Kukonda Abale

Kukonda Abale

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Kulikonse komwetu tingapite,

    Kuli anthu a Yehova, abale athu.

    Tingamvedi

    Kutitu

    Amatikonda.

    Chikondidi.

  2. 2. Abale akugwirizanadi

    Ndi Yehova komanso mwana wake

    Polimbitsa

    Ubale wa

    Padziko lonse.

    Chikondidi.

    (KOLASI)

    Atate atisamala

    Sangatisiye.

  3. 3. Okhala m’nkhalango ndi m’mapiri,

    M’matawuni ngakhale m’zilumba zonse,

    Nonsenu.

    Ndinudi anthu a Yehova.

    Okondedwa.

    (KOLASI)

    Atate atisamala—

    Sangatiiwale.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Ngakhale dziko n’loopsa—

    Ndilochititsa manthadi.

    N’zosangalatsadi kudziwa

    Yehova ndi anthu ake!

  4. 4. Yesu anati tizikondana.

    Abale onsetu akuyesetsadi

    Kukondana—

    Inunso mukuyesetsadi.

    Kukondana.

    Kukondana.