Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tiyendebe

Tiyendebe

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. M’dziko zinthu zikusintha;

    Kale lapitadi.

    Chonde ndithandizeni

    Kusintha mwachangu.

    Ena angatitsutse

    Ena sapezeka,

    Mofunitsitsa titsate,

    Njira zatsopano.

    (KOLASI)

    Tiyendebe.

    Tithandizane.

    Tipambane.

    Mpaka mapeto

    Osasiya

    Tidziwe zoyenera kusintha.

    Tiyende.

  2. 2. Patsiku lililonse

    Timakhala n’zolinga,

    Zimasokonezedwa

    N’zochita zina.

    Pakhala vuto,

    Lovuta kuthetsa.

    Tili ndi zonse zothandiza,

    Kuyendabe ndithu.

    (KOLASI)

    Tiyendebe.

    Tithandizane

    Tipambane.

    Mpaka mapeto

    Osasiya

    Tidziwe zoyenera kusintha.

    Tiyende.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Taona madalitso

    Poyenda ndi gululi.

    Tikasintha Atate

    Adzasangalaladi.

    Chiyembekezo;

    Chathu.

    N’chotsimikizika

    Mavutowa adzatha

    Ndidzasangalala

    N’kamasintha

    (KOLASI)

    Tithandizane

    Tipambane.

    Mpaka mapeto

    Osasiya

    Tidziwe zoyenera kusintha.

    Tiyende.

    Tiyendebe.

    Tithandizane,

    Tipambane.

    Mpaka mapeto

    Osasiya

    Tidziwe zoyenera kusintha.

    Tiyende.

    Tiyendebe.