Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tithamange, Tisatsalile

Tithamange, Tisatsalile

Daunilodi:

  1. 1. Zinthu padziko zisintha, siningatsalile

    Conde nithandizeni kuti n’satsalile

    Pamene titsutsiwa, zitseko n’zovala

    Malangizo akusinthabe otithandizila

    (KOLASI)

    Tithamange, tisafo’ke tingapambane

    Tifulumile kuti ise tisatsalile tifulumile

    Tithamange

  2. 2. Poyamba tsiku langa, nimafuna zabwino

    Koma zinthu zosokoneza zimabweladi

    Nzelu zikasila thandizo ilipo

    Cifukwa zotithandizila nizambili-mbili

    (KOLASI)

    Tithamange, tisafo’ke tingapambane

    Tifulumile kuti ise tisatsalile tifulumile

    Tithamange

    (BILIJI)

    Tidzapeza zabwino (mwamsanga)

    Ngati ticita khama (pamodzi)

    Kuyendela pamodzi na malangizo onse (thamanga)

    Tidzakhala okondwa.

    M’lungu adzatipatsa

    Umoyo wamuyaya

    Conco nthawi zonse

    (KOLASI)

    Tithamange, tisafo’ke tingapambane

    Tifulumile kuti ise tisatsalile tifulumile

    Tithamange

    Tithamange (tithamange)

    tisafo’ke tingapambane (tisafo’ke)

    Tifulumile kuti ise tisatsalile tifulumile (ooh......)

    Tithamange

    Tithamange