Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Malo Amene Adzachititsa Kuti Mulemekezedwe

Malo Amene Adzachititsa Kuti Mulemekezedwe

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Yehova, wolenga kumwamba,

    M’mwamba simungakwanemo,

    Ngakhalenso pano padziko.

    Koma mwatipatsa mzimu.

    Anthu anu akongoletsa

    Malo olambirirawa.

    Timadzipereka n’kumatumikira

    Mosangalala.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Zonsetu Yehova

    Munatipatsa ndinu.

    Zomwe tikupereka

    Mwatipatsa ndinu.

    (KOLASI)

    Tikuthokozatu zonsezi,

    Poimba mokweza mawu.

    Ndi malo mwatipatsa

    Tidikira madalitso.

  2. 2. Yehova munadziwa ndithu

    Tinkafunika malowa,

    Adzathandiza anthu anu

    Kuyendabe m’njira zanu.

    Pali ntchito yoti tigwire.

    Malowa adzathandiza,

    Pogwiratu ntchito ya Yesu

    N’kuyendabe ndi gululi.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Tim’patse zabwino

    Nthawi ndi chuma chathu.

    Ndinu woyenera ku​—landira

    Zonsezi.

    (KOLASI)

    Tikuthokozatu zonsezi,

    Poimba mokweza mawu.

    Ndi malo mwatipatsa

    Tidikira madalitso.