Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kudalila Imwe

Kudalila Imwe

Daunilodi:

  1. 1. Monga mizu yamitengo

    Mawu anu M’lungu,

    Alidi mumtima wanga

    Anipatsa mtendele.

    Olo zinganivute,

    Mumanipatsa nzelu,

    Coonadi ca mawu anu cinikumbutsa kuti

    (MWANA WA KOLASI)

    Limba usayope

    Pilila um’dalile.

    (KOLASI)

    Mu mavuto mawu anu

    Amanipatsa mphamvu

    Tsiku iliyonse nimadalila imwe.

  2. 2. Zocitika zam’dzikoli

    Zinganifooketsedi

    Nimadziŵa kuti

    Imwe muli nane

    Pamene niŵelenga

    Mawu anu Yehova

    Anitsogolela

    Ndipo aniuza kuti

    (MWANA WA KOLASI)

    Limba usayope

    Pilila um’dalile.

    Ulimbe nthawi yamavuto

    Uone zinthu zam’tsogolo.

    (KOLASI)

    Mu mavuto mawu anu

    Amanipatsa mphamvu

    Tsiku iliyonse nimadalila imwe.

    Imwe.

    (MWANA WA KOLASI)

    Limba usayope

    Pilila um’dalile.

    Ulimbe nthawi yamavuto

    Uone zinthu zam’tsogolo.

    (KOLASI)

    Mu mavuto mawu anu

    Amanipatsa mphamvu

    Tsiku iliyonse nimadalila imwe.