifukwa Chiyani Ndimakhulupirira Kuti Kuli Mulungu?

Kodi mungakonde kuti muzifotokozera ena molimba mtima zimene mumakhulupirira zoti kuli Mulungu? Werengani nkhaniyi kuti mupeze mfundo zimene zingakuthandizeni kuyankha ngati munthu wina wakufunsani zimene mumakhulupirira.

Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?—Gawo 3: N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kukhulupirira Kuti Zinthu Zinachita Kulengedwa?

Kodi munthu amafunika kudana ndi sayansi n’cholinga choti azikhulupirira zoti zinthu zinachita kulengedwa?

Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?—Gawo 4: Kodi Ndingafotokozere Bwanji Munthu Kuti Zinthu Zinachita Kulengedwa?

Simukufunika kuchita kukhala wodziwa kwambiri sayansi kuti muthe kufotokozera munthu umboni wosonyeza kuti n’zomveka kukhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa. Gwiritsirani ntchito zitsanzo zosavuta kumva zopezeka m’Baibulo.