Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nchito Zanu Zodabwitsa Zimanilimbikitsa

Nchito Zanu Zodabwitsa Zimanilimbikitsa

Daunilodi:

  1. 1. Mbalame ziimba mosangalala.

    Nyenyezi nazo zingena powala dzuŵa.

    Dzuŵali liŵala mu mithengo

    Namphepo ikuwomba yomveka bwino.

    (MWANA WA KOLASI)

    Niimba nyimbo, Yehova M’lungu

    Zonse mwalenga n’zodabwitsa.

    “munthu nindani, kuti muzimuganizila?”

    (KOLASI)

    Mulungu wathu timuimbile

    Mulungu wathu, timuthamande

    Tim’tamande.

  2. 2. Zamoyo zonsezi munalenga

    Mudzuŵa na usiku zikuthamandeni.

    Za m’maphili na za m’kati mwanyanja,

    Zonse zili na moyo, zikuthamandeni.

    (MWANA WA KOLASI)

    Niimba nyimbo, Yehova M’lungu

    Zonse m’nalenga n’zodabwitsa

    “Munthu nindani, kuti muzimuganizila?”

    (KOLASI)

    Mulungu wathu timuimbile

    Mulungu wathu, timuthamande

    Tim’thamande

    (BILIJI)

    Zimene timaona ndi maso

    Zimatiphunzitsa zambili za

    M’lengi wa moyo.

    (MWANA WA KOLASI)

    Niimba nyimbo, Yehova M’lungu

    Zonse mwalenga n’zodabwitsa

    “Munthu nindani kuti muzimuganizila?”

    (KOLASI)

    Mulungu wathu, timuimbile

    Mulungu wathu, timuthamande

    Mulungu wathu, tamandedi

    Mulungu wathu, timutamande

    Mulungu wathu, timuimbile

    Tim’tamande.