Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Cikondi ca Paubale

Cikondi ca Paubale

Daunilodi:

  1. 1. Konse mungapite mupeza banja

    Ndipo konse mudzapeza anthu a Yehova

    Mudzapeza cikondi ca paubale

    Tikondana oh.

  2. 2. Abale na alongo mu dziko

    Amatengela Yehova na Yesu

    Mu cikondi

    Iwo ni banja la cikondi

    Tikondana

    (KOLASI)

    Yehova amatisunga

    Akonda onse

  3. 3. M’kati mwatengo na mumaphili

    Mu matauni akulu na kumidzi

    Mudziŵe namwe ndimwe anthu a M’lungu

    Tikondana oh.

    (KOLASI)

    Yehova amatisunga

    Atikonda tonse.

    (BILIJI)

    Mudzikoli nimovuta

    Zoonadi nimoopsa

    N’zosangalatsadi kudziŵa

    Yehova na anthu ake

  4. 4. Yesu anaphunzitsa cikondi

    Kuti anthu azitengela cikondi

    ca Yehova, namwe muli pakati pawo

    Tikondana

    Tikondana oh.