Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anzanga Apamtima

Anzanga Apamtima

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Ndikuona aliyense

    Ali ndi wocheza naye.

    Ndikudziwa, ndiyenera

    Anzangawa ndizisankha.

    Ndizabwino kudziwatu

    Komwe ndingapeze anthu

    Ondikonda, abwinodi,

    Omandilimbikitsadi.

    (KOLASI)

    Ndatsimikiza,

    Inu Yehova.

    Mundithandize

    Kuti ndisankhe

    Anzanga apamtima.

  2. 2. Mumtimamu ndikudziwa,

    Ndikuchita zoyenera.

    Mawu anu n’kawerenga,

    Amandikhudzadi mtima.

    Ndaonatu; ndadziwanso

    Kopeza ‘nzanga abwino.

    Tili ngati pachibale;

    M‘lungu wandipatsa onse.

    (KOLASI)

    Ndatsimikiza,

    Inu Yehova.

    Mundithandize

    Kuti ndisankhe

    Anzanga apamtima.