Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amandithandiza Kukonza Tsogolo Langa

Yehova Amandithandiza Kukonza Tsogolo Langa

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Pena ndimafunadi n’tadziwa za tsogolo langa

    Ndiponso zomwe zingadzachitike pa moyo wanga.

    Mulimonsemo mmene zingakhalire,

    Ndine wa Yehova ndidzipereke.

    (KOLASI)

    Pa zinthu zonse zomwe ndingakhale nazo,

    Chofunikatu kuposa zonsezo,

    N’kusangalatsa Yehova m’zomwe ndimasankha.

    Zimene wandipatsa; sindidzaiwala.

    Ndipo sindidzanong’oneza bondo.

    Andithandiza kukonza tsogolo labwino.

  2. 2. Pena zinthu zikhoza kuoneka ngati zabwino,

    Koma ndikudziwa zikhoza kundisocheretsa.

    Ndimakumbuka kuti n’nadzipereka

    Kuti n’khale ndi chikhulupiriro.

    (KOLASI)

    Pa zinthu zonse zomwe ndingakhale nazo,

    Chofunikatu kuposa zonsezo,

    N’kusangalatsa Yehova m’zomwe ndimasankha.

    Zimene wandipatsa; sindidzaiwala.

    Ndipo sindidzanong’oneza bondo.

    Andithandiza kukonza tsogolo labwino.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    Kukonza tsogolo labwino zedi

    Yehova ndi yemwe akundithandiza.

    Ndingasangalale nthawi ili yonse,

    Pamenetu Yehova ndam’sangalatsa.

    (KOLASI)

    Pa zinthu zonse zomwe ndingakhale nazo,

    Chofunikatu kuposa zonsezo,

    N’kusangalatsa Yehova m’zomwe ndimasankha.

    Zimene wandipatsa; sindidzaiwala.

    Ndipo sindidzanong’oneza bondo.

    Andithandiza kukonza tsogolo labwino.