Kukonda Abale
Pangani Dawunilodi:
1. Kulikonse komwetu tingapite,
Kuli anthu a Yehova, abale athu.
Tingamvedi
Kutitu
Amatikonda.
Chikondidi.
2. Abale akugwirizanadi
Ndi Yehova komanso mwana wake
Polimbitsa
Ubale wa
Padziko lonse.
Chikondidi.
(KOLASI)
Atate atisamala
Sangatisiye.
3. Okhala m’nkhalango ndi m’mapiri,
M’matawuni ngakhale m’zilumba zonse,
Nonsenu.
Ndinudi anthu a Yehova.
Okondedwa.
(KOLASI)
Atate atisamala—
Sangatiiwale.
(VESI LOKOMETSERA)
Ngakhale dziko n’loopsa—
Ndilochititsa manthadi.
N’zosangalatsadi kudziwa
Yehova ndi anthu ake!
4. Yesu anati tizikondana.
Abale onsetu akuyesetsadi
Kukondana—
Inunso mukuyesetsadi.
Kukondana.
Kukondana.