Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndidzadzukanso

Ndidzadzukanso

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Kusiyana ndi gululi n’kopweteka.

    Yehova ndadziwa n’nalakwitsa.

    Ululu mumtima, chonde ndithandizeni.

    Ndikufunitsitsa kubwerera.

    (KOLASI)

    Zomwe munandiphunzitsa​—ndikukumbuka​—

    Mawu anu olimbikitsawa

    Kuti ngakhale ndipunthwe, ngakhale ndigwe,

    Ndingadzukenso.

  2. 2.Anzanga enienidi,

    Ndawazindikira,

    Omwe amakonda Yehova.

    Mawu anu andithandizanso kubwerera.

    M’njira ya kumoyo ndiyendedi.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Chilichonsetu chikundikumbutsa choonadichi:

    Mapeto afika.

    (KOLASI)

    Yehova, atate, ndimvereni chonde

    Ndikufunikiradi thandizo.

    Ndingakhumudwe kambirimbiridi,

    Ndingadzukenso.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Yehovatu amamvetsa; ndimafunika thandizo.

    Amaona zomwe ena sangazionedi.

    Amayang’ana zabwino.

    (KOLASI)

    Ndikupita kumisonkhano, n’kalandiridwanso,

    N’chikondi ngati poyamba.

    Ngakhale ndikhumudwe, ngakhale ndigwe,

    Ndidzadzukanso.

    Ndingadzukenso.